Chizunzo Chosatha—Kodi Nchifukwa Ninji Chili Chiphunzitso Chosautsa?
“Ndamva kuti munachotsa ntchito pasitala wanu. Chinalakwika nchiyani?”
“Mudziŵa, iye anaumirira kutiuza kuti tonsefe tidzapita ku helo.”
“Kodi pasitala watsopanoyo amanenanji?”
“Nayenso pasitala watsopano amati tidzapita ku helo.”
“Chotero pali kusiyana kotani?”
“Eya, kusiyanako kuli kwakuti pamene pasitala woyamba anali kulankhula, anali kumveka ngati anakondwera nazo; koma pamene mwamuna watsopano akulankhula, amamveka wachisoni.”
NKHANI imeneyi yolembedwa m’buku lazithunzithunzi, imasonyeza mwanjira yakeyake kuti aphunzitsi a Baibulo ambiri, kudzanso opita kutchalitchi, sakupeza bwino ndi chiphunzitso cha helo. Kwakukulukulu, imatsimikiziranso zimene katswiri wazaumulungu wa ku Canada Clark H. Pinnock ananena: “Ndikhulupirira kuti pankhani zonse za maphunziro azaumulungu zimene zavutitsa zikumbumtima za anthu kwa zaka mazana ambiri, zoŵerengeka chabe zingakhale zitachititsa mantha aakulu alionse kuposa malongosoledwe olandiridwa a helo monga chilango chosatha chopweteka thupi ndi moyo.”
Zovutitsa Ponena za Makhalidwe Abwino
Pamenepa, kodi nchifukwa ninji ambiri amavutika maganizo ndi zithunzithunzi za ng’anjo yamoto zimene zimasonyezedwa m’Chikristu Chadziko? (Onani bokosi.) Profesa Pinnock akuti: “Lingaliro lakuti cholengedwa chozindikira chiyenera kuzunzidwa kuthupi ndi m’maganizo ku nthaŵi zosatha nchosautsa kwambiri, ndipo lingaliro lakuti chilangocho chimaperekedwa kwa iwo mwa lamulo laumulungu chimandichititsa kukaikira za chikondi cha Mulungu.”
Inde, chiphunzitso cha chizunzo chosatha chimabutsa mavuto ponena za makhalidwe abwino. Mwachitsanzo, Akristu owona mtima amasinkhasinkha mafunso odzutsidwa ndi katswiri wazaumulungu Wachikatolika Hans Küng: “Kodi Mulungu wachikondi . . . ayenera kupenyerera kosatha chizunzo chosatha, chopanda chiyembekezo, chopanda chifundo, chopanda chikondi, chankhalwe cha kuthupi ndi m’maganizo cha zolengedwa zake?” Küng akupitiriza kuti: “Kodi iye ali wokongoletsa wokakala mtima chotero? . . . Kodi tingamuganizire motani munthu amene amakhutiritsa chilakolako chake cha kubwezera chilango popanda kukhululukira ndi kukhutira konse?”a Ndithudi, kodi ndimotani mmene Mulungu amene amatiuza m’Baibulo kuti tiyenera kukonda adani athu angafunire kuzunza adani ake kosatha? (1 Yohane 4:8-10) Mosadabwitsa, anthu ena amanena kuti mkhalidwe wa helo ngwosayenerana konse ndi mkhalidwe wa Mulungu, kuti chiphunzitsochi sichanzeru malinga ndi makhalidwe abwino.
Okhulupirira ena ambiri amayesayesa kutontholetsa zikumbumtima zawo mwakupeŵa mafunso ameneŵa. Komabe, kunyalanyaza mafunso ameneŵa sikumathetsa zovuta zimenezi. Chotero tiyeni tipende nkhani imeneyi. Kodi nzovutitsa zotani ponena za makhalidwe abwino zimene chiphunzitso chimenechi chimabutsa? Mu Criswell Theological Review, Profesa Pinnock akulemba kuti: “Makhalidwe abwino samalola chizunzo chosatha chifukwa chakuti chimachititsa Mulungu kukhala ngati chilombo chokonda kukhetsa mwazi chimene chili ndi malo onga ndende yamuyaya yachibalo ya Auschwitz kumene amasungira ochimwa omwe samawalola ndi kufa komwe.” Iye akufunsa kuti: “Kodi ndimotani mmene munthu aliyense wokoma mtima angakhalire chete posinkhasinkha lingaliro lotere [chiphunzitso chamwambo cha helo]? . . . Kodi zitheka bwanji kuti Akristu apereke chithunzi cha Mulungu wankhalwe ndi wongokonda kulipsira ameneyu?”
Posonyeza chiyambukiro choipa chimene mwina chiphunzitsochi chakhala nacho pamkhalidwe wa anthu, Pinnock akuti: “Ndimadabwa kuti kodi ndimtundu wotani wa nkhalwe umene wachitidwa ndi awo amene akhulupirira Mulungu yemwe amazunza adani ake?” Iye akumaliza kuti: “Kodi limeneli siliri lingaliro losautsa kwambiri limene lifunikira kupendedwa kachiŵiri?” Inde, ngati ali Mulungu amene amachita nkhalwe yotero, mposadabwitsa kuti opita ku tchalitchi osamala ayamba kupendanso moto wahelo. Ndipo kodi iwo amapeza chiyani? Vuto lina loyang’anizana ndi lingaliro lachizunzo chosatha.
Helo ndi Chiweruzo Cholungama
Ambiri amene amapenda mosamalitsa chiphunzitso cha mwambo cha helo amapeza kuti chimawoneka kukhala chikusonyeza Mulungu kukhala wochita chisalungamo, chotero chimavulaza chikumbumtima chawo cha chiweruzo cholungama. Mwanjira yotani?
Yankho limodzi mungalipeze mwakuyerekezera chiphunzitso cha chizunzo chosatha ndi muyezo wa chiweruzo cholungama woperekedwa ndi Mulungu uwu: “Diso kulipa diso, dzino kulipa dzino.” (Eksodo 21:24) Kungochitira kupereka chigomeko, gwiritsirani ntchito lamulo laumulungu limeneli lopatsidwa kwa Israyeli wakale, lamulo lakubwezera chilango cholingana ndi cholakwa, pa chiphunzitso cha moto wahelo. Kodi inu mwachiwonekere mudzapeza chiyani? Mudzapeza kuti ochimwa amene achititsa chizunzo chosatha ndiwo okha amene ayenereranso chizunzo chosatha—chizunzo chosatha kulipa chizunzo chosatha. Koma popeza kuti anthu (mulimonse mmene angaipire) angachititse chabe chizunzo chokhala ndi mapeto, kuwaweruzira kuchizunzo chosatha kumachititsa kusalingana kwa machimo awo ndi chilango chosatha cha moto wahelo.
Kunena mwachidule, chilango chikakhala chopambanitsa. Chikapitirira muyezo wa “diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino.” Powona kuti ziphunzitso za Yesu zinachepetsako lingaliro lakulipsira, mungathe kuvomereza kuti Akristu owona angakuwone kukhala kovuta kuwona chilungamo m’chizunzo chosatha.—Mateyu 5:38, 39; Aroma 12:17.
Kulungamitsa Chiphunzitsocho
Komabe, okhulupirira ambiri amapitirizabe kuyesa kulungamitsa chiphunzitsocho. Motani? Wolemba nkhani wina wa ku Briteni Clive S. Lewis akulankhulira otetezera chiphunzitsochi ochuluka m’buku lake la The Problem of Pain: “Palibe chiphunzitso chimene ndingakonde kwambiri kuchichotsa m’Chikristu kuposa chimenechi, ngati ndinali wokhoza kutero. Koma chimachilikizidwa kwambiri ndi Malemba ndipo, makamaka, ndi mawu a Ambuye Wathu mwiniyo.” Chotero, ochichilikiza amavomereza kuti chizunzo chosatha nchochititsa mantha, koma panthaŵi imodzimodziyo, amakhulupirirabe kuti chiphunzitsocho nchofunika chifukwa amaganiza kuti Baibulo limachiphunzitsa. Katswiri wazaumulungu Pinnock akuti: “Mwakuvomereza kusakondweretsa kwake, iwo amakhulupirira kuti adzasonyeza kukhulupirika kwawo kosagwedera ku Baibulo ndi ungwazi wakutiwakuti m’kukhulupirira kwawo chowonadi chowopsa chimenechi kokha chifukwa chakuti malemba amachiphunzitsa. Iwo amazichititsa kuti ziwoneke ngati kuti kusalakwa kwa Baibulo kuli pangozi. Koma kodi kulidi tero?”
Inunso mungakaikire ngati kukhulupirika ku Baibulo sikumakulolani kuchitira mwina kusiyapo kuvomereza chiphunzitso chimenechi. Kodi kwenikweni nchiyani chimene Baibulo limanena?
[Mawu a M’munsi]
a Eternal Life?—Life After Death as a Medical, Philosophical, and Theological Problem, tsamba 136.
[Bokosi patsamba 5]
MALONGOSOLEDWE ATATU OPEREKA LINGALIRO LOFANANA
Mpambo wa zikhulupiriro wa Westminster Confession of Faith, wolandiridwa ndi Aprotestanti ambiri, umati awo osapita kumwamba “adzaponyedwa m’zizunzo zosatha, ndipo adzalangidwa ndi chiwonongeko chosatha.” “M’Chikristu cha Roma Katolika,” ikufotokoza motero The Encyclopedia of Religion, “helo amawonedwa kukhala mkhalidwe wa chilango chosatha . . . wophatikizapo . . . kuzunzika m’moto ndi zizunzo zina.” Buku lanazonse limeneli limawonjezera kuti “Chikristu cha Eastern Orthodox” chimavomereza “chiphunzitso chakuti helo ndigawo la moto wosazima ndi chilango loyembekezera otembereredwa.”—Volyumu 6, masamba 238-9.