Kulankhulana—Kumaphatikizapo zoposa kukambitsirana chabe
TAYEREKEZERANI khamu la alendo owona malo osangalatsa adzikolo. Ngakhale kuti gulu lonselo likuona malo amodzimodziwo, munthu aliyense akuona mosiyana. Chifukwa ninji? Chifukwa aliyense waima pamalo osiyana oonera. Palibe anthu aŵiri amene aima ndendende pamalo ofanana. Ndiponso, sialiyense amene akuyang’ana mbali imodzimodziyo ya malowo. Munthu aliyense wapeza mbali yosiyana imene ili yokondweretsa mwapadera.
Zimenezi nzofanananso muukwati. Ngakhale pamene ali oyenerana kwambiri, palibe okwatirana aŵiri amene amaona zinthu mofanana kwambiri. Mwamuna ndi mkazi amasiyana m’nkhani zonga ngati malingaliro, kakulidwe, ndi ziyambukiro za banja. Malingaliro osiyana amene amakhalapo angafikire kukhala magwero a mikangano yaikulu. Mtumwi Paulo ananena mosabisa mawu kuti: “Awo amene amakwatira adzakhala ndi mavuto ndi chisoni.”—1 Akorinto 7:28, The New English Bible.
Kulankhulana kumaphatikizapo kuyesetsa kugwirizanitsa anthu osiyana ameneŵa kuti akhale thupi limodzi. Zimenezi zimafunikira kukhala ndi nthaŵi ya kukambitsirana. (Onani bokosi patsamba 7.) Koma zambiri zimaloŵetsedwamo.
Kusonyeza Luntha
Mwambi wa Baibulo umati: “Mtima wa wanzeru uchenjeza m’kamwa mwake [kusonyeza luntha, NW], nuphunzitsanso milomo yake.” (Miyambo 16:23) Liwu Lachihebri panopa lotembenuzidwa “kusonyeza luntha” limatanthauza nzeru, kupenda zinthu mosamalitsa m’malingaliro. Chifukwa chake, malo enieni a kulankhulana kogwira mtima ndiwo mtima, osati pakamwa. Wolankhula wabwino ayenera kukhala woposa wokambakamba chabe; ayenera kukhala womvetsera wachisoni. (Yakobo 1:19) Ayenera kuzindikira malingaliro ndi zovuta zimene zimachititsa mnzakeyo kuchita motero.—Miyambo 20:5.
Motani? Nthaŵi zina zimenezi zingachitidwe mwa kupenda mikhalidwe yochititsa kusamvana. Kodi mnzanu wamuukwati ali wotsenderezeka kwambiri m’malingaliro kapena mwakuthupi? Kodi matenda ndiwo amene akuchititsa mkhalidwe wa mnzanuyo? “Nkosangalatsa chotani kunena mawu oyenera panthaŵi yabwino!” Baibulo limatero. (Miyambo 15:23, Today’s English Version) Chotero kulingalira mikhalidwe kudzakuthandizani kulabadira moyenera.—Miyambo 25:11.
Komabe, kaŵirikaŵiri chochititsa mkangano chimazikidwa pankhani zakale.
Kuzindikira Maleredwe
Zochitika za paubwana zimaumba kwambiri kaganizidwe kathu pamene tikukula. Popeza kuti anthu okwatirana amachokera kumabanja osiyana, malingaliro osiyana ngosapeŵeka.
Chochitika cholembedwa m’Baibulo chimapereka chitsanzo pazimenezi. Pamene likasa lachipangano linabwezedwa ku Yerusalemu, Davide poyera anasonyeza chikondwerero chake. Koma bwanji nanga za mkazi wake Mikala? Baibulo limati: “Mikala mwana wamkazi wa Sauli, analikupenya pazenera, naona mfumu Davide alikuvina ndi kuseŵera pamaso pa Yehova, nampeputsa mumtima mwake.”— 2 Samueli 6:14-16.
Mikala anasonyeza mkhalidwe wopanda chikhulupiriro wa atate wake wosalungamayo, Sauli. Operekera ndemanga pa Baibulo C. F. Keil ndi F. Delitzsch akulingalira kuti ndicho chifukwa chake Mikala akutchulidwa mu vesi 16 kukhala “mwana wamkazi wa Sauli” mmalo mwakutchulidwa kuti mkazi wa Davide. Mulimonse mmene zingakhalire, mkangano wobuka pakati pawo umasonyeza bwino kuti Davide ndi Mikala anali ndi malingaliro osiyana pachochitika chokondweretsa chimenechi.—2 Samueli 6:20-23.
Chitsanzo chimenechi chikusonyeza kuti ziyambukiro zamachenjera za maleredwe zingachititse mwamuna ndi mkazi kulingalira nkhani mosiyana kotheratu. Zimenezi nzowona ngakhale ngati onse aŵiri akutumikira Yehova mogwirizana. Mwachitsanzo, mkazi amene sanapatsidwe chichirikizo chokwanira cha malingaliro pamene anali mwana angasonyeze kuti afunikira kuvomerezedwa kokulirapo ndi kutsimikiziridwa mwachikondi. Zimenezi zingavutitse maganizo a mwamuna wake. “Ndingamuuze kuti ndimamukonda kwambiri,” mwamunayo angatero, “komabe samakhutiritsidwa!”
M’nkhani zoterezi, kulankhulana kukuphatikizapo kuti “yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:4) Kuti alankhulane, mwamuna ayenera kuona mkazi wake kuchokera pamaleredwe ake m’malo mwa maleredwe a mwamunayo. Ndipo ndithudi, mkazi nayenso ayenera kusonkhezeredwa kuchita chimodzimodzi kwa mwamuna wake.—1 Akorinto 10:24.
Ngati Wina Anakula Mozunzika
Kusamalira za winayo nkofunika kwambiri makamaka ngati mnzanu wamuukwati anagwiriridwa chigololo kapena anachitiridwa nkhanza mwakugonedwa akali mwana—momvetsa chisoni, ndilo vuto lomakulakula lerolino. Mwachitsanzo, panthaŵi ya unansi wa kugonana, mkazi sangathe kusiyanitsa chochitikacho ndi chakale, sangathe kusiyanitsa mwamuna wake ndi womgwirira chigololo, kapena unansi wa kugonana ndi nkhanza yakugonedwa. Zimenezi zingakhale zokhumudwitsa, makamaka ngati mwamunayo salingalira nkhani yovuta imeneyi monga momwe mkazi wake akuganizira.—1 Petro 3:8.
Pamene kuli kwakuti simungafafanize chikumbukiro cha chochitika chakale kapena kuthetsa ziyambukiro zake kotheratu, mukhoza kuchita zambiri kutonthoza mnzanu wamuukwati wotsenderezekayo. (Miyambo 20:5) Motani? “Amunanu muyenera kuyesetsa kumvetsetsa akazi amene mukhala nawo,” analemba motero Petro. (1 Petro 3:7, Phillips) Kumvetsetsa kakulidwe ka mnzanu wamuukwati ndimbali yofunika m’kulankhulana. Popanda kumvera chisoni, mawu anu adzakhala opanda pake.
Yesu ‘anachitira chifundo’ pamene anaona awo amene anali odwala, ngakhale kuti iyemwini sanadwalepo matenda awo. (Mateyu 14:14) Mofananamo, mwinamwake inuyo simunanyalanyazidwe mofananamo kapena kuchitiridwa nkhanza monga momwe zinachitikira kwa mkazi wanu, koma mmalo mwakunyalanyaza kuvutika kwake maganizo, dziŵani mmene anakulira, ndi kumpatsa chichirikizo. (Miyambo 18:13) Paulo analemba kuti: “Ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.”—Aroma 15:1.
Kukodwa Mumsampha wa Mkwiyo
Ukwati uli ngati chotengera cha mtengo wapatali. Pamene chiswedwa ndi chigololo, chimawonongeka kwambiri. (Miyambo 6:32) Zowona, ngati mwamuna kapena mkazi wopanda liŵongoyo asankha kukhululukira, zidutswazo zingamatiriridwe pamodzi mwa kuyanjananso. Komabe ming’alu yake imakhalapobe, ndipo atayambana, pangakhale chikhoterero cha kuyang’ana paming’aluyo ndi kugwiritsira ntchito zakalezo monga chida.
Kukwiya kwa mwamuna kapena mkazi chifukwa cha kusakhulupirika kwa mnzake ndiko mchitidwe wachibadwa. Koma ngati inu mwakhululukira mnzanuyo, samalani ndi kuipidwa kosatha kumene kungawononge zabwino zimene mwapeza mwakachitidwe ka kukhululukira. Kaya mkwiyowo ukutukutira chamkati kapena moonekera, mkwiyo wosatha umavulaza aŵiri nonsenu. Chifukwa ninji? Dokotala wina akunena kuti: “Ngati mukwiya ndi mnzanu wa muukwati, kumeneko kuli chifukwa chakuti mumasamalabe za iye. Chotero mwakuleka kapena kufunafuna kubwezera, inu simukuvulaza kokha mnzanuyo komanso mukudziwononga. Mumawonjezera kupasula unansi umene mumafuna kuti ukhalepo.”
Inde, simungathe kuthetsa zovuta za muukwati wanu popanda kuchepetsa mkwiyo wanu. Chifukwa chake, kambitsiranani za mmene mukumvera ndi mnzanuyo panthaŵi imene muli wosakwiya. Fotokozani chifukwa chake mukupwetekedwa mtima, zimene mufunikira kotero kuti mutsimikizire, ndi zimene mudzachita kuti musungebe unansiwo. Musagwiritsire ntchito zochitika zakale kukhala chida champhamvu mumkangano.
Kumwerekera m’Zoledzeretsa Kumawononga Mkhalidwe wa Kulankhulana
Ukwati umakhala ndi mavuto aakulu pamene wina wa muukwati agwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa kapena mankhwala oledzeretsa. Wa muukwati winayo amene sali womwerekera angakhale mumkhalidwe wofanana ndi wa Abigayeli, monga momwe kwasimbidwira m’Baibulo. Pamene mwamuna wake Nabala ‘anali woledzera kwambiri,’ Abigayeli anali kuyesayesa kusintha zochitika za khalidwe la mwamuna wake lopanda pakelo. (1 Samueli 25:18-31, 36) Maukwati amene ali m’vuto la munthu mmodzi womwerekera ndi zakumwa zoledzeretsa kapena mankhwala ndipo winayo akumayesayesa kusintha khalidwe la womwerekerayo kaŵirikaŵiri amafanana ndi banja la Nabala ndi Abigayeli.a
Momvekera bwino, pamamvedwa mpumulo waukulu pamene womwerekerayo amayamba kusintha. Koma kumeneku nkuyamba chabe. Yerekezerani za mkuntho waukulu wowononga wokantha patauni yaing’ono. Nyumba zikugwa, mitengo ikuzuka, zingwe za telefoni zikumaduka. Pamakhala chisangalalo chachikulu pamene mkunthowo utha. Koma tsopano pamafunikira ntchito yaikulu ya kukonzanso zinthu. Zimenezo zili zofanananso ndi pamene mnzanu wa muukwati ayamba kusintha. Maunansi owonongeka ayenera kukonzedwanso. Kudalirana ndi umphumphu ziyenera kukhazikitsidwanso. Njira zolankhulirana ziyenera kukonzedwanso. Kwa munthu womwerekerayo, kukonzanso zinthu mwapang’onopang’ono kumeneku kuli mbali ya “munthu watsopano” amene Baibulo limafuna kuti Akristu akulitse. Munthu watsopano ameneyu ayenera kuphatikizapo “mzimu wa mtima wanu.”—Aefeso 4:22-24.
Phunziro la Baibulo linakhozetsa Leonard ndi Elaine kuleka kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa, koma mzimu wa mtima unali usanafike pamkhalidwe wake wokwanira wa kugwira ntchito.b Posapita nthaŵi anabwerera kumikhalidwe ina ya kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa. “Kwazaka 20 tinayesayesa kugwiritsira ntchito malamulo a Baibulo ndi kukhala ndi ukwati wokhutiritsa, komano nthaŵi zonse tinkalephera,” akutero Elaine. “Kumwerekera kwathu m’mankhwala oledzeretsa kunazika mizu zolimba. Tinali osakhoza kuthetsa vutolo mwaphunziro kapena pemphero.”
Leonard ndi Elaine anafunafuna uphungu kuti adziŵe chimene chinachititsa kumwerekera kwawoko. Nkhani zotuluka panthaŵi yake zochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ponena za kuchitira nkhanza mwana, uchidakwa, ndi kuchitira ulemu akazi zakhaladi zothandiza.c (Mateyu 24:45-47) “Tathandizidwa kukonzanso mkhalidwe wowonongekawo ndi kubwezeretsanzo unansi wathu,” akutero Elaine.
Kuthetsa Mavuto
Rebeka anavutika m’moyo chifukwa cha akazi a mwana wake Esau. Powopera mwana wake wina wa mwamuna, Yakobo, kuti angatsatire njira ya Esau, Rebeka anauza mwamuna wake Isake za kukhumudwa kwake kuti: “Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Heti: akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Heti, onga ana aakazi a m’dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?”—Genesis 27:46.
Onani kuti pamene Rebeka ananena mwamphamvu za malingaliro ake, sanaimbe mlandu Isake mwachindunji. Sananene kuti, “Nchifukwa chanu!” kapena, “Mukanayenera kulamulira ana anuwa!” Mmalomwake, Rebeka anagwiritsira ntchito mneniyo “ndalema” kufotokoza mmene vutolo linamuyambukirira. Kanenedwe koteroko kanasonkhezera kumvera chisoni kwa Isake, osati chikhumbo chofuna kuchitiridwabe ulemu. Podziona kukhala wosaimbidwa mlandu mwachindunji, mchitidwe wa Isake pakudandaula kwa Rebeka mwachiwonekere unali wapanthaŵi yomweyo.—Genesis 28:1, 2.
Amuna ndi akazi okwatirana angatenge phunziro m’chitsanzo cha Rebeka. Pamene mkangano ubuka, limbanani ndi vutolo mmalo mwa kulimbana. Mofanana ndi Rebeka, fotokozani mmene vutolo lakukhumudwitsirani. Kunena kuti “Ndakhumudwa chifukwa cha. . . ” kapena, “Ndiyesa simunandimvetsetse chifukwa cha . . . ” nkwabwino kwambiri koposa kunena kuti “Mwandikhumudwitsa!” kapena, “Simundimvetsetsa konse!”
Kuposa Kukhalitsa
Ukwati wa anthu aŵiri oyamba, Adamu ndi Hava, unakhalako kwa zaka mazana ambiri, akumabala ana aamuna ndi aakazi. (Genesis 5:3-5) Komatu zimenezi sizimatanthauza kuti ukwati wawo unali woyenera kuutsanzira. Pachiyambi pomwe, mzimu wa kudzilamulira ndi kunyalanyaza malamulo olungama a Mlengi zinawononga chomangira chawo cha thupi limodzi.
Mofananamo, lerolino ukwati ungakhalitse, komabe nusoŵa mbali zofunika za kulankhulana. Malingaliro amphamvu ndi zikhoterero zosayenera zokhomerezeka kwambiri zingayenerere kuzulidwa. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 10:4, 5.) Umenewu ndi mchitidwe wa kuphunzira kosalekeza. Koma kuyesayesa kumeneko nkoyenera. Yehova Mulungu amakondwerera kwambiri kakonzedwe ka ukwati, popeza kuti ndiye Mlengi wake. (Malaki 2:14-16; Ahebri 13:4) Chifukwa chake, ngati tichita mbali yathu, tingakhale ndi chidaliro chakuti adzazindikira zoyesayesa zathu ndi kutipatsa nzeru ndi nyonga zofunika kuthetsera zovuta za kusalankhulana muukwati.—Yerekezerani ndi Salmo 25:4, 5; 119:34.
[Mawu a M’munsi]
a Thandizo la mabanja okhala ndi zidakwa lafotokozedwa m’kope la Galamukani! wa June 8, 1992, tsamba 21-26.
b Maina awo asinthidwa.
c Onani makope a Galamukani! wa October 8, 1991, June 8, 1992, ndi July 8, 1992.
[Bokosi patsamba 6]
“Zinyalala zili ndi nthaŵi yambiri!”
MWAMUNA ndi mkazi wake amene anali ndi mavuto m’banja anafunsidwa kuti ayerekezere nthaŵi imene anapatula kukataya zinyalala mlungu uliwonse. Yankho lawo linali lakuti anapatula pafupifupi mphindi 35 pamlungu, kapena mphindi 5 patsiku. Ndiyeno anafunsidwa za nthaŵi imene anathera akumalankhulana. Mwamunayo anadabwa kwambiri. “Zinyalala zili ndi nthaŵi yambiri!” iye anatero, akumawonjezera kuti: “Tikudzipusitsadi ngati tiganiza kuti kupatula mphindi zisanu patsiku nkokwanira kusamalira unansi wa muukwati. Ndipo ndithudi ndiyo nthaŵi yosanunkha kanthu yoti nkukulitsira unansi wa muukwati.”
[Bokosi patsamba 7]
Khazikitsani Malamulo a Kachitidwe ka Zinthu
◻ Kambitsiranani chinthu chimodzi panthaŵi imodzi (1 Akorinto 14:33, 40)
◻ Fotokozani malingaliro; musaimbe wina mlandu (Genesis 27:46)
◻ Musamenyane (Aefeso 5:28, 29)
◻ Musanenane (Miyambo 26:20)
◻ Khalani ndi chonulirapo cha kuyanjananso, osati kupambana wina (Genesis 13:8, 9)
[Chithunzi patsamba 4]
Pamene mkangano ubuka, limbanani ndi vutolo mmalo mwa kulimbana
[Chithunzi patsamba 8]
Fotokozani malingaliro anu; musaimbane mlandu