Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 10/15 tsamba 23-26
  • Kulalikira m’Dziko la Zinthu Zosiyanasiyana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulalikira m’Dziko la Zinthu Zosiyanasiyana
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Mbiri Yabwino Ikufalikira
  • Nyumba Zaufumu Zomangidwa Mofulumira m’Madera Akutali
  • Kupita ku “Nsonga Yapamwamba”
  • Kupita ku Alice Springs ndi Kuchoka m’Dera la Mkati
Nsanja ya Olonda—1993
w93 10/15 tsamba 23-26

Kulalikira m’Dziko la Zinthu Zosiyanasiyana

A KANGAROO, a koala, a wombat, ndi ma platypus, thanthwe la Ayers Rock ndi materezi a Great Barrier Reef​—maina ameneŵa amabwera m’maganizo pamene anthu aganiza za Australia. Koma ngakhale kuti zingakhale zodabwitsa, unyinji wa anthu a ku Australia mwina sanapiteko konse ku thanthwe la Ayers Rock kapena materezi a Great Barrier Reef kapena kuona zinyama zonga koala, wombat, kapena platypus kunja kwa paki ya zinyama. Nchifukwa chakuti 85 peresenti ya chiŵerengero cha anthu a m’dzikoli cha 17.3 miliyoni amakhala m’mizinda, akumakhala m’mizinda isanu yaikulu kugombe la nyanja.

Mukachoka kudera la kugombe ndi kupita chamkati kwa makilomita 200 kapena kuposapo, mumafika koyambira dera la mkati lotchuka la dzikoli. Maonekedwe a malowo amasintha kuchoka pankhalango za mvula zobiriŵira ndi minda yachonde kukhala malo atetete, otentha ndi ouma kumene kuli tizitsamba ndi udzu zomera apa ndi apo. Komabe, kuli zamoyo kumalo a mkati ameneŵa. Makola aakulu a nkhosa ndi ng’ombe amakhala ndi ukulu wa makilomita mazana ambiri mbali zonse zinayi. Chamkati kwambiri muli zipululu zotentha kwambiri, kumene nthaŵi zina anthu amafa ngati sadzitetezera bwino.

Mbiri Yabwino Ikufalikira

Ndim’mikhalidwe yotero mmene mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ikulalikidwa m’dzikoli la Australia. Zikwi zambiri chaka chilichonse zikuchitapo kanthu pa lonjezo la Yehova la dziko latsopano lolungama. Chaka chautumiki chathacho, chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu chinakhala chapamwamba kuposa 57,000, pafupifupi kuŵirikiza kaŵiri kuposa cha zaka khumi zapitazo. Pamene kuli kwakuti ofalitsa ambiri, mofanana ndi chiŵerengero chachikulu cha anthu, amapezeka kwambiri m’mizinda ya kugombe, mbiri yabwino ikufalikiranso m’madera a mkati.

Kuti mudziŵe mmene kuliri kulalikira m’dziko lalikululi la zinthu zosiyanasiyana, tiyeni titsagane ndi mmodzi wa oyang’anira zigawo athu asanu ndi mkazi wake pamene akuchezera mipingo ina m’madera akutali a mkati. Maulendo awo amafola boma la Western Australia, theka la boma la Queensland, ndi chigawo cha Northern Territory, mtunda woposa makilomita 4.7 miliyoni mbali zonse zinayi. Kukula kwa mtunda umenewu kuli pafupifupi ukulu wa Ulaya, kuchotsako dziko limene kale linali Soviet Union.

Ulendo wathu uyambira ku Perth, mzinda waukulu wa Western Australia. Mumzinda wamakono kotheratu umenewu wa anthu 1.2 miliyoni, tsopano muli mipingo 49 ya Mboni za Yehova. Kuwonjezera pa Yachingelezi, muli mipingo ya Chigiriki, Chitaliyana, Chipwitikizi, ndi Chispanya limodzinso ndi magulu aang’ono m’zinenero zina. Mulinso mpingo wa abale ndi alongo a mtundu wa Aborigine okhaokha, amene amasumika ntchito yawo yolalikira pakati pa anthu ameneŵa amene ali enidzikoli. Ambiri a anthu odzichepetsa ameneŵa tsopano akulabadira uthenga wa Ufumu. Koma kodi zinthu zili bwanji kumadera akutali ndi mizinda?

Kuchokera ku Perth tiyenda ulendo wa makilomita 1,800 kupita kumpoto ku Port Hedland, kumene kudzachitikira msonkhano wadera. Ambiri mwa opezekapo 289 ayenda ulendo wapakati pa makilomita 200 ndi 700 kuti afike kunoko. Amachokera kumadera akutali kumene mpingo wapafupi kwambiri ungakhale pamtunda wa makilomita 250 kuyenda pamisewu yopanda phula yamiyala yakuthwa imene kaŵirikaŵiri imaboola matayala a galimoto. Mipingo itatu m’derali yamanga Nyumba Zaufumu posachedwapa, mwakugwiritsira ntchito njira yomanga mofulumira.

Nyumba Zaufumu Zomangidwa Mofulumira m’Madera Akutali

Nkosiyana chotani nanga kumanga Nyumba Yaufumu m’madera ameneŵa ndi kumanga ina m’mizinda ndi matauni aakulu! Zinthu zambiri zomangira ziyenera kubweretsedwa m’lole kuchokera ku Perth, mtunda wa makilomita 1,600 kummwera. Mazana a abale ndi alongo amayenda mtunda umenewu ndi kuposapo pamapeto a mlungu olinganizidwa kudzamanga Nyumba Yaufumu m’malo otentha kuyambira pa 40 mpaka 45 digiri Celsius. Kubwera kwa anthu ochuluka motero m’zitaganya zazing’ono kumachitira umboni waukulu mwa iko kokha. Pamene Nyumba Yaufumu inamangidwa ku Tom Price, tauni yaing’ono ya migodi ya mtapo wa chitsulo, nyuzipepala ya kumaloko inalengeza patsamba loyamba kuti: “Tikulandirani amisiri ndi othandiza odzifunira oloŵetsedwa m’masiku atatu a ‘kumanga mofulumira’ Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova m’Tom Price.”

Kunaoneka kuti aliyense m’tauniyo anali wofunitsitsa kuthandiza. Mmalo mwa mtengo wamasiku onse wa $11,000 wobweretsera matani 50 a zinthu zomangira, mwini lole wina wowoloŵa manja anangopempha kuti abale apereke chopereka cha mafuta a galimoto. Kampani ya utoto yakumaloko inapereka malita 100 a utoto. Kampani ya akatapila inapereka akatapila ake, ndipo kampani ya migodi inapereka katapila yonyamulira zinthu kwaulere. Panali vuto la kupeza malo ogona alendo okwanira 300, koma kugwirizanika kwa anthu a m’tauniyo kunali kodabwitsa. Ena anaimba lamya ndi kupereka makama. Mwamuna wina anaimba lamya akunena kuti adzachokapo pamapeto a mlungu koma kuti akasiya chitseko chakumbuyo chosatseka. Anati: “Nyumba ndiyanu kwautali umene mudzakhala mukumanga.”

Chochitika choseketsa chinachitika pamene abale ena anapatsidwa keyala ya kumene akatenga ngolo ya dera la kumaloko. Iwo anadabwa kuona chikwangwani pachipata chakuti, “Sitifuna Anthu Achipembedzo.” Koma ngolo inali pomwepo. Chotero anauza mkazi wa panyumbapo kuti akutenga ngoloyo, imene inali yodzaza ndi zinyalala. Pamene anali kuiyeretsa, anazindikira mwadzidzidzi kuti sinali ngolo ya dera! Pamene mwini wa ngoloyo anafika panyumba, mkazi wake anamuuza kuti Mboni za Yehova zatenga ngolo yake. Abalewo posapita nthaŵi anabwerera ndi ngolo imene tsopano inali yopanda kanthu, akumafotokoza kuphonya kwawo. Kukambitsirana kwabwino kunatsatirapo, ndipo amene anali otsutsa ameneŵa anali ndi mafunso ambiri ponena za ifeyo ndi ntchito yathu. Tsopano anali ofunitsitsa kubwera kudzaona Nyumba Yaufumu yatsopanoyo.

Kulalikira mbiri yabwino m’dera lino kumafuna chipiriro. Choyamba, pali mitunda yaitali. Mlongo wina yemwe ndi mpainiya ndi mwamuna wake nthaŵi zonse amayenda ndi galimoto ulendo wa makilomita 350 kupita ndi kubwera pamisewu yopanda phula ndi yafumbi, kuchokera ku Port Hedland kupita ku Marble Bar, kuchita maulendo obwereza ndi kukachititsa maphunziro a Baibulo. Marble Bar ali amodzi a malo otentha kwambiri m’Australia, kaŵirikaŵiri kutentha kumafika pa 50 digiri Celsius kuyambira m’October mpaka m’March.

Kupita ku “Nsonga Yapamwamba”

Tauni ya Darwin, pamtunda wa makilomita 2,500 kumpoto kwenikweni, nkumene kudzachitikira msonkhano wadera wotsatira. Woyang’anira chigawo ndi mkazi wake akugwiritsira ntchito maola ambiri a kuyenda ndi galimoto kuchita phunziro laumwini. Choyamba akuŵerenga ndi kupenda lemba la tsiku. Ndiyeno amvetsera tepu ya kuŵerengedwa kwa Baibulo. Pamene asinthana kuyendetsa galimoto, asinthananso kuŵerenga nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!

Akuona chikwangwani cha pamsewu chowachenjeza za “masitima a pamsewu.” Amenewo ndimalole aakulu amphamvu kwambiri amene amakoka ngolo zitatu kapena zinayi ndipo utali wake wonse ndimamita 55. Choncho pafunikiradi malo otakata powadutsa. Amagwiritsiridwa ntchito kunyamulira ng’ombe ndi zinthu zina kupereka kumatauni akutali.

Nthaŵi zonse mphepo imakhala yotentha ndipo nthaka ya malowo njouma. Malo oumawo mwinamwake angaonedwe molakwa kukhala manda aakulu chifukwa nthaka yake ili ndi zulu zokhala pafupipafupi molinganizika bwino. Zulu zimenezi nzosiyana maonekedwe ake, malinga ndi dothi limene chiswe chinaziumbira, ndipo zingakhale zautali woyambira pa mita imodzi kapena asanu. Ndiyeno, pamene aulendo athu adutsa mtsinje wa Victoria, aona zikwangwani zambiri zopangidwa panyumba. Chimodzi chimati, “Mpowopsa: Kusambira Nkosaloledwa. M’mitsinjemu Muli Ng’ona Zodya Athu!” Mwanzeru, iwo apeza njira zina zosambira ndi kudziziziritsa!

Pomalizira pake, iwo afika kunsonga yakumpoto ya Australia, yodziŵika mofala kukhala “Nsonga Yapamwamba.” Ku Darwin, mzinda waukulu wa chigawo cha Northern Territory, kuli mipingo yaikulu iŵiri ya Mboni za Yehova. Anthu amafuko osiyanasiyana a m’Darwin angaonedwe mosavuta pamsonkhano wadera. Pali Charles wa zaka 30 zakubadwa, amene anachokera ku East Timor wokanthidwa ndi nkhondo ku Indonesia. Makolo ake a ku China anamphunzitsa kulambira makolo akufa. Ndipo anadziloŵetsanso kwambiri m’maseŵera omenyana monga ngati judo ndi karate. Kuleka zimenezi kunali kovuta kwambiri chifukwa chogwirizana kwambiri ndi mizimu. Komabe, pokumbukira lonjezo la Yesu lakuti “chowonadi chidzakumasulani,” anamasuka kunjira ya moyo imeneyi. (Yohane 8:32) “Lerolino,” iye akutero, “ndili ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Yehova, ndipo tsopano ndikutumikira monga mtumiki wotumikira. Chonulirapo changa nchakuloŵa Sukulu Yophunzitsa Utumiki.”

Wotsatira ndi Beverly, wa ku Papua New Guinea. “Poyamba ndinali ndi chidaliro chochepa cha kuchitira umboni kwa azungu,” akutero Beverly, “chifukwa Chingelezi ndinangochiphunzira ndipo mawu ena, limodzi ndi matchulidwe a nzika za Australia, anandivuta kumva. Koma pokumbukira kuti Baibulo limatiuza kudalira mwa Yehova ndi kumyesa kuona kuti ali wabwino, ndinayamba utumiki waupainiya wanthaŵi yonse mu January 1991. Amene ndinayamba kumuphunzitsa Baibulo ndimpainiya tsopano. Aŵiri a ana ake aakazi nawonso alandira chowonadi, ndipo mmodzi wa iwo ndimpainiya, limodzi ndi mwamuna wake.”

Tisanachoke ku Darwin, tiyeni titenge ulendo wofulumira wa makilomita 250 kupita kummaŵa ku Kakadu National Park, yotchuka chifukwa cha mitundu yake yosiyanasiyana ya mbalame. Kunoko tikumana ndi Debbie, mlaliki mmodzi yekha wa mbiri yabwino m’dera lonseli. Timfunsa mmene amakhozera kukhalira wolimba mwauzimu m’dera lakutali layekha limeneli. Iye akuyankha kuti: “Choyamba, mwapemphero. . . . Ndipo ndimapeza chitonthozo m’malemba onga Yesaya 41:10, limene limati: ‘Usawope, pakuti ine ndili pamodzi ndi iwe; usawopsedwe, pakuti ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchilikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.’”

Ku Jilkmingan, makilomita 450 kummwera kwa Darwin, tikumana ndi kagulu ka mtundu wa Aborigine. Kwa zaka zambiri chitaganya cha Aborigine chimenechi chinaonedwa kukhala chitaganya cha Mboni za Yehova chifukwa ambiri a iwo anali kufika pamisonkhano yachigawo ndi yadera nthaŵi zonse, ngakhale kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wobatizidwa. Chitaganyachi chinali chotchuka chifukwa cha ukhondo wake. Mwachimwemwe, ena tsopano atenga kaimidwe kolimba kumbali ya chowonadi ndipo abatizidwa. Iwo ali amodzi a Aborigine okhala kumidzi oyambirira kuchita zimenezi. Kumafunikira kulimbadi mtima ndi kudalira pamzimu woyera wa Yehova kuti anthu odzichepetsa ameneŵa amasuke kumiyambo yamakedzana ndi madzoma a kukhulupirira mizimu a anthu a mtundu wawo.

Kupita ku Alice Springs ndi Kuchoka m’Dera la Mkati

Tsopano ndinthaŵi ya kuchoka ku “Nsonga” ndi kuyenda makilomita 1,600 kupita kummwera ku Alice Springs, ku “Red Center,” pafupi ndi thanthwe lotchuka la Ayers Rock. Kunoko m’Nyumba Yaufumu yokhala ndi makina oziziritsa, muli malo okhala abwino a msonkhano wadera, ndipo opezekapo okwanira 130 kapena oposapo achokera m’mipingo iŵiri ya m’derali. Kunonso, tiona maonekedwe osangalatsa a Apolynesia, Azungu, ndi Aborigine akuyanjana monga gulu la Akristu.

Pomalizira pake tichoka ku Alice Springs ndi kuyamba chigawo chothera cha ulendo wathu ndi woyang’anira wathu wachigawo woyendayenda ndi mkazi wake. Ulendowu utipereka kumtunda wa makilomita 2,000 kudutsa dzikoli, kupita kumpoto koma chakummaŵa. Pamene tikutero, tikusiya dera la mkati, pakuti pomalizira pake tifika m’nkhalango yobiriŵira ya mvula m’dera lotentha la Queensland. Kunoko, kugombe la kumpoto kwa Queensland​—kumalo a materezi a Great Barrier Reef​—kuli mipingo yambiri yokhala ndi chiŵerengero chachikulu cha Mboni pa munthu mmodzi.

Komabe, ulendo wathu wopita kumsonkhano wadera womalizira sunathe. Tikukwera ndege ku Cairns​—tauni yotentha ya m’Queensland yotchuka ndi Barrier Reef​—tikuchoka kumtunda kwa Australia paulendo waufupi wa ndege kudzera pansonga yakumpoto ya Cape York Peninsula, kudutsa thamanda la Torres Strait, kupita ku Thursday Island. Kunoko kuli mpingo wa ofalitsa 23 chabe. Nkosangalatsa chotani nanga kuona opezekapo 63 pamsonkhano wathu wadera womalizira paulendowu!

Tikhulupirira mwasangalala kuona mmene ntchito yolalikira Ufumu ikuchitidwira m’dziko lino la zinthu zosiyanasiyana. Mwinamwake tsiku lina mungakhoze kutichezera m’dziko losangalatsa la Australia ndi kuonana maso ndi maso ndi abale ndi alongo amene mokhulupirika amachita utumiki wawo m’magawo achilendo.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 23]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Port Hedland

Canberra

Tom Price

Marble Bar

Newman

Darwin

Katherine

Alice Springs

Ayers Rock

Thursday Island

Cairns

Adelaide

Melbourne

Hobart

Sydney

Brisbane

Perth

[Chithunzi patsamba 24]

Perth, likulu la Western Australia

[Chithunzi patsamba 25]

Umboni wa m’khwalala umabala zipatso zabwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena