Nthaŵi ya Kututa!
KODI nchifukwa ninji mbiri ya “Chikristu” yakhala yopanda Chikristu? Anthu ambiri oganiza amafunsa funso limeneli, koma Yesu analiyankha m’fanizo pafupifupi zaka 2,000 zapitazo. Iye anasimba za “munthu, amene anafesa mbewu zabwino m’munda mwake.” Ndiyeno, “mdani wake anadza nafesa namsongole pakati pa tirigu.” Pamene mbewuzo zinamera, antchito anaona namsongole nafuna kumzula. Koma munthuyo anati: “Kazilekeni zonse ziŵiri, zikulire pamodzi kufikira pakututa.” Panthaŵi ya kututa, tirigu akalekanitsidwa ndi namsongole.—Mateyu 13:24-30.
Pofotokoza fanizolo, Yesu ananena kuti iye mwiniyo anali munthuyo amene anafesa “mbewu zabwino”—Akristu owona. Mdaniyo anali Satana, amene anafesa “namsongole”—kuloŵetsa Akristu ongoyerekezera mumpingo. Yesu analola Akristu onama ndi owona kukhalira limodzi—komatu kokha kufikira pakututa. Pamenepo zikalekanitsidwa.—Mateyu 24:36-44.
Chifukwa chake, sitimadabwa pamene tiphunzira kuti magulu “Achikristu” m’zaka mazana onse anyoza Mulungu mwakulandira ziphunzitso zachikunja, kulekerera chisembwere, kuchilikiza nkhondo za chilakiko, ndi kuzenga milandu mwakupereka zilango za nkhanza. Mwa zimenezi timaona mbewu yoipa yofesedwa ndi Satana. Komabe, pamene tiŵerenga za anthu amene anaponyedwa m’ndende kapena kufa mmalo mololera molakwa malamulo a Baibulo, timaona kuti mbewu yabwino sinazimiririke.
Yesu ananena kuti kututa ndiko “chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano.” Popeza kuti tikukhala ndi moyo m’chimaliziro cha dongosolo la zinthu la dziko lilipoli, imeneyi iyenera kukhala nthaŵi ya kututa! Chotero kulekanitsidwa kwa Akristu owona ndi onama kuyenera kukhala kutayamba kale. Lerolino, payenera kukhala anthu, osati munthu aliyense payekha momwazikana, amene amayenerera mafotokozedwe a Yesu a Akristu owona—amene ali nzika za Ufumu wa Mulungu ndi amene amalalikira mbiri yake yabwino, amene amachilikiza makhalidwe abwino ozikidwa m’Baibulo ndi kukana ziphunzitso zachikunja moyanja chowonadi cha Baibulo, amene amadziŵikitsa dzina la Mulungu ndipo sali mbali ya dziko.—Mateyu 6:33; 24:14; Yohane 3:20; 8:32; 17:6, 16.
Tikukutsimikizirani kuti, anthu otero alipo! Kodi mufuna kutumikira Mulungu movomerezeka? Pamenepo funafunani anthu ameneŵa, ndi kutumikira Mulungu pamodzi nawo.