Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 12/1 tsamba 10-13
  • Zochita za Yehova za Kupulumutsa Tsopano Lino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zochita za Yehova za Kupulumutsa Tsopano Lino
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikondi Chogwira Ntchito
  • Ubale wa Padziko Lonse
  • Magwero a Chitetezo Chowona
  • Zinthu Zimene Mkuntho wa Hurricane Andrew Sunakhoze Kuwononga
    Galamukani!—1993
  • Chimene Mkuntho Sunathe Kukokolola
    Galamukani!—2003
  • Utumiki Wothandiza Anthu pa Nthawi ya Mavuto
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • Anthu Amene Anavutika ndi Chimphepo ku Myanmar Anathandizidwa
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 12/1 tsamba 10-13

Zochita za Yehova za Kupulumutsa Tsopano Lino

BAIBULO limatiuza izi ponena za Yehova: “Masautso a wolungama mtima achuluka: koma Yehova amlanditsa mwa onsewa” ndipo, “[Yehova, NW] adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo.”​—Salmo 34:19; 2 Petro 2:9.

Kodi ndimotani mmene Yehova amathandizira anthu ake pamene ali pamavuto? Osati mwa kubweza mphamvu za chilengedwe mozizwitsa kapena mwa kachitidwe kena kosakhala kachibadwa, monga momwe anthu ambiri amaganizirira kuti ayenera kutero, koma mwa mphamvu ina imene anthu ochuluka samadziŵa​—chikondi. Inde, Yehova amakonda anthu ake, ndipo wawaphunzitsa kukondana mwamphamvu kwakuti ngwokhoza kuwachitira zinthu zimene zimaonekera kukhala monga zozizwitsadi.​—1 Yohane 4:10-12, 21.

Ena anganene kuti panthaŵi ya tsoka, zimene zimafunika ndizo chakudya, mankhwala, ndi ziwiya​—osati chikondi. Zowonadi, chakudya, mankhwala, ndi ziwiya nzofunika. Komabe, mtumwi Paulo akufotokoza motere: “Ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe. Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m’moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ayi.”​—1 Akorinto 13:2, 3.

Kaŵirikaŵiri timaŵerenga za katundu wa chithandizo wongokhala pamalo osungira akumawonongeka kapena kudyedwa ndi makoswe pamene kuli kwakuti anthu osoŵa akufa ndi nthenda ndi njala. Mwinamwakenso choipitsitsa nchakuti, katundu wa chithandizoyo angafikire m’manja mwa anthu aumbombo ndi osakhulupirika amene amapeza naye phindu. Chotero, katundu wachithandizoyo akhoza kupezedwa, koma nkovuta kuti alandiridwe ndi osoŵawo. Chikondi chenicheni ndi kudera nkhaŵa zikhoza kutheketsa zimenezo.

Chikondi Chogwira Ntchito

Mu September 1992, mkuntho wa Hurricane Iniki unakantha chilumba cha Kauai ku Hawaii, cha anthu 55,000. Mkunthowo unali kuyenda paliŵiro la makilomita 210 pa ola mpaka kufikira makilomita 260 pa ola, unapha anthu 2 ndi kuvulaza anthu 98, unawononga 75 peresenti ya nyumba, nusiya anthu 8,000 opanda nyumba, ndipo unawononga zinthu zoyerekezeredwa kukhala za ndalama zokwanira madola mamiliyoni chikwi chimodzi [a United States]. Pakati pa anthu amene amakhala pachilumba chaching’ono chimenechi panali Mboni za Yehova pafupifupi 800 zokhala m’mipingo isanu ndi umodzi. Kodi zinthu zinawayendera motani?

Mkuntho wa Iniki usanakanthe, akulu a mipingo, molangizidwa ndi woyang’anira woyendayenda, anali atafikira kale ziŵalo zonse za mipingo kuti atsimikizire kuti zinali zotetezereka, zokonzekera tsokalo. Kudera nkhaŵa kwachikondi kotero kunali kothandiza poleŵa ngozi kapena imfa pakati pa Mbonizo.​—Yerekezerani ndi Yesaya 32:1, 2.

Ngakhale kuti njira za kulankhulana ndi zoyendera zinasakazidwa kwambiri, nthumwi zitatu za ofesi ya nthambi ya Watch Tower Bible and Tract Society mu Honolulu zinali pakati pa anthu oyamba kufika m’malowo mkunthowo utachitika, pakuti anapatsidwa chilolezo chapadera ndi gulu lotetezera anthu kuyenda ulendo wa pandege kumka ku Kauai. Nthaŵi yomweyo, anaonana ndi Mboni za kumalowo ndipo, mmaŵa wotsatira, analinganiza za kuchita msonkhano kuti akonze njira zothandizira. Komiti yachithandizo inakhazikitsidwa kuti ione zofunika ndi kupeza zipangizo zofunika kupyolera kuofesi ya nthambi mu Honolulu. Pogwira ntchito mosalekeza, anatsogolera m’ntchito ya kupereka zinthu kwa awo amene anali osoŵa ndi kuyeretsa malo ndiponso kukonzanso nyumba zimene zinawonongeka.

Mboni za kuzilumba zina zinachitapo kanthu mofulumira kuthandiza abale awo ovutika. Mwamsanga pamene bwalo la ndege la Kauai linatsegulidwa, Mboni 70 zinayenda ulendo wa pandege kukathandiza kumeneko. Katundu wachithandizo wofikira mtengo wa $100,000, kuphatikizapo majenaleta, zitofu, nyali, ndi chakudya, zinatumizidwa m’dzikomo. Nyumba Yaufumu imodzi ya pachilumbacho inagwiritsiridwa ntchito monga malo ofikirapo katundu; komabe, panali mantha akuti mwina katunduyo angabedwe. Ndiyeno malole ena a Gulu Lankhondo anafika pa Nyumba Yaufumupo, ndipo oyendetsa ake anapempha kuti aimike malole awo pamenepo. Asilikali amene analonda malolewo anathetsanso nkhaŵa ya kuwopa kuberedwa katundu wachithandizoyo.

Abale anatengera majenaletawo kunyumba ndi nyumba, akumawagwiritsa ntchito panyumba iliyonse kwa maola aŵiri kapena atatu kuthandiza anthu kuti mafiriji awo agwire ntchito. Timagulu ta abale tinatumizidwa kunyumba zosiyanasiyana kukathandiza kuyeretsa malo ndi kukonza mowonongeka. Pamene anagwira ntchito panyumba ya mlongo wina amene mwamuna wake anamtsutsa mwamphamvu kalelo, mwamunayo anachita chidwi kwambiri kwakuti anangoima namalira. Mlendo wina wochokera kumtunda amene anaona kagulu ka Mboni kakugwira ntchito anachita chidwi kwambiri ndi khalidwe lawo ndi kulinganizika kwakuti anawafikira nawafunsa chimene chinawapangitsa kukhala osiyana kwambiri ndi anthu ena. Pamene mbale wina anafotokoza kuti kunali kukonda kwawo Mulungu ndi Akristu anzawo, munthuyo anati: “Kodi ndingadziŵe bwanji Mulungu?” (Mateyu 22:37-40) Ndiyeno anawonjezera kuti: “Anthunu ndinu olinganizika kwambiri ndikukakuyembekezerani kwathu pamene ndibwereranso ku Florida!”

Zonse pamodzi, Mboni za Yehova zinathandiza kuyeretsa ndi kukonzanso nyumba zokwanira 295 ku Kauai. Mwa nyumba zimenezi, 207 zinafunikira kukonzetsera kochepa, koma nyumba 54 zinawonongeka kwambiri, ndipo nyumba 19 zinawonongedweratu. Ntchito yawo inaphatikizaponso kufikira Mboni iliyonse pachilumbapo kuti atsimikizire kuti aliyense wasamaliridwa. Pamene katundu wachithandizo anaperekedwa kwa mlongo wina, mnansi wake Wachibuddha anaona kuti sanalandire ngakhale masamba a tiyi ndi kagulu kake. Mzimayi wina, amene nyumba yake inayeretsedwa ndi kagulu ka Mboni, anati: “Mwakhala mukufika pakhomo panga kwanthaŵi yaitali, ndipo ndakuonani kukhala anansi abwino, komano chikondi chaunansi mwandichitirachi chikundisonyeza zimene gulu lanu lilidi. Ndikuthokoza kugwira ntchito kwanu zolimba.”

Kuwonjezera pachisamaliro cha zosoŵa zakuthupi cha Akristu anzawo onse, awo amene anali ndi udindo wa kupereka chithandizo anadera nkhaŵanso za ubwino wawo wauzimu. Pasanapite masiku aŵiri mkunthowo utakantha, mipingo ingapo inali itayamba kale kuchita misonkhano yawo. Mwamsanga, timagulu ta maphunziro a buku ampingo tinayamba kuchititsidwa. Akulu khumi ochokera kuzilumba zina anadza ku Kauai kudzathandiza akulu amomwemo kotero kuti maulendo aubusa apangidwe pa Mboni iliyonse ya pachilumbapo. Sande lotsatira, mipingo yonse isanu ndi umodziyo inali ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda, ndi nkhani ya mphindi 30 yonena za njira za chithandizo yokambidwa ndi chiŵalo cha Komiti ya Chithandizo, ndi nkhani yotsiriza yamphindi 30 yokambidwa ndi chiŵalo cha Komiti ya Nthambi chimene chinachokera ku Honolulu kaamba ka chifuno chimenechi. Wopenyerera wina akusimba kuti: “Anthu onse anatonthozedwa ndi chitsogozo chimene chinaperekedwa ndipo anakhala okonzekera kusamalira okha mavuto amene anatsala. Omvetsera ambiri analira pamene programuyo inali kumalizidwa, ndipo anasonkhezereka kuombera m’manja.”

Ubale wa Padziko Lonse

Chikondi chotero ndi chisamaliro ndizo chizindikiro cha anthu a Yehova padziko lonse. Pamene Chimphepo cha Val chinaomba mu Western Samoa pafupifupi chaka chimodzi kalelo, chinawononga kwambiri, koma Mboni za Yehova kumbali zina za dziko zinadza kumeneko msanga kudzathandiza abale awo. Pambuyo pake, pamene boma linapereka chithandizo cha ndalama ku zipembedzo zonse​—kuphatikizapo kwa Mboni za Yehova​—kuti akonzetsere malo awo, Mbonizo zinabweza ndalamazo limodzi ndi kalata yofotokoza kuti zinali zitakonzetsa kale malo awo, ndipo ndalamazo zingagwiritsiridwe ntchito kukonzetsera nyumba zina za boma. Mchitidwe wawo umenewo unalembedwa mu nyuzipepala yakomweko. Powona zimenezi, mkulu wina wa boma anauza Mboni ina kuti anachita manyazi ndi tchalitchi chake chifukwa chakuti chinalandira ndalama za kuboma ngakhale kuti nyumba zawo zimene zinali zitawonongeka mkati mwa chimphepocho zinakonzedwa ndi ndalama zolipiriridwa ndi inshuwalansi.

Mofananamo, mu September 1992, pamene mtsinje wa Ouvèze wokhala kummwera koma chakummaŵa kwa France unasefukira ndi kuwononga Vaison-la-Romaine ndi midzi 15 ya m’malowo, Mboni zinachitapo kanthu mofulumira. Usiku umodzi wokha, madzi osefukirawo anapha anthu 40, ndi kugumula nyumba 400, ndiponso anawononga nyumba zina mazana ambiri, ndipo anasiya mabanja zikwi zambiri ali opanda madzi kapena magetsi. Mmamaŵa wotsatira, Mboni zochokera kumipingo ina ya momwemo zinali zoyambirira kufika kudzathandiza mikholeyo. Awo amene anali ofunikira malo okhala anatengedwera kunyumba za mabanja a Mboni m’chigawocho. Mazana ambiri a Mboni anadza kuchokera kumadera onse kudzathandiza. Komiti ya chithandizo inakhazikitsidwa mumzinda wa pafupi wa Orange kuti isamalire ntchito za timagulu tinayi ta odzipereka, amene anachotsa thope ndi kuyeretsa nyumba, kuchapa zovala zathope, ndipo anaphika ndi kupereka chakudya ndi madzi kumadera onse oyambukiridwa. Iwo anadzipereka kukayeretsa ngakhale sukulu yakomweko ndi nyumba zingapo za konsolo. Kuyesayesa kwawo kosatopa kunayamikiridwa ndi abale awo ndi anthu wamba omwe m’malowo.

M’malo ena ambiri, Mboni za Yehova zavutika ndi masoka, monga ngati kusefukira kwa madzi, mikuntho, ndi zivomezi, monga momwe zachitikira kwa anthu ena alionse. Podziŵa kuti zimenezi ndizo zotulukapo za zochitika zosaonedweratu kapena zosapeŵeka, izo sizimaimba mlandu Mulungu kapena munthu wina aliyense. (Mlaliki 9:11) Mmalo mwake, izo zimakhulupirira kuti okhulupirira anzawo okhala ndi chikondi chodzimana adzazipulumutsa mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta imene ingazichitikire. Machitidwe achikondi oterowo amakhalapo chifukwa cha chikhulupiriro chimene onsewo ali nacho. Wophunzira Yakobo amafotokoza kuti: “Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, nichikamsoŵa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nawo, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosoŵa za pathupi; kupindula kwake nchiyani? Momwemonso chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo.”​—Yakobo 2:15-17.

Magwero a Chitetezo Chowona

Mmalo mwa kuyembekezera zozizwitsa mumpangidwe wa kuloŵerera kwaumulungu kwinakwake, Mboni za Yehova zimazindikira kuti chitetezo chikapezedwa muubale wawo Wachikristu wa padziko lonse. Kwenikweni, zimene ubale umenewo ukhoza kuchita m’nthaŵi zamavuto zili zozizwitsa. Izo zimakumbukira mawu a Yesu opezeka pa Mateyu 17:20 akuti: “Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambewu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakulakani kosachitika.” Inde, zopinga zonga mapiri zimazimiririka pamene chikhulupiriro chowona cha Chikristu, limodzi ndi chikondi, zigwiritsiridwa ntchito.

Anthu a Yehova padziko lonse amawona dzanja lotetezera la Mulungu wawo m’nthaŵi zosakhazikika ndi zangozi zino. Iwo amamva monga momwe anamvera wamasalmo kuti: “Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.” (Salmo 4:8) Mwachidaliro, amaika chisamaliro pantchito imene ilipo: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Ndipo amayembekezera motsimikiza za kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova la dziko latsopano la mtendere ndi lolungama, mmene sadzaonanso masoka amtundu uliwonse, opangidwa ndi munthu kapena achilengedwe.​—Mika 4:4.

[Zithunzi patsamba 12]

Mboni zinachokera kumadera onse kudzathandiza mikhole ya kusefukira kwa madzi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena