Lipoti la Olengeza Ufumu
“Dzina la Yehova Ndilo Linga Lolimba”
TIKUKHALA ndi moyo m’nthaŵi zosakhazikika. Miyoyo yathu yoonekera kukhala yokhazikikayi ingasinthe kamodzi nkamodzi, ndipo mwadzidzidzi ena adzipeza ali m’mavuto aakulu mosazindikirika. Ngozi ingabwere kuchokera ku kusintha kwa zandale, kuukiridwa mwachiwawa, tsoka la chilengedwe, kapena matenda aakulu. Mulimonse mmene zingakhalire, kodi Mkristu ayenera kutembenukira kuti pamene moyo wake uli paupandu?
David, mmishonale amene amakhala pa imodzi ya nthambi za Watch Tower Society, anadziŵa yankho la funso limenelo pa chokumana nacho chowopsa. Akumagwira ntchito monga woyendetsa galimoto, iye ananyamuka mmaŵa wina kukatenga ogwira ntchito pa Beteli amene amakhala kunja (odzipereka amene sakhala panthambi). Kunali kudakali mdima. Ananyamula Rosalía ndipo anali kudutsa pa polisi pamene anamva kulira kwa mfuti koyamba.
Ndiyeno zinthu zinachitika mofulumira. Anamva phokoso la kuphulika kwakukulu ndipo anazindikira kuti mpweya unali kutuluka m’tayala limodzi. Mwadzidzidzi anaona msilikali ataima pakati pa msewu atalunjika mfuti yake pa iye. Zinthu zitatu zinachitika pafupifupi panthaŵi imodzi: Zipolopolo zambiri zinaboola mbali imodzi ya galimoto ya Jeep, zikumaswa mazenera; David ndi Rosalía anawerama; msilikali anaombera pa zenera lakutsogolo.
Pamene Jeep inali kulasidwa mobwerezabwereza ndi zipolopolo, David anaiimika bwino galimotolo monga momwe akanathera ali chiweramire. Aŵiri onsewo David ndi Rosalía analingalira kuti adzafa. Iwo anapemphera mokweza mawu kwa Yehova, akumampempha kuti awayang’anire. Pambuyo pake Rosalía ananena kuti m’mphindi zimenezo anadabwa mmene banja lake likachitira litamva za imfa yake!
Adakali ndi Moyo!
Pomalizira pake phokoso la kuwombera ndi kusweka kwa magalasi linaleka, ndipo David anayang’ana Rosalía. Pamene anaona dontho la mwazi kumsana kwake, anachita mantha kwambiri. Koma chidutswa cha galasi, osati chipolopolo, chinazikika kumsanako. Maondo ake anali kuchucha mwazi chifukwa cha kuchekeka ndi magalasi akugwa, komabe anali bwino ndithu.
Amuna ovala yunifomu ya asilikali omangirira timikwamba toyera m’mikono anafika pa Jeep ndi kulamula kuti atuluke atatukula manja. Mmodzi, amene anaonekera kukhala wamkulu, anatembenukira kwa msilikali wina nati: “Munauzidwa kuti musawombere anthu wamba.” Msilikaliyo anapereka zodzikhululukira, akumanena kuti anamva kulira kwa mfuti ndipo anaganiza kuti kunachokera ku Jeep imeneyo.
Pamene David ananena kuti iye ndi Rosalía anali Mboni za Yehova, kulabadira kunakhala kwachiyanjo. Iye analongosola zimene anali kuchita, koma asilikaliwo anafunabe kuwasunga. Mwachionekere, m’maola a m’mawa, kagulu ka asilikali kanafuna kulanda boma, ndipo asilikali ameneŵa anali kupita kukalanda malo a polisi pamene David ndi Rosalía anadutsa ali mu Jeep.
Rosalía anakwiya kwambiri koma modziletsa kwambiri anakhala chete pamene David anachonderera kuti amasulidwe. Pomalizira pake analoledwa kupita—popanda Jeep. Anayenda kupita kumsewu wapafupi kukakwera basi kupita kunthambi, kumene Rosalía anasamaliridwa ku chipatala.
Mphamvu ya Pemphero
David anaphunzira kanthu kena m’chokumana nacho chimenechi—osanyalanyaza konse mphamvu ya pemphero lamtima wonse, ndipo osaiwala konse kuti kudzizindikiritsa molimba mtima monga mmodzi wa Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri kumakhala chitetezo. M’chenicheni zingakhale zowona kuti “dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.”—Miyambo 15:29; 18:10; Afilipi 4:6.
[Mawu a Chithunzi patsamba 19]
Fotografia de Publicaciones Capriles, Caracas, Venezuela