Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mulungu anachenjeza Kaini kuti ‘uchimo unali kubwatama pakhomo: kwa iye kukakhala kulakalaka kwake,’ zimene zikuonekera ngati zikunena za chilombo chakuthengo ndi nyama yolusiridwa. (Genesis 4:7) Kodi nchifukwa ninji mawu otero anagwiritsiridwa ntchito ngati zinyama zinali kudya zomera zokha Chigumula chisanadze?
M’mabuku olembedwa ndi Mose, timapeza mavesi angapo amene amanena zochitika zenizeni kapena mbiri imene ingaonekere kukhala yosayenerana ndi nthaŵi yake ya mbiri.
Mwachitsanzo, nkhani ya pa Genesis 2:10-14 imapereka tsatanetsatane wa malo a munda wa Edene. Mose analemba kuti mtsinje umodzi “ndiwo wakuyenda cha kummaŵa kwake kwa Asuri.” Koma dziko la Asuri linatenga dzina lake kuchokera ku dzina lakuti Ashuri, mwana wa Semu amene anabadwa pambuyo pa Chigumula. (Genesis 10:8-11, 22; Ezekieli 27:23; Mika 5:6) Malinga ndi umboni, m’cholembedwa chake cholondola, chouziridwa, Mose anangogwiritsira ntchito chabe liwu lakuti “Asuri” kutanthauza chigawo chimene chinali chozoloŵereka kwa oŵerenga ake.
Talingalirani chitsanzo china cha m’machaputala oyambirira a Genesis. Adamu ndi Hava atachimwa ndi kuthamangitsidwa m’mundamo, Yehova anawaletsa kubwererako. Motani? Lemba la Genesis 3:24 limati: “Anamuingitsa munthuyo; nakhazika Makerubi cha kummaŵa kwake kwa munda wa Edene, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.” Onani mawu akuti “lupanga lamoto.” Kodi Mulungu ndiye anayamba kupanga malupanga?
Sitinganene kuti Mlengi wathu wachikondi anali woyamba kupanga amene timawadziŵa kukhala malupanga. Adamu ndi Hava anaona chinachake chikuzungulira patsogolo pa angelo chimene chinali kuyaka moto. Kodi icho chinali chiyani kwenikweni? Panthaŵi imene Mose analemba buku la Genesis, malupanga anali odziŵika bwino ndipo anali kugwiritsiridwa ntchito m’nkhondo. (Genesis 31:26; 34:26; 48:22; Eksodo 5:21; 17:13) Chotero mawu a Mose akuti “lupanga lamoto” anatheketsa oŵerenga ake kuyerekezera kumlingo wakutiwakuti zimene zinali pachipata cha Edene. Zinthu zodziŵika m’tsiku la Mose zinathandizira kumvetsetsa nkhani zotero. Ndipo mawu ogwiritsiridwa ntchito ndi Mose ayenera kukhala ali olondola, popeza kuti Yehova anawaphatikiza m’Baibulo.—2 Timoteo 3:16.
Tsopano bwanji za Genesis 4:7? Pamenepo Mulungu anachenjeza Kaini kuti: “Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.” Monga momwe taonera, mawuwo akuonekera ngati kuti akunena za chilombo chakuthengo chanjala chobwatama ndi kufuna kulikwira nyama yolusiridwa.
Komabe, umboni wa m’Baibulo ukusonyeza kuti Adamu ndi Hava anali pa mtendere ndi zinyama zonse. Zolengedwa zina zingakhale zinali zokondwera kukhala pafupi ndi anthu, kapena ngakhale kupindula ndi kuyandikana koteroko. Zina zinali zilombo zakuthengo, nyama zimene mwachibadwa zinafuna kukhala kutali ndi anthu. (Genesis 1:25, 30; 2:19) Komabe, Baibulo silimapereka lingaliro lakuti nyama zimenezi zinali kulusira nyama zina kapena anthu. Poyambirira, Mulungu anapereka mwachindunji zomera kukhala chakudya cha nyama ndi anthu omwe. (Genesis 1:29, 30; 7:14-16) Zimenezo sizinasinthe kufikira pambuyo pa Chigumula, monga momwe lemba la Genesis 9:2-5 likusonyezera.
Nangano, bwanji ponena za chenjezo la Mulungu kwa Kaini, monga momwe timaŵerengera pa Genesis 4:7? Ndithudi chithunzi cha chilombo cholusa chobwatama ndi chokonzekera kulumphira nyama yolusiridwa chikanamvedwa mosavuta m’tsiku la Mose, ndipo timachimvetsetsanso. Chotero, kachiŵirinso, Mose angakhale anali kugwiritsira ntchito mawu ozoloŵereka kwa oŵerenga a m’dziko la pambuyo pa Chigumula. Ndipo ngakhale ngati Kaini anali asanaonepo cholengedwa choterocho, akanakhala wokhoza kuzindikira chenjezo limene linayerekezera chikhumbo chake chauchimo ndi chilombo chanjala, cholusa.
Mbali zazikulu zimene ziyenera kukhala ndi chisonkhezero chachikulu pa ife ndiizi: Kukoma mtima kwa Mulungu m’kuchenjeza Kaini, phindu la kulandira uphungu modzichepetsa, mmene nsanje ingaipitsire munthu mosavuta, ndi mmene tiyenera kuwonera mwamphamvu machenjezo ena aumulungu amene Mulungu anaika m’Malemba kaamba ka ife.—Eksodo 18:20; Mlaliki 12:12; Ezekieli 3:17-21; 1 Akorinto 10:11; Ahebri 12:11; Yakobo 1:14, 15; Yuda 7, 11.