Kodi Ndani Anakulengani?
1 Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.—Genesis 1:1
2 Mulungu ali ndi dzina. Dzina lake ndilo Yehova.—Salmo 83:18
Yehova amakhala kumwamba. Iye ali mzimu. Simungamuone.—Yesaya 66:1; Yohane 1:18; 4:24
3 Yehova Mulungu anapanga angelo ambiri kumwamba. Iwo nawonso ali mizimu. Iwo onse anali abwino. Kale iwo nthaŵi zina anali kuvala matupi a anthu kotero kuti anthu awaone.—Ahebri 1:7
4 Yehova anapanga nyama kalekale, munthu asanapangidwe.—Genesis 1:25
5 Yehova anapanganso munthu wotchedwa Adamu ndi mkazi wake wotchedwa Hava.—Genesis 1:27
Mulungu anawaika m’munda wokongola, kapena paradaiso. Iye anapangira Adamu mkazi mmodzi yekha. Mwamunayo anayenera kukhala ndi mkazi wake mmodziyo.—Genesis 2:8, 21, 22, 24
6 Munthu ndiye moyo.—Genesis 2:7
7 Nyama zili miyoyo.—Genesis 1:24