Kupita Kumwamba Kapena ku Helo?
“KODI muganiza kuti mudzapita kumwamba kapena ku helo?”
Zimenezi nzimene zinafunsidwa m’kufufuza kopangidwa kwa Aamereka onse kwaposachedwapa. Gulu la Princeton Religion Research Center linafalitsa zotulukapo mu Religion in America 1992-1993.
Kodi inu mukanayankha motani? Kodi mnzanu wa muukwati kapena okondedwa anu ena akuganiza kuti adzapita kumwamba paimfa? Kodi muganiza kuti nzotheka kuti inuyo, kapena iwo, potsirizira pake angapite ku helo?
Kufufuzako kunasonyeza kuti 78 peresenti analingalira kuti mwaŵi wawo wakupita kumwamba unali wooneka kukhala wothekera kapena wosakayikitsa konse, koposa chiŵerengero chimene chinayankha mofananamo pafupifupi zaka 40 zapitazo. Bwanji za ku helo? Pafupifupi 77 peresenti ananena kuti kupita kwawo kumeneko kunali kokayikitsa.
Kodi mayankho awo anali ozikidwa pa chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo? Eya, pafupifupi 4 pa 10 anavomereza kuti anali kupita kumapemphero achipembedzo mwakamodzikamodzi kusiyana ndi mmene ankachitira zaka zisanu kumbuyoko. Okwanira 28 peresenti okha ndiwo ananena kuti anali kupezeka pamagulu ophunzira Baibulo ndipo 27 peresenti anali kukhala ndi phande m’makalasi ophunzitsa zachipembedzo.
Ngati muphunzira Baibulo mosamalitsa, mudzapeza zenizeni zodabwitsa. Mwachitsanzo, Baibulo limatchula momvekera bwino kuti paimfa Yesu anapita ku “helo,” monga momwe Mabaibulo ena amatembenuzira mawuwo. (Machitidwe 2:31, King James Version; “Hade,” New World Translation) Mawu a Mulungu amatsimikiziranso kuti Mfumu Davide ndipo ngakhale Yohane Mbatizi sanapite kumwamba paimfa. (Mateyu 11:11; Machitidwe 2:29) Zimenezo zinali zenizeni, osati malingaliro chabe ochokera m’kufufuza kwachipembedzo.
Nazi zenizeni zina zimene zingakuyambukireni: Baibulo limaphunzitsa kuti atumwi a Yesu ndi anthu ena oŵerengeka adzatengeredwa kumwamba kukalamulira pamodzi ndi Yesu. Komabe, anthu ochuluka amene anamwalira anangopita ku manda wamba a anthu. Mulungu adzawaukitsa, kuwabwezeretsa ku moyo padziko lapansi ndi chiyembekezo cha moyo wokhutiritsa, wachimwemwe ndi wosatha m’paradaiso wobwezeretsedwa wa padziko lapansi.
Mboni za Yehova zidzakhala zokondwera kukuthandizani kuyala maziko a chiyembekezo chodalirika chimenecho kuchokera m’Baibulo lanu lenilenilo.