Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 2/15 tsamba 31
  • Mmene Mpingo Wachikristu Walinganizidwira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mpingo Wachikristu Walinganizidwira
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 2/15 tsamba 31

Mmene Mpingo Wachikristu Walinganizidwira

NGAKHALE kuti mipingo Yachikristu ya Mulungu inakhazikitsidwa m’malo osiyanasiyana, iyo sinayendetse zinthu modziimira payokha. Ndipo siimatero ndi lero lomwe. M’malo mwake, iyo yonse inazindikira ulamuliro wa bungwe lolamulira Lachikristu lokhala ku Yerusalemu. Bungwe lolamulira limeneli linapangidwa ndi atumwi ndi akulu a mpingo wa Yerusalemu, ndipo panalibe mabungwe ena otsutsa kwina kulikonse ofuna kuyang’anira mpingo. Kunali kwa bungwe lolamulira Lachikristu lokhulupirikalo la m’zaka za zana loyamba C.E. kumene nkhani ya mdulidwe inaperekedwa kukaipenda. Pamene bungwe lolamulira linapanga chosankha chake, motsogozedwa ndi mzimu woyera, chosankhacho chinalandiridwa ndi kukhala chogwira ntchito pamipingo yonse Yachikristu, ndipo iyo inali yofunitsitsa kuchilabadira. Ife timatsatira chitsanzo cha bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba.​—Machitidwe 15:22-31.

Bungwe Lachikristu mu Yerusalemu linatumiza oimira oyendayenda. Motero, Paulo ndi ena anapereka chosankha cha bungwe lolamulira chimene tatchulacho, chofotokozedwa motere: “Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akulu a pa Yerusalemu.” Ponena za chiyambukiro chotsatirapo, kwanenedwa kuti: “Kotero mipingoyo inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiŵerengo chawo tsiku ndi tsiku.” (Machitidwe 16:4, 5) Mofananamo, oyang’anira oyendayenda lerolino, mofanana ndi m’zaka za zana loyamba, amathandizira kupereka zosankha ndi zitsogozo za Bungwe Lolamulira. Kodi pamakhala mapindu otani? Kukhazikika kwauzimu ndi chiwonjezeko!

Mipingo umodzi ndi umodzi inamamatira kwambiri kuchitsogozo cha bungwe lolamulira Lachikristu, limene linayang’anira kuikidwa kwa akulu. (Tito 1:1, 5) Choncho zinali motero, kuti potsogozedwa ndi bungwe lolamulira Lachikristu losonkhezeredwa ndi mzimu woyera, oyang’anira limodzinso ndi othandiza, atumiki otumikira, anaikidwa pampingo uliwonse. Amuna ameneŵa oikidwa m’malo a udindo ndi thayo anafunikira kufikira ziyeneretso zakutizakuti. (1 Timoteo 3:1-13; Tito 1:5-9) Oimira oyendayenda a bungwe lolamulira, onga ngati Paulo, anatsatira Kristu ndipo anakhazikitsa chitsanzo chabwino chochitsanzira. (1 Akorinto 11:1; Afilipi 4:9) Kwenikweni, onsewo okhala m’malo a ubusa wauzimu anafunikira kukhala “zitsanzo za gululo” (1 Peter 5:2, 3), anafunikira kusonyeza nkhaŵa yachikondi kwa munthu mmodzi ndi mmodzi mumpingo (1 Atesalonika 2:5-12), ndipo anafunikira kukhala chithandizo chenicheni kwa awo odwala mwauzimu.​—Agalatiya 6:1; Yakobo 5:13-16.

Chifukwa chake, monga momwe Yehova analinganizira mpingo wa Israyeli pansi pa amuna akulu, mitu, oweruza ndi adindo (Yoswa 23:2), Iye anaikanso uyang’aniro wa mpingo Wachikristu mwa kuchititsa kuikidwa kwa amuna akulu m’malo athayo mmenemo. (Machitidwe 14:23) Ndipo, monga momwe amuna athayo nthaŵi zina anachitira zinthu moimira mpingo wonse wa Israyeli, monga m’nkhani zachiweruzo (Deuteronomo 16:18), Mulungu analinganiza mpingo umodzi ndi umodzi Wachikristu kuimiriridwa mofananamo m’nkhani zoterozo ndi amuna oikidwa m’malo aulamuliro ndi mzimu woyera. (Machitidwe 20:28; 1 Akorinto 5:1-5) Komabe, ngati pabuka zovuta pakati pa ziwalo za mpingo Wachikristu wa Mulungu, mawu a Yesu Kristu olembedwa pa Mateyu 18:15-17 (olankhulidwa pamene mpingo Wachiyuda wa Mulungu unali usanakanidwe ndi Yehova ndipo motero poyambirira ogwira ntchito kwa uwo) anagwira ntchito monga maziko othetsera kapena osamalirira mavuto otero.

Kuti apindulitse mpingo ndi “mphatso mwa amuna” (NW), Yehova Mulungu waika ziwalo mu “thupi” lauzimu la Kristu “monga anafuna.” Ndipo Paulo anati: “Mulungu anaika ena [mumpingo, NW], poyamba atumwi, achiŵiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundu mitundu.” Sionse amene anachita ntchito zofanana, koma onse anali ofunika mumpingo Wachikristu. (1 Akorinto 12:12-31) Paulo anafotokoza kuti kuperekedwa kwa atumwi, aneneri, alaliki, abusa, ndi aphunzitsi mumpingo Wachikristu kunali kaamba kakuti “akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu.”​—Aefeso 4:11-16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena