Lipoti la Olengeza Ufumu
Chowonadi cha Baibulo Chigwirizanitsa Banja
LEROLINO, m’mbali zambiri za dziko, umodzi wa banja kulibiretu. Komabe, Baibulo limavumbula chinsinsi cha umodzi wa banja. Talingalirani mawu a Yesu awa: “Yense amene akamva mawu anga ameneŵa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.” (Mateyu 7:24) Zikwizikwi za mabanja a Mboni za Yehova zapeza umodzi mwa kugwiritsira ntchito mawu ameneŵa ndi kugwiritsira ntchito Baibulo monga maziko omangira banja logwirizana. Ena akupezanso umodzi woterowo, monga momwe chokumana nacho chotsatirachi chikusonyezera.
Pamene Daniel anali kutumikira m’gulu lankhondo ku France, mtsogoleri wachipembedzo wa gulu lankhondo anapereka lingaliro lakuti Daniel agule Baibulo, limene analigula, ndipo anayamba kuliŵerenga nthaŵi zonse. Pomalizira pake anasamutsidwira ku Tahiti. Ena a asilikali anzake a Daniel anali achipembedzo cha Adventist, ndipo ena anali a Mormon. Kaŵirikaŵiri makambitsirano awo anali kukhudza nkhani yachipembedzo. Tsiku lina mtsogoleri wankhondo anadziŵikitsa Daniel kwa mkazi wake, amene anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Mkaziyo anathera masana onse akuyankha mafunso ambiri a Daniel namudziŵikitsa ku mpingo wa Mboni za Yehova wa ku Tahiti. Posakhalitsa anayamba phunziro la Baibulo lokhazikika.
Makolo a Daniel ku France anali Akatolika owona mtima. Atate ake anali phungu wa sukulu ndipo anali woyang’anira maphunziro achipembedzo pa sukulu Yachikatolika. Pofuna kugaŵana ndi makolo ake chidziŵitso chamtengo wake chauzimu chimene anali kuphunzira, Daniel anayamba kuphatikiza pang’onopang’ono malingaliro angapo a m’Baibulo m’makalata ake opita kwa iwo.
Poyamba amake Daniel anakondwera, komano anachita mantha kupeza dzina lakuti Yehova mu imodzi ya makalata a mwana wawo. Masiku angapo pambuyo pake, mayiyo anamva programu ya pa wailesi imene inatcha Mboni za Yehova kukhala “kagulu kampatuko kowopsa.” Iwo analembera Daniel, kumupempha kuleka mwamsanga kugwirizana kulikonse ndi Mboni. Komabe, Daniel anapitiriza kupita patsogolo m’phunziro lake la Baibulo ndipo posakhalitsa anapanga makonzedwe a kuchoka m’gulu lankhondo ndi kubwerera ku France.
Atangobwerera kunyumba, Daniel anathera madzulo aliwonse—nthaŵi zina mpaka usiku ndithu—m’kukambitsirana Baibulo ndi amake. Pomalizira pake anavomereza kutsagana ndi Daniel ku Nyumba Yaufumu. Pamene anafika pamsonkhano woyamba, anakondweretsedwa kwambiri kwakuti anayamba phunziro lawo lokhazikika la Baibulo. Anapanga kupita patsogolo kofulumira ndipo posapita nthaŵi anabatizidwa.
Atate a Daniel anali mwamuna wololera koma odzipereka kwambiri ku ntchito yawo ndi machitachita achipembedzo. Komabe, tsiku lina anaperekeza pagalimoto akazi awo ndi Daniel ku msonkhano wachigawo. Panali pa July 14, ndipo anali ndi cholinga chokaonerera perete wa Bastille Day mumzinda. Akudikirira, analingalira zoloŵa mkati mwa holo yamsonkhanoyo kuti akaone zimene zinali kuchitika. Iwo anakondweretsedwa ndi dongosolo ndi mtendere umene anaona pakati pa anthu a Yehova, ndipo pamene anali kudutsa madipatimenti amsonkhano osiyanasiyana aliyense anali kuwatcha “mbale.” Anaiwala zonse za perete wa Bastille Day nakhala mpaka mapeto a msonkhanowo. Iwo anapempha phunziro la Baibulo ndipo anapanga kupita patsogolo kofulumira pophunzira chowonadi. Komabe, pamene anaphunzira zambiri, anavutika kwambiri maganizo chifukwa cha mtundu wa ntchito yawo, chotero pamsinkhu wa zaka 58, anasiya ntchito yawo. Tsopano onse atatu m’banjamo ali odzipatulira ndi obatizidwa ndipo akutumikira Yehova pamodzi mogwirizana.
Chinali chowonadi cha Baibulo chimene chinagwirizanitsa banja la Daniel. Chingagwirizanitsenso mabanja ena ngati achiphunzira ndi kuchigwiritsira ntchito ndi mtima wonse.