Akufa Anu Okondedwa—Kodi Ali Kuti?
ALEC anathedwa nzeru. Mkati mwa mlungu umodzi, anataikiridwa aŵiri a mabwenzi ake. Mmodzi wa iwo, Nevil, anamwalira ndi chilonda cha mfuti. Winayo, Tony, anaphedwa pa ngozi ya galimoto. Mafunso omwe anali asanamvutitsepo ndi kale lonse tsopano anakantha mnyamata wazaka 14 wa ku South Africa ameneyu. ‘Kodi nchifukwa ninji anthu ayenera kufa? Ndipo kodi nchiyani chimachitika pambuyo pa imfa?’ iye anadabwa motero.
Ali paulendo wopita kumaliro a Nevil, Alec anayembekezera moona mtima kuti akapeza mayankho a mafunso ameneŵa. “Koma,” iye akukumbukira, “wansembeyo anangoŵerenga m’buku ndi kunena kuti Nevil anapita kumwamba. Ndiyeno, kumandako, iye anati timadikirira chiukiriro. Ndinasokonezeka. Ngati Nevil anali kumwamba, kodi angamadikirire chiukiriro motani?”
Pambuyo pake tsiku lomwelo, Alec anapita kumaliro a Tony. Mwambowo unachitidwa m’chinenero chimene sanamve. Komabe, khalidwe la chisoni chosalamulirika la olira ena linakhutiritsa Alec kuti panalibe chitonthozo chomwe chinaperekedwa. “Usiku umenewo,” iye akulongosola motero, “ndinakwiya kwambiri. Ndinadziona kukhala wopanda chithandizo ndi wotayika. Palibe amene akanapereka mayankho okhutiritsa a mafunso anga. Kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga, ndinakayikiradi ngati kuli Mulungu.”
Chaka chilichonse mamiliyoni, mofanana ndi Alec, amatayikiridwa okondedwa awo mu imfa. “Padziko lonse,” ikulongosola motero 1992 Britannica Book of the Year, “panachitika imfa 50,418,000 mu 1991.” Ndipo kodi ndi mamiliyoni owonjezereka ochuluka motani amene afa chiyambire nthaŵiyo? Tayerekezerani mitsinje ya misozi imene yakhetsedwa ndi oferedwa otsalawo! Chomwe chikuwonjezera chisoni chawo ndicho chisokonezo chochititsidwa ndi malingaliro otsutsana onena za imfa.
Motero ambiri, mofanana ndi Alec, amataya mtima ndi kukayikira ngati pali maziko alionse a chiyembekezo cha moyo wa mtsogolo pambuyo pa imfa. Malinga ndi kunena kwa Encyclopedia of Religions, “m’nyengo zonse, anthu oganiza akhala osiyana ndi namtindi, . . . akumakayikira kuti kodi moyo (soul) kapena moyo (life) wokha ungakhaleko motani popanda ubongo ndi thupi.”
Mokondweretsa, buku la nazonse lotchulidwa pamwambalo limavomereza kuti nthanthi yachipembedzo ya moyo wosafa wokhalapo kunja kwa thupi simachirikizidwa m’Baibulo. Zoona, m’malo oŵerengeka, Baibulo limanenadi za “moyo” wa munthu kukhala ukuchoka ndipo ngakhale kubwerera ku thupi lakufa, koma m’zochitika zimenezi “moyo” (soul) umagwiritsiridwa ntchito m’lingaliro la “moyo” (life), wotayika kapena kupezedwanso. (Genesis 35:16-19, NW; 1 Mafumu 17:17-23) Mobwerezabwereza kwambiri, liwu lakuti “moyo” (soul) limagwiritsiridwa ntchito m’Baibulo kulongosola zolengedwa zooneka za thupi ndi mwazi, inde, zolengedwa zamoyo. (Genesis 1:20; 2:7) Chifukwa chake, Baibulo limanena mobwerezabwereza kuti miyoyo imafa. (Ezekieli 18:4, 20; Machitidwe 3:23; Chivumbulutso 16:3) Mawu a Mulungu amanena kuti miyoyo itafa, ‘siidziŵa kanthu bi.’—Mlaliki 9:5, 10.
Kumbali ina, Baibulo lili ndi zolembedwa za anthu akufa kukhala akubwezeretsedwa ku moyo. M’chochitika cha Lazaro, zimenezi zinachitika atakhala wakufa kwa masiku anayi. (Yohane 11:39, 43, 44) Komano, kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa anthu amene anafa zaka mazana kapena zikwi zapitazo? Kodi chiyembekezo chawo cha moyo wa mtsogolo chimafunikira kuti Mulungu adzaukitse thupi lenileni limene anali nalo pamene anafa?
Ayi. Lingaliro lotero silili logwirizana ndi zimene zimachitikira maatomu amene amapanga thupi lakufa. M’kupita kwa nthaŵi, ena a maatomu amodzimodziŵa amatengedwa ndi zomera zimene, nazonso, zimadyedwa ndi zolengedwa zina ndi kukhala mbali ya matupi awo.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe chiyembekezo kwa anthu amene anafa kalekale? Ayi. Mlengi wa chilengedwe chathu chachikuluchi ali ndi chikumbukiro chachikulu, chopanda malire. Mkati mwa chikumbukiro chake changwiro, ali ndi kuthekera kwa kusungamo umunthu ndi kapangidwe ka majini a munthu wakufa amene iye asankha kumkumbukira. Ndiponso, Yehova Mulungu ali ndi mphamvu ya kulenganso thupi laumunthu lokhala ndi majini ofanana ndendende ndi a munthu amene anakhalako kale. Iye angaikenso mkati mwake chikumbukiro ndi umunthu wa uyo amene akumbukira, monga ngati Abrahamu.
Pafupifupi zaka zikwi ziŵiri pambuyo pa imfa ya Abrahamu, Yesu Kristu anapereka chitsimikiziro ichi: “Za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye amtchulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye.” (Luka 20:37, 38) Kuwonjezera pa Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, mamiliyoni a anthu ena akufa ali amoyo m’chikumbukiro cha Mulungu, kudikirira chiukiriro chikudzacho. “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama,” limatsimikizira motero Baibulo.—Machitidwe 24:15.
Milungu yoŵerengeka pambuyo pa kuferedwa kwake, Alec anapeza mayankho a mafunso ake. Mmodzi wa Mboni za Yehova anafika panyumba pake namusonyeza zimene Mawu a Mulungu amanena ponena za imfa ndi ponena za chiukiriro. Zimenezi zinatonthoza Alec ndi kudzetsa tanthauzo latsopano m’moyo wake.
Kodi nanunso mungakonde kuphunzira zambiri ponena za chiyembekezo cha chiukiriro chozikidwa pa Baibulo? Mwachitsanzo, kodi kuuka kochuluka kudzachitikira kumwamba kapena padziko lapansi? Ndipo kodi munthu ayenera kuchita chiyani kuti apeze chivomerezo cha Mulungu ndi kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo Lake labwino koposa lakuti anthu angagwirizanenso ndi akufa okondedwa?