Msonkhano Wachigawo Wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu” wa Ethiopia—Nthaŵi ya Chisangalalo Chapadera
UMENEWU sunali msonkhano wachigawo woyamba kuchitidwa mu Ethiopia pambuyo pa kupeza ufulu wa kulambira, koma unalidi wapadera. Kuyambira pamene zinapeza chivomerezo chalamulo pa November 11, 1991, Mboni za Yehova zinasonkhana kachitatu m’sitediyamu yaikulu m’dzikolo, yotchedwa City Stadium, pakati penipeni pa Addis Ababa. Popeza kuti poyamba kunali kosatheka kugwiritsira ntchito bwalo limeneli pa Sande ndipo panalibe malo ena aakulu bwino amene anapezeka, programuyo inapanikizidwa m’masiku atatu, kuyambira pa Lachinayi mpaka pa Loŵeruka, January 13-15, 1994.
Masiku atatu ameneŵa sanali chabe ndi kachedwe kakunja kabwino ndi kokongola pansi pa thambo lobiriŵira, komanso anali ndi kuunikira kwauzimu kokhala ndi mphamvu yonse ya “Chiphunzitso Chaumulngu.” Pokhala pamalo okonzedwa bwino ndi maluŵa okongola kuzungulira pulatifomu, mutu wa msonkhanowo unaonekera bwino lomwe m’malembo Achiamharic.
Koma kodi nchiyani chimene chinachititsa msonkhanowo kukhala wapadera? Kuwonjezera pa programu yopindulitsa, maganizo ndi mtima wa aliyense unakopeka ndi ubale wathu wachikondi wa dziko lonse ndi maumboni oonekera bwino a dalitso la Mulungu pa anthu ake loonekera m’chiwonjezeko cha Ufumu. Panali nthumwi zakunja pafupifupi 270 zochokera kumaiko 16, kuphatikizapo ngakhale Djibouti ndi Yemen. Zoposa theka zinachokera kumadera ozizira a ku Ulaya ndi North America. Alendowo anaphatikizapo ziŵalo ziŵiri za Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, Lloyd Barry ndi Daniel Sydlik.
Kuchereza alendo kwamwambo kwa anthu a ku Ethiopia limodzi ndi chikondi chochokera mumtima kwa abale awo alendowo zinachititsa chisangalalo chimene chinagonjetsa vuto la kusamvana zinenero. Sanali kupatsana moni mwa kungogwirana chanza chabe komanso mwa kukupatirana ndi kupsompsonana, mobwerezabwereza kasanu ndi kamodzi! Alendo ambiri anali ataŵerenga za ntchito ya Ufumu m’Ethiopia ndipo anadziŵa kuti abale awo a ku Ethiopia anali osunga umphumphu oyesedwa amene anali atapirira kuponyedwa m’ndende ndi mitundu ina ya zizunzo.a Koma nthumwi zochokera kunjazo zinadabwa kuona achichepere ambiri ali ndi nkhope zachimwemwe ndipo akusonyeza ulemu umene ukuzimiririka m’maiko ochuluka lerolino. Alongo ambiri a ku Ethiopia anavala maderesi awo oyera amwambo okometseredwa mwaluso, amene anawonjezeradi mzimu wachisangalalo.
Ubatizo pa Lachisanu unalidi wokondweretsa. Mzera wautali wa odzipatulira chatsopano 530, a zaka zakubadwa kuyambira pa 10 mpaka 80, unapyola pakati pa bwalo loseŵerera m’sitediyamu. Zimenezi zinaposeratu zimene aliyense anali kuyembekezera—kugaŵa koposa munthu 1 pa Mboni 7 zilizonse m’dzikoli. Umenewu ndi umboni wotani nanga wa dalitso la Yehova pa anthu ake kunoko! Ambiri anagwetsa misozi ya chimwemwe poona zimenezi, chochitika chimene chinakometseredwa ndi maimbidwe okoma a nthumwi zoposa 40 za ku Italy. Ambiri anakumbukira mawu aulosi a Yesaya 60:5: “Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe.”
Zochititsa Chisangalalo Zapadera
Dalitso la Yehova linasonyezedwa mowonjezereka pa Lachisanu, pamene ziyambi zazing’ono za ntchito ya Ufumu m’Ethiopia zinasimbidwa panthaŵi ya kufunsa. Ofunsidwawo anali gulu la amishonale oyambirira amene anatumikira kumeneko m’ma 1950 ndi m’ma 1970. Anthu oposa 8,000 anamva Ray Casson, John Kamphuis, ndi Haywood Ward akufotokoza ntchito yawo ya kuphunzitsa Baibulo, kuyambira pa September 14, 1950, pamene anafika m’Addis Ababa. Boma lachifumu la masikuwo linafuna kuti iwo aziphunzitsa anthu maphunziro akusukulu. Chotero iwo anakhazikitsa sukulu yophunzitsa achikulire mkati mwa tauni, akumaphunzitsa maphunziro osiyanasiyana. Koma panthaŵi imene anali omasuka, amishonale ameneŵa anayesayesa kupititsa patsogolo maphunziro onena za chiphunzitso chaumulungu. Analimbana ndi kuphunzira Chiamharic, chinenero chovuta chokhala ndi alufabeti ya zilembo 250. Kunawatengera pafupifupi theka la chaka kuti ayambe kuchititsa phunziro lawo loyamba la Baibulo lapanyumba. Pambuyo pa zaka pafupifupi 43, anakumana ndi anthu m’khwalala amene anakumbukira aphunzitsi awo akale ameneŵa. Komabe, iwo anakondwera pamsonkhanopo kukumananso ndi ochuluka a ophunzira Baibulo awo akale amene anakhala olimba m’chikhulupiriro, ndi amene anawasonyeza kwa ana awo ndi adzukulu awo auzimu.—1 Atesalonika 2:19, 20.
Omvetsera achimwemwe ndi otchera khutuwo anawomba m’manja kwa nthaŵi yaitali osati chabe kaamba ka mayankho a amishonale pakufunsako komanso kaamba ka malipoti ndi malonje ochokera ku Britain, Canada, Germany, Israel, Italy, Kenya, Netherlands, ndi United States—obwera ndi nthumwi za maiko akunja. Zimenezi zinasonyezanso ubale wachikondi wa dziko lonse wa anthu a Mulungu. Nkhani zazikulu zokambidwa ndi abale a m’Bungwe Lolamulira, limodzinso ndi mapemphero awo ogwira mtima, zinakhudza kwambiri mitima ya omvetserawo. Achichepere m’sitediyamu anaona kuti anakhudzidwa ndi oseŵera drama la achichepere amene amakumbukira Mlengi wawo, dramalo likumachitidwa mwachibadwa kwambiri ndi mwaumoyo. Kuwonjezera pa zotulutsidwa zatsopano m’Chingelezi, zotulutsidwa zitatu zatsopano m’Chiamharic zinachititsa chikondwerero chachikulu.b
Popuma ndi panthaŵi zina, panali mipata yabwino yodziŵira anthu ambiri okondedwa. Mwachitsanzo, mumzera wa kutsogolo weniweni, munakhala wofalitsa wokalamba koposa m’Ethiopia, Tulu Mekuria, amene anali ndi ndodo yopanga ndi manja. Chaka chatha, paukalamba wotheratu wa zaka 113, anabatizidwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Pamsonkhanowu anakondwera kuona mkazi wake wazaka 80 akutsanzira chitsanzo chake, akumakhalanso mlongo wake wauzimu. Kukhalapo kwake pa programu yonseyo kunasonkhezera kwambiri achichepere. Mmodzi wa iwo anali Yohanes Gorems, amene pa usinkhu wa zaka 16 ndipo akali pasukulu, watumikira kale zaka zinayi monga wofalitsa amene ali mpainiya wokhazikika. Iyeyo ndi apainiya ena ausinkhu wopita kusukulu amene alidi ocheperapo aphunzira kuwombola nthaŵi yoyenera, mwa kuchita umboni mmamaŵa popita kusukulu kapena mwa kugwiritsira ntchito nthaŵi yopuma ndi maola apambuyo pa sukulu.
Ali Zitsanzo za Umphumphu Chotani Nanga!
Ambiri mwa omvetserawo anaponyedwapo m’ndende ndi kuzunzidwa m’maboma akumbuyoku. Mandefro Yifru amakumbukira zaka zisanu zotero zimene anathera m’ndende, koma tsopano akukondwa kutumikira ku Addis Ababa mu ofesi yokhazikitsidwa chatsopano, imene imasamalira ntchito za kutembenuza, kusindikiza, ndi mitokoma. Mnyamata wina amene akutumikira limodzi naye, Zecarias Eshetu, sanataye umphumphu wake zaka zisanu ndi zitatu zapitazo pamene atate wake anaphedwa chifukwa chosunga uchete Wachikristu m’zaka zitatu zimene anakhala m’ndende. Zecarias, mmodzi wa ana asanu, anali ndi zaka khumi pamene atate wake anapita kundende. Meswat Girma ndi mchemwali wake, Yoalan, amene tsopano ali kumapeto kwa zaka za 13 mpaka 19 ndipo akali pasukulu, amakumbukira atate wawo pa zithunzithunzi pokha, pakuti anali aang’ono kwambiri pamene atate wawo ananyongedwa mwadzidzidzi chifukwa cha uchete wawo. Kukhulupirika kwawo kunawasonkhezera, ndipo onse aŵiri akutumikira monga apainiya okhazikika, monga momwe atate wawo anali kuchitira panthaŵi ya imfa yawo.
Wosunga umphumphu wina anali Tamirat Yadette, amene akutumikira monga mpainiya wapadera kudera lokongola la Rift Valley. Chifukwa cha uchete wake Wachikristu, anathera zaka zitatu m’ndende zisanu ndi ziŵiri zosiyanasiyana, nthaŵi zina kumangidwa maunyolo ndi kumenyedwa kowopsa. Komabe, m’ndendemo anathandiza anthu oposa khumi ndi aŵiri kuima kumbali ya Ufumu wa Mulungu.
Tesfu Temelso, amene tsopano akutumikira monga woyang’anira dera, anaponyedwa m’ndende nthaŵi 17 m’zaka zimene anali kutumikira monga mpainiya wapadera. Iye ali ndi zipsera za kumenyedwa, koma ali wachimwemwe kuona mipingo m’magawo ake akale. Abale ndi alongo ochuluka a ku Mpingo wa Akaki anaponyedwa m’ndende ndi kuchitiridwa nkhanza, komabe mpingowo wakula kukhala ndi ofalitsa oposa zana limodzi. Iwo amanga Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova yoyamba m’Ethiopia. Ku Dese, tauni yokongola pamtunda wa pafupifupi makilomita 300 kumpoto kwa likulu, kunachokera kagulu ka anthu asanu amene anayang’anizana ndi imfa ndi kuona mbale wakomweko alikufa chifukwa cha kuzunzidwa. Mkulu wina pakati pawo, Maseresha Kasa, anafotokoza kuti anapirira zaka zisanu ndi chimodzi m’ndende, osati chifukwa chakuti anali wapadera mwanjira ina, koma chifukwa chakuti anaphunzira kudalira Yehova basi.—Aroma 8:35-39; yerekezerani ndi Machitidwe 8:1.
Ngakhale posachedwapa, ena asonyeza kukhulupirika kwawo poyesedwa. Gulu lina lalikulu linadza kumsonkhano kuchokera kudziko loyandikana nalo, kumene, chifukwa cha uchete wawo, Mboni zinamanidwa chitetezo cha apolisi, ziphaso zoyendera, mitchato, chithandizo cha chipatala, ndi ntchito. Pamene nkhondo inali kumenyedwa pafupi ndi Mesewa, doko la ku Eritrea ku Nyanja Yofiira, mpingo wonsewo, anthu 39, kuphatikizapo ana, anakhala pafupifupi miyezi inayi m’chipululu mmunsi mwa ulalo wotsika mmene anathaŵira kusiya nyumba zawo zimene boma lakale linali kuphulitsa ndi mabomba. M’malo ameneŵa otentha ndi osoŵa zofunikira, makambitsirano awo a lemba latsiku ndi misonkhano ina zinawapatsa nyonga yaikulu ndi kukulitsa unansi wathithithi ndi Yehova ndi wina ndi mnzake. Alongo aŵiri omwe ali apainiya apadera amene akutumikira pafupi ndi magwero a mtsinje wa Blue Nile anapirira ziwopsezo za magulu achiwawa ndi kusautsidwa kosonkhezeredwa ndi Tchalitchi cha Orthodox, koma aŵiriwo anapirirabe naona ophunzira Baibulo awo angapo akusonyeza kudzipatulira kwawo mwa ubatizo pamsonkhano umenewu.
Mbale wina anasimba chiyeso chake cha kukhala yekha kutali pantchito mkati mwenimweni mwa chigawo chotentha cha Ogaden, pafupi ndi Somalia. Anapitiriza kukhala wamoyo mwauzimu mwa kulalikira ndiyeno mwa kuchita misonkhano ndi okondwerera, kuphatikizapo madokotala, amene anapindula ndi chiphunzitso chaumulungu ndipo tsopano nawonso akuphunzitsa ena. Wina amene anapereka chitsanzo chabwino cha kusunga umphumphu anali mpainiya wapadera m’Addis Ababa amene, mu 1992, anamenyedwa kowopsa ndi gulu losonkhezeredwa ndi ansembe a Orthodox nasiyidwa atakomoka. Mwamwaŵi, anachira ndipo akupitirizabe kutumikira m’gawo limodzimodzilo. Nkhope yake yachimwemwe simasonyeza udani uliwonse. Kwa iye, mofanana ndi ena onse oyesedwa ndi achatsopano, Msonkhano uwu wakuti “Chiphunzitso Chaumulungu” unali phwando la chisangalalo.
Kakonzedwe ka msonkhanowo kanayenda bwino lomwe, kakumachititsa alendo kulingalira kuti antchito odzifunira oloŵetsedwamo anali ndi kuzoloŵera kwa zaka zambiri. Kwenikweni, iwo apita patsogolo mofulumira m’zaka ziŵiri zapitazo. Msonkhano wamasiku atatu unaoneka monga unatha mofulumira kwambiri. Chiŵerengero chapamwamba cha opezekapo pa Loŵeruka chinali 9,556. Nyumba ya wailesi yakanema ndi ya wailesi yamawu za dzikolo, ndi manyuzipepala zinafalitsa bwino nkhani zake. Onse anakhoza kuona kuti Yehova anali kulemeretsa anthu ake mwauzimu. Omvetserawo anaphatikizapo okondwerera zikwi zambiri amene ayamba kupindula ndi “Chiphunzitso Chaumulungu.” Munda waukulu watsegukira Mboni za Yehova m’dzikoli la anthu pafupifupi 50 miliyoni, ndipo msonkhanowo unalimbitsa onse m’kutsimikiza kwawo kugwiritsira ntchito nthaŵi yotsala m’dongosolo ili la zinthu kuthandizira oona mtima kuti nawonso apindule ndi chiphunzitso chaumulungu.
[Mawu a M’munsi]
a Onani 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Your Youth—Getting the Best Out Of It, Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe, ndi Mboni za Yehova—Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi.
[Zithunzi patsamba 23]
Addis Ababa, January 13-15, 1994
[Zithunzi patsamba 24]
Kagulu ka apainiya ku Addis Ababa (kulamanja); osunga umphumphu onsewo anali m’ndende (pansi); Mboni ya zaka 113 ndi mkazi wake