“Chipangidwe Changa . . . ndi Chodabwiza”
“KODI ndinachokera kuti?” Limeneli ndi funso limene ana ambiri amafunsa nthaŵi ndi nthaŵi. Pamene ana akukula, kaŵirikaŵiri funso lawo limakhala lofufuza kwambiri: “Kodi moyo unachokera kuti?” Funso limeneli lakambitsiridwa kwa zaka zikwi zambiri, ndipo pakali pano asayansi ambiri amalingalira chisinthiko kukhala yankho loyenerera koposa ponena za chiyambi cha moyo chovuta kumvetsetsacho. Kwakukulukulu, mafotokozedwe a katswiri wachisinthiko ngakuti moyo unakhalapo mwangozi.
Pafupifupi zaka 3,000 zapitazo, Mfumu Davide analemba kuti: “Chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza.” (Salmo 139:14) Pamene tiphunzira zambiri ponena za moyo, mpamenenso timaona kwambiri choonadi cha mawuwo. Ndithudi, katswiri wa physics Fred Hoyle analemba kuti: “Akatswiri a biochemistry atulukira zowonjezereka za kucholoŵana kowopsa kwa moyo, nkwachionekere kuti kuyambika kwangoziko nkwakung’ono kwambiri kwakuti kungathe kunyalanyazidwa. Moyo sunangokhalapo mwangozi.”
Chotero kodi chiyambi cha moyo nchotani? Nkhani ziŵiri zoyamba za magazini ano zikuyankha funso limenelo. Ngati mungafune kupeza chidziŵitso chowonjezereka, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera yondandalikidwa patsamba 2.