Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 9/15 tsamba 3-4
  • Kodi Muli Wokhululukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muli Wokhululukira?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhululukira Kuli Kovuta
  • ‘Pitirizani Kukhululukirana Eni Okha’
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Khululukani Kuchokera Mumtima
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Muzikhululukirana ndi Mtima Wonse
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Nkukhaliranji Wokhululukira?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 9/15 tsamba 3-4

Kodi Muli Wokhululukira?

BILL ndi mwana wake wamkazi wazaka 16, Lisa, sanali kumvana. Kaŵirikaŵiri mikangano yawo yaing’ono inkakula kukhala kulalatirana. Potsirizira pake, vutolo linakula kufikira pamene Lisa anapemphedwa kuchoka panyumba.a

Patapita nthaŵi, Lisa anazindikira kuti anali wolakwa napempha atate ake kumkhululukira. Koma mmalo monyalanyaza zolakwa zakale za Lisa, atate ake opwetekedwa mtimawo anakana zoyesayesa zake za kupanga mtendere. Tangolingalirani! Iwo sanafune kusonyeza chifundo kwa mwana wawo weniweni wamkazi!

Zaka mazana ambiri zapitazo munthu wosalakwa anaweruzidwa kufa chifukwa cha upandu umene sanachite. Mboni zinapereka umboni wonama, ndipo akuluakulu a ndale anakana dala kuchita chilungamo. Munthu wopanda liwongo ameneyo anali Yesu Kristu. Atatsala pang’ono kufa, iye anapempha Mulungu m’pemphero kuti: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.”​—Luka 23:34.

Yesu anakhululukira mwaufulu, kuchokera mumtima mwake, ndipo otsatira ake anafulumizidwa kumtsanzira m’nkhaniyi. (Aefeso 4:32) Komabe, mofanana ndi Bill, ena mouma mtima samafuna kukhululuka. Kodi inu mukuchita motani pankhaniyi? Kodi muli wofunitsitsa kukhululukira ena pamene akuchimwirani? Ndipo bwanji ponena za machimo aakulu? Kodi ameneŵanso ayenera kukhululukidwa?

Kukhululukira Kuli Kovuta

Nthaŵi zina kukhululukira kumakhala kovuta. Ndipo m’nthaŵi zino zoŵaŵitsa, maunansi aumunthu akhala ovutirapo kwambiri. Makamaka moyo wa banja uli wodzala ndi zipsinjo ndi zitsenderezo. Kalelo mtumwi Wachikristu Paulo ananena kuti mikhalidwe yotero ikafika pachimake mu “masiku otsiriza.” Iye anati: “Anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, . . . osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima.”​—2 Timoteo 3:1-4.

Pamenepa, mosapeŵeka, tonsefe timayang’anizana ndi zitsenderezo zakunja zimene zimayesa kukhoza kwathu kwa kukhululukira ena. Ndiponso, timalimbananso ndi zitsenderezo za mkati. Paulo anadandaula kuti: “Chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe mkati mwanga ndiwo.” (Aroma 7:19, 20) Chotero, ambiri a ife sitili okhululukira monga mmene tingafunire kukhalira. Ndi iko komwe, kupanda ungwiro kwa choloŵa ndi uchimo zili ndi chisonkhezero champhamvu kwambiri pa tonsefe, nthaŵi zina zikumatilanda chifundo cha kwa anthu anzathu.

Pamene analimbikitsidwa kukhululukira munthu wina pa cholakwa chaching’ono, mkazi wina anati: “Palibe aliyense amene amayenerera zoyesayesa za kukhululukira.” Popanda kupendetsetsa ndemanga yotero ingaoneke kukhala yopanda chifundo, youma mtima, ngakhale yamwano. Komabe, titaipenda mwakuya timapeza kuti imavumbula kugwiritsidwa mwala kumene anthu ambiri amakhala nako pamene ayang’anizana ndi dziko limene amaona kukhala ladyera, losasamala, ndi laudani. Mwamuna wina anati: “Anthu amakudyera masuku pamutu pamene uwakhululukira. Amakuyesa ngati chosansira fumbi kumapazi.”

Pamenepa, mposadabwitsa kuti kukulitsa mkhalidwe wamaganizo wa kukhululukira kuli kovuta m’masiku ano otsiriza. Chikhalirechobe, Baibulo limatilimbikitsa kukhululukira mokoma mtima. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 2:7.) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala okhululukira?

[Mawu a M’munsi]

a Maina asinthidwa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena