Nkukhaliranji Wokhululukira?
KATSWIRI ndi mlembi Wachiyuda Joseph Jacobs panthaŵi ina anafotokoza kukhululukira kukhala “phunziro lapamwamba koposa ndi lovuta koposa pa maphunziro onse a makhalidwe.” Ndithudi, ambiri amaona mawuwo “Ndakukhululukira” kukhala ovuta kwambiri kunena.
Kukuoneka ngati kuti kukhululukira kuli kofanana ndi ndalama. Kungaperekedwe mwaufulu ndi mwachifundo kwa ena kapena munthu angangokusunga mwadyera kwa iye mwini. Yoyambayo ndiyo njira yaumulungu. Tiyenera kukulitsa zizoloŵezi za kupereka mooloŵa manja ponena za kukhululukira. Chifukwa? Chifukwa chakuti Mulungu amalimbikitsa zimenezo, ndipo chifukwa chakuti mzimu wosakhululukira ndi wolipsira ungangoipitsirako zinthu.
Anthu ambiri amanena kuti: “Sindimakwiya; ndimangobwezera basi!” Momvetsa chisoni, umenewu ndiwo mkhalidwe wa anthu ambiri lerolino. Mwachitsanzo, mkazi wina anakana kulankhula ndi mlamu wake kwa zaka zoposa zisanu ndi ziŵiri chifukwa chakuti, “anandilakwira kwambiri ndipo sindinakhoze kumkhululukira,” anatero mkaziyo. Koma kunyalanyaza munthu kotero, kutagwiritsiridwa ntchito monga njira youmirizira wamlanduyo kupepesa kapena monga chida chomlangira, kaŵirikaŵiri sikumakhutiritsa chikhumbo cha kubwezera. Mmalomwake, kungangotalikitsa mkanganowo, kukumalola udani waukulu kubuka. Ngati mkwiyo umenewo suthetsedwa, kulamuliridwa mwamphamvu ndi mzimu wa kulipsira kungawononge maunansi ndipo ngakhale thanzi la munthuwe.
Ngozi ya Mzimu wa Kusakhululukira
Pamene munthu ali wosakhululukira, mkangano umene umabuka umadzetsa kupsinjika. Kupsinjika nakonso kungayambitse matenda aakulu. Dr. William S. Sadler analemba kuti: “Palibe munthu aliyense amene angamvetsetse mokwanira monga dokotala chiŵerengero chachikulu chodabwitsa cha matenda ndi mavuto a anthu amene amachititsidwa mwachindunji ndi nkhaŵa, mantha, mikangano, . . . kulingalira zosayenera ndi kakhalidwe koipa.” Komabe, kodi ndi kuvulaza kwakukulu motani kumene kupsinjika mtima kumachititsa kwenikweni? Buku lina la zamankhwala likuyankha motere: “Ziŵerengero . . . zinasonyeza kuti aŵiri a magawo atatu a odwala amene anapita kwa dokotala anali ndi zizindikiro za matenda zochititsidwa kapena zokulitsidwa ndi kupsinjika maganizo.”
Inde, kupwetekedwa mtima, mkwiyo, ndi njiru zilidi zovulaza. Mikhalidwe ya mtima yosakaza imeneyi ili ngati dzimbiri limene pang’onopang’ono limadya chithupi cha galimoto. Kunja kwa galimoto kungaoneke kokongola, koma mkati mwa utoto mungakhale mukudyeka.
Ndipo zowopsa kwambiri zili zakuti, kukana kwathu kukhululukira pamene pali maziko a chifundo nakonso kungativulaze mwauzimu. Kwa Yehova Mulungu, tingakhale ngati kapolo wa m’fanizo la Yesu. Kapoloyo anakhululukidwa mangawa ake ochuluka ndi mbuye wake. Komabe, pamene kapolo mnzake anachonderera kuti amkhululukire mangawa aang’ono poyerekezera ndi ake, iye anachita nkhanza ndipo sanakhululukire. Yesu anamveketsa bwino lomwe kuti ngati ife mofananamo sitifuna kukhululukira, Yehova adzakana kutikhululukira machimo athu. (Mateyu 18:21-35) Chotero, ngati sitili okhululukira tingataye chikumbumtima chathu choyera pamaso pa Mulungu ndipo ngakhale chiyembekezo chathu cha mtsogolo! (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 1:3.) Pamenepa, kodi nchiyani chimene tingachite?
Phunzirani Kukhululukira
Kukhululukira kwenikweni kumachokera mumtima. Kumaphatikizapo kukhululuka cholakwa cha wochimwayo ndi kuchotsa chikhumbo chilichonse cha kubwezera. Motero, chiweruzo chomalizira ndi kubwezera kumene kungakhalepo zimasiyidwa m’manja mwa Yehova.—Aroma 12:19.
Komabe, tiyenera kuzindikira kuti popeza kuti “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika,” sumafuna kukhululukira nthaŵi zonse ngakhale pamene uyenera kutero. (Yeremiya 17:9) Yesu mwiniyo anati: “Mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano.”—Mateyu 15:19.
Ubwino wake ngwakuti, mtima wathu ungaphunzitsidwe kuchita choyenera. Komabe, maphunziro amene tifunikira ayenera kuchokera kumagwero apamwamba. Sitingachite zimenezo mwa ife tokha. (Yeremiya 10:23) Wamasalmo wouziridwa mwaumulungu anazindikira zimenezi napempherera chitsogozo cha Mulungu. Iye anachonderera Yehova m’pemphero kuti: “Mundiphunzitse malemba anu. Mundizindikiritse njira ya malangizo anu.”—Salmo 119:26, 27.
Malinga ndi kunena kwa salmo lina, Mfumu Davide wa Israyeli wakale anafika pa ‘kuzindikira njira’ ya Yehova. Iye anayendamo ndipo anaphunziramo kanthu. Chifukwa chake, anakhoza kunena kuti: “Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuwopa Iye.”—Salmo 103:8, 13.
Tifunikira kuphunzira monga momwe Davide anachitira. Kuphunzira mwapemphero chitsanzo changwiro cha Mulungu cha kukhululukira, limodzinso ndi chija cha Mwana wake. Motero, tingaphunzire kukhululukira kuchokera mumtima.
Komabe, ena angafunsebe kuti: Bwanji ponena za machimo aakulu? Kodi machimo onse ayenera kukhululukidwa?
Kupeza Uchikatikati
Pamene munthu walakwiridwa kwakukulu, kupweteka mtima kungakhale kwakukulu. Zimenezi zimakhala choncho makamaka ngati munthuyo alibe liwongo lililonse. Ena angadabwedi kuti, ‘Kodi ndingakhululukire bwanji munthu amene anandilakwira kwambiri ndi kundikhumudwitsa?’ Ponena za tchimo lalikulu limene lingafune kuchotsedwa kwa munthuyo, wolakwiridwayo afunikira kugwiritsira ntchito uphungu wa pa Mateyu 18:15-17.
Mulimonse mmene zingakhalire, zambiri zimadalira pa wochimwayo. Kuyambira pamene analakwa kodi wasonyeza chizindikiro chilichonse cha kulapa koona? Kodi wochimwayo wasintha, mwinamwake ngakhale kuyesa kuwongoleradi zinthu? Kwa Yehova kulapa koteroko ndiko maziko a kukhululukira ngakhale pamene machimo owopsadi achitidwa. Mwachitsanzo, Yehova anakhululukira Manase, mmodzi wa mafumu oipitsitsa m’mbiri ya Israyeli. Pamaziko otani? Mulungu anachita zimenezo chifukwa chakuti Manase pomalizira pake anadzichepetsa nalapa pa njira zake zonyansa.—2 Mbiri 33:12, 13.
M’Baibulo kulapa kwenikweni kumaphatikizapo kusintha koona kwa mkhalidwe wa maganizo, chisoni chochokera mumtima kaamba ka zolakwa zilizonse zimene zinachitidwa. Pamene kuli koyenerera ndi kotheka, kulapa kumatsagana ndi zoyesayesa za kupereka malipo kwa wochimwiridwayo. (Luka 19:7-10; 2 Akorinto 7:11) Pamene palibe kulapa kotero, Yehova samakhululukira.a Ndiponso, Mulungu samayembekezera Akristu kukhululukira awo amene kale anali ounikiridwa mwauzimu koma amene tsopano mwadala, akuchita machimo mosalapa. (Ahebri 10:26-31) M’zochitika zonyanyitsa, kukhululukira kungakhale kosayenerera konse.—Salmo 139:21, 22; Ezekieli 18:30-32.
Kaya kukhululukirako kuli kotheka kapena ayi, wochitiridwa tchimo lalikuluyo angafunikire kulingalira funso lina: Kodi ndiyenera kumavutikabe mtima kwambiri, kukhala wokhumudwa kwambiri ndi wokwiya, kufikira nkhaniyo itathetsedwa yonse? Talingalirani chitsanzo china. Mfumu Davide inakhumudwa kwambiri pamene kazembe wake, Yoabu, anapha Abineri ndi Amasa, “anthu aŵiri olungama ndi okoma oposa [Yoabu].” (1 Mafumu 2:32) Davide anasonyeza mkwiyo wake mwamawu ndipo mosakayikira m’pemphero kwa Yehova. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, kupwetekedwa mtima kwakukulu kwa Davide kuyenera kuti kunazirala. Sanalamuliridwe ndi mkwiyo kufikira mapeto a moyo wake. Ndipo Davide anapitirizabe kugwira ntchito ndi Yoabu, koma sanangokhululukira wakupha wosalapa ameneyu. Davide anatsimikizira kuti chiweruzo chinaperekedwa pomalizira pake.—2 Samueli 3:28-39; 1 Mafumu 2:5, 6.
Kungatenge nthaŵi yaitali ndi kuyesayesa kuti awo okhumudwa ndi machimo aakulu a ena aleke mkwiyo wawo wapoyamba. Kuchira kungakhale kosavutirapo pamene wochimwayo avomereza cholakwa chake nalapa. Komabe, wochimwiridwayo ayenera kupeza chitonthozo ndi chisangalalo m’chidziŵitso chake cha chilungamo ndi nzeru za Yehova ndi mumpingo Wachikristu, mosasamala kanthu za njira ya wochimwayo.
Ndiponso, zindikirani kuti pamene mukhululukira wochimwayo, zimenezo sizikutanthauza kuti mukulekerera tchimolo. Kwa Mkristu, kukhululukira kumatanthauza kusiya nkhaniyo mwachidaliro m’manja mwa Yehova. Iye ali Woweruza wolungama wa chilengedwe chonse, ndipo adzapereka chiweruzo panthaŵi yake. Zimenezo zidzaphatikizapo kuweruza “adama ndi achigololo” onyenga.—Ahebri 13:4.
Mapindu a Kukhululukira
Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.” (Salmo 86:5) Kodi inu, mofanana ndi Yehova, muli “wokhululukira”? Mapindu ake ngambiri.
Loyamba, kukhululukira ena kumachirikiza maunansi abwino. Baibulo limafulumiza Akristu kuti: “Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.”—Aefeso 4:32.
Lachiŵiri, kukhululukira kumadzetsa mtendere. Umenewu suli chabe mtendere ndi anthu anzathu komanso mtendere wamaganizo.—Aroma 14:19; Akolose 3:13-15.
Lachitatu, kukhululukira ena kumatithandiza kukumbukira kuti ife enife tifunikira kukhululukiridwa. Inde, “onse anachimwa, napereŵera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.
Lotsirizira, kukhululukira ena kumalambula njira yakuti machimo athu akhululukidwe ndi Mulungu. Yesu anati: “Ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.”—Mateyu 6:14.
Talingalirani zinthu zochuluka zimene zingakhale zinali m’maganizo mwa Yesu patsiku la imfa yake. Anali wodera nkhaŵa za ophunzira ake, ntchito yolalikira, ndipo makamaka umphumphu wake kwa Yehova. Komabe, ngakhale pamene anali kuvutika kwambiri pamtengo wozunzirapo, kodi iye analankhula za chiyani? Ena a mawu ake omalizira anali akuti, “Atate, muwakhululukire iwo.” (Luka 23:34) Tingatsanzire chitsanzo changwiro cha Yesu mwa kukhululukirana kuchokera mumtima.
[Mawu a M’munsi]
a Komabe, Yehova amalingalira zinthu zina pofuna kukhululukira. Mwachitsanzo, ngati wolakwayo sadziŵa za miyezo ya Mulungu, kusadziŵako kungachepetse ukulu wa liwongo. Pamene Yesu anapempha Atate wake kukhululukira awo amene anali kumupha, Yesu mwachionekere anali kulankhula za asilikali Achiroma amene anamupha. Iwo ‘sanadziŵe chimene anali kuchita,’ pokhala osadziŵa za amene iye anali kwenikweni. Komabe, atsogoleri achipembedzo amene anali kusonkhezera kunyongako anali ndi liwongo lalikulu kwambiri—ndipo ambiri a iwo sanakhululukiridwe.—Yohane 11:45-53; yerekezerani ndi Machitidwe 17:30.
[Zithunzi patsamba 5]
Kodi mwaona mfundo ya fanizo la Yesu la kapolo wosakhululukira?
[Zithunzi patsamba 7]
Kukhululukira ena kumachirikiza maunansi abwino ndipo kumadzetsa chimwemwe