‘Musalire Monga Otsalawo’
KODI munayamba mwaonapo mmene duŵa limazyolikira litakanthidwa ndi mvula yamkuntho wamphamvu? Zimenezo zingakhale zomvetsa chisoni. Ndi iko komwe, mwachionekere chimvulacho chinathamangitsa zinyama ndi anthu ochuluka—zolengedwa zamphamvu kuposa duŵa lililonse—kukapeza pobisalira. Komabe, duŵalo linachirimika pamenepo, lozika mizu yake, likumalimbana ndi mphepo yamphamvuyo. Tsopano, lidakali chikhalire pamenepo, lozyolika inde koma losathyoka, likumasonyeza nyonga yosiyana ndi kaonekedwe kake kosalimba. Mungazizwe pamene mukulikhumbira, ngati ilo lidzapezanso mphamvu yake ndi kutukula mutu wake wokongolawo ndi kupenyanso kumwamba.
Anthu alinso motero. M’nthaŵi zovuta zino, timayang’anizana ndi mikuntho yosiyanasiyana. Mavuto a zachuma, tondovi, kudwala, kutaya wokondedwa mu imfa—anamondwe oterowo amatikantha tonsefe panthaŵi ndi nthaŵi, ndipo nthaŵi zina sitimatha kuwathaŵa monga momwe duŵa silingadzizulire lokha ndi kukabisala. Nkochititsa chidwi kuona anthu amene amaonekera kukhala osalimba akumasonyeza nyonga ndi kupirira mikuntho yoteroyo. Kodi iwo amakhoza motani? Kaŵirikaŵiri mankhwala ake amakhala chikhulupiriro. Yakobo, mbale wa Yesu Kristu wa atate wina, analemba kuti: “Mudziŵa kuti pamene chikhulupiriro chanu chipambana poyang’anizana ndi mayesero, chotulukapo ndicho nyonga ya kupirira.”—Yakobo 1:3, Today’s English Version.
Mankhwala ena ndiwo chiyembekezo. Mwachitsanzo, pamene imfa ikantha wokondedwa, chiyembekezo chingathandize kwambiri awo otsala ndi moyo. Mtumwi Paulo analembera Akristu a ku Tesalonika kuti: “Sitifuna, abale, kuti mukhale osadziŵa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.” (1 Atesalonika 4:13) Pamene kuli kwakuti Akristu mosakayikira amalira maliro, pali kusiyana. Iwo ali ndi chidziŵitso cholongosoka ponena za mkhalidwe wa akufa ndi ponena za chiyembekezo cha chiukiriro.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Chidziŵitso chimenechi chimawapatsa chiyembekezo. Ndipo chiyembekezo chimenechonso, pang’onopang’ono chimachepetsa chisoni chawo. Chimawathandiza kupirira, ndi zina zowonjezereka. M’kupita kwanthaŵi, mofanana ndi duŵa lija pambuyo pa mvula yamkuntho, angatukule mitu yawo kuchokera m’chisoni ndi kupezanso chisangalalo ndi chikhutiro m’moyo.