Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Pamene Hava, ndiyeno pambuyo pake Adamu, anadya chipatso cha mtengo wa kudziŵitsa zabwino ndi zoipa, kodi linali apulo limene anadya?
Sitikudziŵa. Anthu ambiri alingalira kuti ‘chipatso choletsedwacho’ chinali apulo, ndipo kwa zaka mazana ambiri aluso la kujambula kaŵirikaŵiri asonyeza zimenezo. Koma Baibulo silimatchula mtengo kapena chipatso chake. Hava anangotchula kuti “zipatso za mtengo umene uli mkati mwa munda.”—Genesis 3:3.
Chokondweretsa pankhaniyi ndicho nkhani yakuti “Apple” yopezeka mu Insight on the Scriptures imene imati:
“Pali malingaliro osiyanasiyana kwambiri ponena za mtundu wa mtengo ndi chipatso zotanthauzidwa ndi liwu Lachihebri lakuti tap·puʹach. Liwuli mwa ilo lokha limatanthauza chinthu chodziŵika ndi kununkhira kwake, kapena fungo. Limachokera ku liwu lakuti na·phachʹ, lotanthauza ‘kuuzira; kupuma ŵefuŵefu; kuchita befu.’ (Gen 2:7; Yobu 31:39; Yer 15:9) Pazimenezi, M. C. Fisher analemba kuti: ‘Mgwirizano [ndi na·phachʹ] poyamba umaoneka kukhala wokanikana, koma malingaliro a “kupuma” ndi “kutulutsa fungo” ali ogwirizana. Liwu lake lofanana lakuti puah limatanthauza zonse ziŵiri “kuuzira” (kwa mpweya) ndi “kutulutsa fungo lokoma, kununkhira.”’—Theological Wordbook of the Old Testament, lokonzedwa ndi R. L. Harris, 1980, Vol. 2, tsa. 586.
“Zipatso zina zingapo zalingaliridwa m’malo mwa apulo, kuphatikizapo lalanje, citron, quince, ndi apricot. . . . Komabe, liwu lofanana nalo la Chiarabu lakuti tuffah kwakukulukulu limatanthuauza ‘apulo,’ ndipo nkodziŵika kuti maina amalo Achihebri akuti Tappuah ndi Beth-tappuah (mwinamwake otchedwa motero chifukwa cha kufala kwa chipatso chimenechi m’malowo) asungidwa ndi mawu ofanana nawo Achiarabu mwa kugwiritsira ntchito liwu limeneli. (Yos 12:17; 15:34, 53; 16:8; 17:8) Malo ameneŵa sanali kuzidikha koma kumtunda, kumene mkhalidwe wa mphepo kwakukulukulu umakhala wofundirapo. Ndiponso, kuthekera kwa kusiyanasiyana kwa mkhalidwe wa mphepo m’nthaŵi zakale sikunganyalanyazidwe. Mitengo ya maapulo imakula mu Israel lerolino motero ikuonekera kukhala ikuyenera bwino lomwe malongosoledwe a Baibulo. William Thomson, yemwe anathera zaka zambiri mu Syria ndi Palestine m’zaka za zana lapitalo, anasimbadi kuti anapeza minda ya maapulo m’malo a Ashkelon pa Zidikha za Philistia.—The Land and the Book, lokonzedwanso ndi J. Grande, 1910, mas. 545, 546.
“Mtengo wa maapulo (Pyrus malus) ukutchulidwa makamaka mu Nyimbo ya Solomo, mmene mawu a chikondi a mnyamata wa Msulami akufaniziridwa ndi mthunzi wokoma wa mtengo wa maapulo ndi kutsekemera kwa chipatso chake. (Nyi 2:3, 5) Ndiyenonso, akuyerekezera mpweya wa mtsikanayo ndi kununkhira kwa maapulo. (Nyi 7:8; onaninso 8:5.) M’Miyambo (25:11) malankhulidwe oyenera ndi apanthaŵi yake amafanizidwa ndi ‘maapulo a golidi m’zotengera za siliva.’ Malo ena okha pamene apulo likutchulidwa ndi pa Yoweli 1:12. Chikhulupiriro chamwambo chofala chonena za apulo kukhala chipatso choletsedwa mu Edene chilibe maziko alionse a Malemba. Mofananamo, mawu akuti ‘apulo la diso’ akupezedwa mu King James Version (Sal 17:8; Miy 7:2; ndi malemba ena) koma sali mawu Achihebri, matembenuzidwe achindunji akumakhala ‘mwana wa diso [la munthu].’”—Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, masamba 131-2, lofalitsidwa mu 1988 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.