Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 1/1 tsamba 3-4
  • Sungani Umphumphu ndi Kukhala ndi Moyo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sungani Umphumphu ndi Kukhala ndi Moyo!
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Pitirizani Kukhala ndi Mtima Wosagawanika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Tidzayenda Mogwirizana Ndi Mtima Wathu Wosagawanika
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yobu Analemekeza Dzina la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Mudzakhalabe Wokhulupirika?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 1/1 tsamba 3-4

Sungani Umphumphu ndi Kukhala ndi Moyo!

“CHITIRA Mulungu mwano, ufe”! Chikuto cha magazini athu chikusonyeza mkazi wa Yobu, amene anaukira iye ndi mawu amenewo. Zimenezo zinachitika pafupifupi zaka 3,600 zapitazo. Komabe, kuukiridwa kumeneko kwa mtumiki wokhulupirika wa Mulungu kumasonyeza nkhani imene mtundu wa anthu wayang’anizana nayo kufikira lerolino. Yobu wokhulupirikayo anatayikidwa kwakukulu​—zifuyo zake, nyumba yake, ana ake khumi. Tsopano thupi lake linali pa ululu wa nthenda yozunza, ikumamuyesa kufikira pogomera chipiriro. Chifukwa? Mdani wamkulu wa Mulungu ndi munthu, Satana Mdyerekezi, anali kupereka chitokoso chakuti munthu sangathe kusunga umphumphu kwa Mulungu pamene ali pachiyeso chachikulu.​—Yobu 1:11, 12; 2:4, 5, 9, 10.

Lerolino, monga m’tsiku la Yobu, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (1 Yohane 5:19) Ndithudi, zimenezo nzoona kwenikweni lerolino, pakuti tsopano “wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse,” wagwetsedwa kuchokera kumwamba kudza padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:9) Zimenezi zimasonyeza chifukwa chake pali masoka aakulu amene akuvutitsa mtundu wa anthu m’nthaŵi yathu. Nkhondo yadziko yoyamba, imene inaulika mu 1914, inasonyeza “zoŵaŵa zoyamba” zimene zapitirizabe kufikira mkati mwenimweni mwa zaka za zana la 20.​—Mateyu 24:7, 8.

M’dziko lino lankhanza ndi la mikhalidwe yoipa, kodi nthaŵi zina mumamva kuti mwafika pogomera chipiriro cha munthu? Kodi mumadabwa nthaŵi zina kuti, ‘Kodi pali chifuno chilichonse chokhalira moyo?’ Yobu angakhale atalingalira motero, koma sanataye konse chikhulupiriro chake mwa Mulungu, ngakhale kuti anachita zolakwa. Iye anasonyeza kutsimikiza mtima kwake m’mawu awa: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.” Iye anali ndi chidaliro chakuti Mulungu ‘akadziŵa ungwiro wake.’​—Yobu 27:5; 31:6.

Yesu Kristu, Mwana wakewake wa Mulungu, nayenso anapirira mayesero pamene anali pano padziko lapansi. Satana anaukira Yesu m’njira zosiyanasiyana. Iye anapezera mwaŵi pa zosoŵa zakuthupi za Yesu ndi kuyesa chidaliro Chake cha pa Mawu a Mulungu, monga momwe zinachitikira pa phiri lomuyesera. (Mateyu 4:1-11) Iye anazunza Yesu mwa kuchititsa alembi ndi Afarisi ampatukowo ndi anthu onyengedwa ndi iwo kumuzunza, kumneneza kukhala wamwano, ndi kulinganiza chiwembu cha kumupha. (Luka 5:21; Yohane 5:16-18; 10:36-39; 11:57) Iwo anachita zoipa kwambiri kwa Yesu koposa zimene otonthoza onyenga atatu aja anachita kwa Yobu.​—Yobu 16:2; 19:1, 2.

M’munda wa Getsemane, pamene Yesu anayandikira chimake cha chiyeso chimenechi, iye anauza ophunzira ake kuti: “Moyo wanga uli wozingidwa ndi chisoni cha kufika nacho kuimfa.” Pamenepo, “nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate, ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire ine; koma si monga ndifuna ine, koma Inu.” Potsirizira pake, pamtengo wozunzirapo, mwa kukwaniritsa mawu aulosi a Salmo 22:1, Yesu anafuula nati: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” Koma kwenikweni, Mulungu sanamsiye Yesu chifukwa chakuti Yesuyo anasungabe umphumphu wake wangwiro kwa Iye, akumapereka chitsanzo kwa Akristu oona onse choti achitsatire. Yehova anafupa kusunga umphumphu kwa Yesu mwa kumuukitsa ndi kumkweza kumiyamba yokwezeka kwenikweni. (Mateyu 26:38, 39; 27:46; Machitidwe 2:32-36; 5:30; 1 Petro 2:21) Mulungu adzafupa ena onse amene amasunga umphumphu kwa iye mofananamo.

Umphumphu wa Yesu sunangopereka yankho lokwanira lokha ku chitokoso cha Satana komanso nsembe ya moyo wake waumunthu wangwiro inapereka dipo, pamaziko amene anthu osunga umphumphu angapezere moyo wosatha. (Mateyu 20:28) Choyamba, Yesu akusonkhanitsa “kagulu ka nkhosa” ka odzozedwa omwe akukhala oloŵa nyumba ndi iye mu Ufumu wa kumwamba. (Luka 12:32) Pambuyo pa zimenezi, “khamu lalikulu” likusonkhanitsidwa kuti lipulumuke “chisautso chachikulu,” akumatulukamo kuti alandire moyo wosatha mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu padziko lapansi.​—Chivumbulutso 7:9, 14-17.

Yobu wosunga umphumphuyo adzakhala pakati pa mamiliyoni zikwizikwi za akufa omwe adzaukitsidwa panthaŵiyo kukhala mbali ya chitaganya chamtendere cha “dziko latsopano.” (2 Petro 3:13; Yohane 5:28, 29) Monga momwe kwasonyezedwera kumbuyo kwa magazini athu, umphumphu unali ndi mphotho yake m’tsiku la Yobu pamene Yehova “anadalitsa chitsiriziro cha Yobu koposa chiyambi chake.” Iye anali atapeza nyonga yauzimu monga amene “sanachimwa ndi milomo yake.” Mulungu anatalikitsa moyo wake ndi zaka zina 140. Ponena za chuma, iye anapatsa Yobu zonse zimene anali nazo poyamba moŵirikiza kaŵiri, ndipo Yobu “anali nawonso ana amuna asanu ndi aŵiri ndi ana akazi atatu,” ana aakazi analingaliridwa kukhala okongola koposa m’dziko lonselo. (Yobu 2:10; 42:12-17) Koma kulemera konseku kunali chabe kulaŵa madalitso amene osunga umphumphu adzasangalala nawo m’Paradaiso wa “dziko latsopano.” Nanunso mungagaŵanemo m’chisangalalo chimenecho, monga momwe masamba otsatira adzalongosolera!

[Chithunzi patsamba 4]

Yesu anapereka chitsanzo changwiro monga wosunga umphumphu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena