Kumlaka Satana ndi Ntchito Zake
“Mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.”—YAKOBO 4:7.
1. Kodi ndimotani mmene “dzanja la woipa” layambukirira mtundu wa anthu lerolino?
YOBU molondola anati: “Dziko lapansi laperekedwa m’dzanja la woipa.” (Yobu 9:24) Ndipo tsopano tikuyang’anizana ndi nthaŵi zoŵaŵitsa koposa m’mbiri yonse ya anthu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ano ali “masiku otsiriza” a ulamuliro wauchiŵanda wa Satana pa dziko lapansi. Nchifukwa chake, mosonkhezeredwa ndi Satana, ‘anthu oipa ndi onyenga akuipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.’ (2 Timoteo 3:1, 13) Ndiponso, zizunzo, chisalungamo, nkhanza, upandu, mavuto azachuma, matenda alizunzo, zoŵaŵa za ukalamba, kupsinjika mtima—izi ndi zinthu zina zambiri zingatiyambukire moipa.
2. Kodi tingalimbane nazo motani ziukiro za Satana lerolino?
2 Mdani wamkulu, Satana Mdyerekezi, akuukira zolimba mtundu wa anthu ndipo makamaka olambira oona a Mulungu. Cholinga chake ndicho kuchititsa anthu okhoza kusunga umphumphu onse kupandukira Mulungu ndi kuwatsogolera ku chiwonongeko pamodzi naye ndi angelo ake auchiŵanda. Komabe, tapatsidwa chitsimikizo chakuti ngati tipirira ndi umphumphu wathu, Mdyerekezi adzatithaŵa. Monga Yesu, ‘tingaphunzire kumvera’ Mulungu mwa zinthu zimene tivutika nazo, ndipo mwa chisomo cha Iye mwini, tingapeze moyo wosatha.—Ahebri 5:7, 8; Yakobo 4:7; 1 Petro 5:8-10.
3, 4. (a) Kodi ndi ziyeso zakunja zotani zimene Paulo analimbana nazo? (b) Kodi nkhaŵa ya Paulo monga mkulu Wachikristu inali yotani?
3 Mtumwi Paulo nayenso anayesedwa m’njira zambiri. Potchula maumboni ake a kukhala mtumiki wa Kristu, iye analemba kuti: “Makamaka ine; m’zivutitso mochulukira, m’ndende mochulukira, m’mikwingwirima mosaŵerengeka, muimfa kaŵirikaŵiri. Kwa Ayuda ndinalandira kasanu mikwingwirima makumi anayi kupereŵera umodzi. Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka chombo, ndinakhala m’kuya tsiku limodzi usana ndi usiku; paulendo kaŵirikaŵiri, mowopsa mwake mwa mitsinje, mowopsa mwake mwa olanda, mowopsa modzera kwa mtundu wanga, mowopsa modzera kwa amitundu, mowopsa m’mudzi, mowopsa m’chipululu, mowopsa m’nyanja, mowopsa mwa abale onyenga; m’chivutitso ndi m’cholemetsa, m’madikiro kaŵirikaŵiri, m’njala ndi ludzu, m’masalo a chakudya kaŵirikaŵiri, m’chisanu ndi umaliseche.
4 “Popanda za kunjazo pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, ch[i]labadiro cha mipingo yonse. Afooka ndani wosafooka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?” (2 Akorinto 11:23-29) Chotero, Paulo anasunga umphumphu poyang’anizana ndi zizunzo ndi ziyeso zochokera kunja, ndipo pokhala mkulu Wachikristu, nkhaŵa yake yaikulu inali ya kulimbikitsa abale ndi alongo ofookerapo mumpingo, kuwathandiza kusunga umphumphu. Ha, anali chitsanzo chabwino chotani nanga kwa akulu Achikristu lerolino!
Kusunga Umphumphu Pozunzidwa
5. Kodi yankho la chizunzo chachindunji nlotani?
5 Kodi ndi zida ziti zimene Satana amagwiritsira ntchito kuswera umphumphu? Monga momwe taonera pamwambapo, ena a machenjera oipitsitsa a Satana ndiwo chizunzo chachindunji, koma yankho lake lilipo. Aefeso 6:10, 11 amatilangiza kuti: “Tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m’kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.”
6. Kodi kungasonyezedwe motani kuti Mboni za Yehova ‘zalakatu’?
6 M’masiku ano otsiriza, Mboni za Yehova zakhala zikulimbana ndi ziyeso nthaŵi zambiri. Chotero, tinganene mogwirizana ndi Paulo kuti: “M’zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.” (Aroma 8:37) Zimenezi zikutsimikiziridwa ndi mbiri ya umphumphu wa Mboni za Yehova m’misasa yachibalo ya Germany, Austria, Poland, ndi Yugoslavia m’nyengo ya Nazi pakati pa 1933 ndi 1945, mkati mwa kupondereza kwa Chikomyunizimu ku Eastern Europe pakati pa 1945 ndi 1989, ndi mkati mwa zizunzo zimene zakantha madera ena a Afirika ndi Latin America posachedwapa.
7. Kodi ndi zitsanzo ziti zolimbikitsa za kusunga umphumphu zimene zikusimbidwa kuchokera ku Ethiopia?
7 Mboni za Yehova za ku Ethiopia zinapereka chitsanzo chosonkhezera kwambiri cha kusunga umphumphu pakati pa 1974 ndi 1991. Wina wa osunga ndende otengeka maganizo ndi ndale anauza mbale womangidwa kuti: “Kulipo bwino kumasula mikango mosungiramo zinyama kuposa kumasulanso anthu inu!” Ozunza ankhanza ameneŵa anazunza atumiki a Yehova, ndipo patapita zaka zingapo bwalo la milandu la apilo linalamula kuti anyongedwe. Mtembo wa mbale wina unaikidwa poyera monga chenjezo kwa ena. Abale ena amene anachitira apilo chiweruzo cha imfa anamasulidwa ndi bwalo la milandu lachifundo, ndipo ena a ‘olakika’ okhulupirika ameneŵa anali m’programu pa Msonkhano Wachigawo wa “Chiphunzitso Chaumulungu” ku Addis Ababa kuchiyambi kwa 1994.a—Yohane 16:33; yerekezerani ndi 1 Akorinto 4:9.
8. Kodi ndimotani mmene Satana wayesera kudyerera pa “kuyeretsa fuko”?
8 Satana walephera kuswa umphumphu wa abale ndi alongo okhulupirika amenewo mwa kuukira kwachindunji. Chotero, kodi ndi machenjera ati ena amene amagwiritsira ntchito? Chivumbulutso 12:12 chimafotokoza masiku ano otsiriza motere: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” Pokhala atalephera kufafaniza anthu a Mulungu okhulupirika kupyolera m’zizunzo, iye mumkwiyo wake amayesa kupululutsa anthu onse, mosakayikira ndi cholinga cha kuwonongera anthu a Yehova pamodzi ndi ena onse. Nchifukwa chake kotchedwa kuyeretsa fuko kwachitidwa m’madera ena a Yugoslavia wakale, ndipo pakhala zoyesayesa za kupha fuko lonse ku Liberia, Burundi, ndi Rwanda.
9. Kodi chifukwa ninji machenjera a Satana amalephera kaŵirikaŵiri? Perekani zitsanzo.
9 Koma kaŵirikaŵiri, machenjera a Satana amambwererera iye mwini, pakuti nsautso yausatana imachititsa anthu oona mtima kuona kuti chiyembekezo chawo chokha ndicho Ufumu wa Mulungu, wolengezedwa mwachangu ndi Mboni za Yehova. (Mateyu 12:21) Ndithudi, okondwerera akupita muunyinji wawo ku Ufumuwo! Mwachitsanzo, m’maiko osakazidwa ndi nkhondo a Bosnia ndi Herzegovina, anthu 1,307 anapezeka pa phwando la Chikumbutso cha imfa ya Yesu pa March 26, 1994, kuposa chaka chapapitapo ndi 291. Ziŵerengero zapamwamba koposa za opezekapo zinali motere, Sarajevo (414), Zenica (223), Tuzla (339), Banja Luka (255), ndi matauni ena. M’Croatia wapafupi munali chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha opezekapo 8,326. Chiwawa chimene chikuchitika mowazinga sichinaletse Mboni za Yehova m’maikowo kumvera lamulo la ‘kulalikira imfa ya Ambuye kufikira akadza iye.’—1 Akorinto 11:26.
M’Rwanda Wosakazikidwa ndi Nkhondo
10, 11. (a) Kodi nchiyani chimene chachitika m’dziko la Rwanda lotchedwa Lachikristu? (b) Kodi ndimotani mmene amishonale okhulupirika afotokozera malingaliro awo?
10 Mu 1993, Rwanda, wokhala ndi olengeza Ufumu 2,080, anali ndi opezeka pa Msonkhano Wachigawo wa “Chiphunzitso Chaumulungu” 4,075, ndi obatizidwa 230. Mwa ameneŵa, 142 anafunsira panthaŵi yomweyo utumiki waupainiya wothandiza. Maphunziro a Baibulo apanyumba anawonjezereka kufika pa 7,655 mu 1994—mwachionekere Satana sanakondwere nazo zimenezi! Ngakhale kuti unyinji wa anthu amanena kuti ali Akristu, kuphana kwa mafuko kunabuka. L’Osservatore Romano ya Vatican inavomereza kuti: “Kumeneku ndi kupululutsana kwenikweni kwa mafuko, kumene mwatsoka ngakhale Akatolika omwe alimo ndi mbali.” Amuna, akazi, ndi ana pafupifupi theka la miliyoni anafa, ndipo pafupifupi mamiliyoni aŵiri anakakamizika kuthaŵa. Zikumasunga uchete wawo Wachikristu wopanda chiwawa, Mboni za Yehova zinakhala pamodzi. Mazana a abale ndi alongo athu anaphedwa. Koma mumpingo umodzi wa ofalitsa Ufumu 65, mmene 13 anaphedwa, opezeka pamsonkhano anawonjezereka kufika pa 170 pofika mu August wa 1994. Mitokoma yachithandizo yochokera kwa Mboni za m’maiko ena inali pakati pa zinthu zoyamba kufika. Tikupereka mapemphero athu m’malo mwa otsala.—Aroma 12:12; 2 Atesalonika 3:1, 2; Ahebri 10:23-25.
11 Pakati pa mkhalidwe wowopsa umenewo, amishonale atatu amene anali m’Rwanda anapulumuka. Iwo akulemba kuti: “Tikudziŵa kuti abale athu kuzungulira padziko lonse akumana ndi mikhalidwe yofanana ndi imeneyi kapena yoipirapo, ndipo tikudziŵa kuti zimenezi zili mbali ya chizindikiro cha masiku otsiriza a dongosolo loipali. Chikhalirechobe, pamene zinthuzi zakugwera, zimakuchititsa kudziŵa mmene zinthu zilili ndi kuzindikira kufunika kwa moyo. Kwa ife malemba ena akhala ndi tanthauzo lina latsopano, ndipo tikuyembekezera mwachidwi nthaŵi pamene zinthu zakale sizidzakumbukikanso. Pakali pano tiyenera kukhala otanganitsidwa mu utumiki wa Yehova.”
Achichepere Osunga Umphumphu
12, 13. (a) Kodi ndi njira yosunga umphumphu yotani imene wachichepere wina anatenga? (b) Kodi nkuti kumene achinyamata athu angapeze chilimbikitso lerolino?
12 Yesu anasonyeza kuti awo amene anakanidwa ndi ziŵalo za banja lawo chifukwa cha choonadi adzafupidwa “makumi khumi.” (Marko 10:29, 30) Ndimmene zinalili ndi Entellia, mtsikana wa zaka khumi kumpoto kwa Afirika, amene anakonda dzina la Mulungu—Yehova—atangolimva. Anaphunzira ndi Mboni za Yehova ndi kuyenda kwa mphindi 90 popita kumisonkhano ndi mphindi 90 pobwerako, ngakhale kuti banja lake lotsutsalo kaŵirikaŵiri linamtsekera kunja atabwerako. Pa usinkhu wa zaka 13, anayamba kulalikira kunyumba ndi nyumba, ndipo chitsutso cha banja chinakula. Tsiku lina achibale ake anammanga mikono ndi miyendo ndi kumgoneka padzuŵa loswa mtengo kwa maola asanu ndi aŵiri, akumamthira madzi akuda mobwerezabwereza. Iwo anammenya kowopsa, kumboola diso limodzi, ndipo potsirizira pake kumpitikitsa panyumba. Koma iye anapeza ntchito pachipatala ndipo m’kupita kwa nthaŵi anayenerera kukhala nesi. Pa usinkhu wa zaka 20, anabatizidwa nalembetsa pomwepo upainiya wothandiza. Pochita chidwi ndi umphumphu wake, banja lake lamlandiranso panyumba pawo, ndipo asanu ndi anayi mwa iwo alandira maphunziro a Baibulo apanyumba.
13 Entellia anapeza chilimbikitso chochuluka m’Salmo 116, makamaka mavesi 1-4, amene waŵerenga mobwerezabwereza: “Ndimkonda, popeza Yehova amamva mawu anga ndi kupempha kwanga. Popeza amanditcherera khutu lake, chifukwa chake ndidzaitanira Iye masiku anga onse. Zingwe za imfa zinandizinga, ndi zoŵaŵa za manda zinandigwira: ndinapeza nsautso ndi chisoni. Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova; ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.” Yehova amayankha mapemphero otero!
14. Kodi Mboni Zachipolishi zasonyeza motani umphumphu wapadera?
14 Monga m’tsiku la Yesu, Satana kaŵirikaŵiri wagwiritsira ntchito anthu otengeka maganizo ndi zachipembedzo kusonkhezera chizunzo—koma sanapambane. Chitsanzo chapadera ndi chija cha abale athu ku Poland, amene asimbidwa mu 1994 Yearbook of Jehovah’s Witnesses. Mikhalidwe inafunikiritsa ngakhale achichepere kusonyeza umphumphu wawo. Mu 1946 wachichepere wina wazaka 15 anauzidwa kuti: “Tangopanga chizindikiro cha mtanda cha Chikatolika. Ngati sutero mfuti ikulirira!” Chifukwa chosunga umphumphu, anakhwekhweretseredwa m’nkhalango, nazunzidwa kowopsa, ndi kuwomberedwa.—Yerekezerani ndi Mateyu 4:9, 10.
Machenjera Ena a Satana
15, 16. (a) Kodi kachitidwe kauchiŵanda ka Satana nkotani, ndipo tingamkanize motani? (b) Kodi nchifukwa ninji achichepere athu safunikira kugwa?
15 Kachitidwe kauchiŵanda ka Satana ndiko “kuwononga atalephera kulamulira”! Iye ali ndi nkhokwe ya zida zambiri zowopsa. Nchifukwa chake mtumwi Paulo akuchenjeza kuti: “Kulimbana kwathu sitilimbana nawo mwazi ndi thupi, komatu nawo maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a choipa m’zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachirimika.” (Aefeso 6:12, 13) Kukhumba zinthu zakuthupi, zosangulutsa ndi manenanena oluluza, nyimbo zausatana, chitsenderezo cha mabwenzi kusukulu, kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, ndi kuledzera—chilichonse mwa zimenezi chikhoza kuwononga miyoyo yathu. Chifukwa chake, mtumwiyo akupitiriza kulangiza kuti: “Koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.”—Aefeso 6:16.
16 Zimenezi zikuoneka kukhala zofunika kwambiri lerolino polingalira za nyimbo zachilendo zimene Satana wadzaza nazo dzikoli. Nyimbo zina nzogwirizana mwachindunji ndi Kulambira Satana. Lipoti lochokera ku ofesi ya sheriff wa San Diego County (U.S.A.) linati: “Tinali ndi konsati kuno kumene gulu loimba linasonkhezera achichepere 15,000 kuimba kuti ‘Natas’—ndiko kuti, Satana wotchulidwa chafutambuyo.” Kulambira Satana kwalongosoledwa kukhala dzenje limene achinyamata akugweramo “chifukwa chakuti akhala akupupulika ali othedwa nzeru, okwiya ndipo osungulumwa.” Achicheperenu amene muli mumpingo Wachikristu, simufunikira kugwa! Yehova amakupatsani chida chauzimu chimene sichingapyozedwe konse ndi mivi ya Satana.—Salmo 16:8, 9.
17. Kodi kupsinjika mtima kungalakidwe motani?
17 Mivi yoyaka moto ya Satana ili yolinganizidwa kusonkhezera mtima. Kupyolera m’zovuta za moyo, zonga matenda kapena kupsinjika mtima kwambiri, mdani wathu angachititse ena kudzimva opanda pake. Wina angalefuke chifukwa cha kulephera kuthera maola ochuluka mu utumiki wa Mulungu kapena chifukwa chophonya misonkhano ina ya mpingo. Chisamaliro chachikondi choperekedwa ndi akulu, abale ndi alongo ena okoma mtima chingathandize kulaka kupsinjika mtima kosautsa. Nthaŵi zonse kumbukirani kuti Yehova amakonda atumiki ake okhulupirika. (1 Yohane 4:16, 19) Salmo 55:22 limati: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”
18. Kodi ndi machenjera ati ausatana amene ena akulimbana nawo?
18 “Machenjerero” a Satana aonekera posachedwapa mumtundu winanso. M’maiko ena maganizo a achikulire ambiri aloŵereredwa ndi malingaliro osautsa opereka chithunzi chakuti iwo anachitiridwa nkhanza ndi timagulu tolambira Satana pamene anali ana. Kodi malingaliro amenewo amachokera kuti? Mosasamala kanthu za kufufuza kwambiri, zonena za anthu zimasiyana kwambiri. Ena amaona malingaliro amenewo monga zikumbukiro za zochitika zenizeni zakale, ena amawaona monga maloto chabe—mwinamwake ochititsidwa ndi machiritso osaoneka bwino—ndipo enanso amaganiza kuti kuli kuona zideruderu kochititsidwa ndi nkhanza yapaubwana.
19. (a) Kodi Yobu analimbana ndi malingaliro otani? (b) Kodi ndimotani mmene akulu angatsatirire chitsanzo cha Elihu?
19 Tifunikira kudziŵa kuti Yobu mtumiki wa Mulungu analimbana ndi “zolingirira” zimene Satana anapereka kupyolera mwa Elifazi ndi Zofari. (Yobu 4:13-18; 20:2, 3) Chotero Yobu anavutika ndi “chisoni,” chikumambwetukitsa ‘mawu osokera’ a “zowopsa” zosautsa maganizo ake. (Yobu 6:2-4; 30:15, 16) Elihu anamvetsera kwa Yobu mwakachetechete namthandizadi kuona njira ya yanzeru kwambiri imene Yehova amaoneramo zinthu. Mofananamo lerolino, akulu achifundo amasonyeza kuti amasamala ovutika mwa kusawonjezera ‘zosenza’ pa anthu otero. M’malo mwake, monga Elihu, iwo moleza mtima amamvetsera kwa iwo ndiyeno amagwiritsira ntchito mafuta otontholetsa a m’Mawu a Mulungu. (Yobu 33:1-3, 7; Yakobo 5:13-15) Chotero aliyense amene malingaliro ake akuvutika ndi zopsinja maganizo, zenizeni kapena zongolingalira, kapena amene ‘akuwopsezedwa ndi maloto, . . . ndi masomphenya’ monga Yobu, angapeze chitonthozo cha m’Malemba mumpingo.—Yobu 7:14; Yakobo 4:7.
20. Kodi ndimotani mmene Akristu amene akuvutika angathandizidwire kusunga mkhalidwe wawo wauzimu?
20 Panthaŵi ino Mkristu angakhale wotsimikizira kuti, mwa njira ina yake, Satana akuchititsa malingaliro oipa ameneŵa. Ngati ena mumpingo akuvutika m’njira imeneyi, angachite bwino kuona malingaliro owopsa amenewo monga zoyesayesa zachindunji za Satana za kukhwethemula mkhalidwe wawo wauzimu. Iwo akufunikira chichirikizo cha Malemba choleza mtima ndi chachifundo. Mwa kutembenukira kwa Yehova m’pemphero ndi mwa kupindula ndi kuŵeta kwauzimu, awo amene akusautsidwa adzapeza mphamvu yoposa yachibadwa. (Yesaya 32:2; 2 Akorinto 4:7, 8) Motero adzakhoza kupirira mokhulupirika ndi kukaniza malingaliro oipa ndi osokoneza kuyambukira mtendere wa mpingo. (Yakobo 3:17, 18) Inde, adzakhoza kukaniza Mdyerekezi, akumasonyeza mzimu umodzimodzi umene Yesu anasonyeza pamene anati: “Choka Satana.”—Mateyu 4:10; Yakobo 4:7.
21. Kodi Malemba amachenjeza motani za machenjera a Satana?
21 Tikudziŵa kuti cholinga cha Satana ndicho kuipitsa maganizo athu, monga momwe mtumwi Paulo anachenjezera pa 2 Akorinto 11:3 kuti: “Ndiwopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Kristu.” Kuwonongeka kwamakono kwa anthu onse, kapena chitaganya cha anthu otalikirana ndi Mulungu, kumatikumbutsa za kuipa kumene kunadzetsedwa ndi zimphona ‘Zogwetsa’ zachiwawa ndi zoipa za m’tsiku la Nowa. (Genesis 6:4, 12, 13, NW, mawu amtsinde; Luka 17:26) Chifukwa chake, nkosadabwitsa kuti Satana watenga njira zamachenjera ndi zongwala zotsanulira mkwiyo wake, makamaka pa anthu a Mulungu.—1 Petro 5:8; Chivumbulutso 12:17.
22. Pamene kudzakhala kulibenso Satana, kodi tingayembekezere madalitso otani?
22 Satana sakutchulidwa nkomwe m’machaputala omalizira a buku la Baibulo la Yobu. Chinenezo chake choipa chakuti anthu sangasunge umphumphu kwa Mulungu chinali chitatsimikiziridwa kukhala chabodza ndi umphumphu wa Yobu. Mofananamo, patsogolopa pamene “khamu lalikulu” la osunga umphumphu ‘likutuluka m’chisautso chachikulu,’ Satana adzaponyedwa m’phompho. Amuna ndi akazi achikhulupiriro, kuphatikizapo Yobu wokhulupirikayo, adzagwirizana ndi “khamu lalikulu” limenelo, kusangalala ndi madalitso a paradaiso, oposatu aja omwe Yobu anafupidwa nawo!—Chivumbulutso 7:9-17; 20:1-3, 11-13; Yobu 14:13.
[Mawu a M’munsi]
a Onani 1992 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, patsamba 177.
Mafunso Openda
◻ Kodi ndi zitsanzo zabwino ziti za umphumphu zimene Yobu, Yesu, ndi Paulo anapereka?
◻ Kodi osunga umphumphu amkaniza motani Satana?
◻ Kodi achinyamata angakanize motani machenjera a Satana?
◻ Kodi tingachitenji kuti tilimbane ndi machenjera ausatana?
[Chithunzi patsamba 7]
Ku Ethiopia, Meswat ndi Yoalan tsopano akutumikira Yehova nthaŵi yonse kutsanzira chitsanzo cha atate awo, amene ananyongedwa
[Chithunzi patsamba 7]
Entellia, wosunga umphumphu wachichepere kumpoto kwa Afirika