Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 1/1 tsamba 10-19
  • Mtundu Wosunga Umphumphu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtundu Wosunga Umphumphu
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtunduwo Ubadwa
  • Chiŵerengero Chapamwamba Chatsopano cha Ofalitsa
  • “Chitani Ichi”
  • “Osaleka Kusonkhana Kwathu Pamodzi”
  • “Chita Nawo”
  • Sungani Umphumphu Kufikira Mapeto
  • Chitani Changu pa Zinthu Zabwino!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Nsanja ya Olonda—1995
w95 1/1 tsamba 10-19

Mtundu Wosunga Umphumphu

“Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene [uli ndi mayendedwe okhulupirika, NW] uloŵemo.”​—YESAYA 26:2.

1. Kodi nchifukwa ninji mawu a Yesaya onena za “mtundu wolungama” angakhale odabwitsa?

LEROLINO, pali mitundu yosiyanasiyana. Ina ndi yademokrase, ina ndi yopondereza. Ina njolemera, inanso njosauka. Koma yonseyo ili ndi chinthu chimodzi chofanana: Ili mbali ya dziko limene Satana ali mulungu wake. (2 Akorinto 4:4) Polingalira zimenezi, ena angadabwe ndi mawu a Yesaya akuti: “Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene uli ndi mayendedwe okhulupirika uloŵemo.” (Yesaya 26:2) Mtundu wolungama? Inde, pali mtundu wolungama, popeza kuti ulosiwo ukutchula za kukhalako kwake m’tsiku lathu. Kodi mtundu wachilendo umenewu ungadziŵidwe motani?

2. Kodi “mtundu wolungama” nchiyani? Kodi tidziŵa bwanji?

2 Malinga ndi mmene New World Translation imamasulira Yesaya 26:2, mtunduwo ukunenedwa kuti “uli ndi mayendedwe okhulupirika.” Baibulo la Revised Nyanja (Union) Version limamasulira vesilo kuti, “mtundu wolungama, umene uchita zoonadi.” Onsewo ali mamasuliridwe oyenera. Ndipotu, mtundu wolungama uli wosavuta kuzindikira chifukwa ndiwo mtundu wokha padziko lapansi umene umagonjera kwa Kristu Mfumu, chotero suli mbali ya dziko la Satana. (Yohane 17:16) Pokhala wotero, ziŵalo zake zili zodziŵika chifukwa cha ‘kukhala ndi mayendedwe okoma mwa amitundu.’ Zimatsatira moyo umene umalemekeza Mulungu. (1 Petro 2:12) Ndiponso, kulikonse kumene zili m’dziko, zili mbali ya “[mpingo, NW] wa Mulungu wamoyo, mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Timoteo 3:15) Popeza kuti zimachirikiza choonadi, zimakana mafilosofi achikunja ophunzitsidwa ndi Dziko Lachikristu, ndipo zimachirikiza “mkaka woyenera [wa mawu, NW]”​—Mawu a Mulungu, Baibulo. (1 Petro 2:2) Ndiponso, zimalalikira mwachangu mbiri yabwino ya Ufumu ku “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.” (Akolose 1:23) Kodi pangakhale kukayikira kulikonse kwakuti mtundu umenewu suli wopangidwa ndi otsalira a “Israyeli wa Mulungu,” mpingo wa Akristu odzozedwa? Kutalitali!​—Agalatiya 6:16.

Mtunduwo Ubadwa

3. Fotokozani mmene “mtundu wolungama” unabadwira.

3 Kodi “mtundu wolungama” umenewo unabadwa liti? Kuyambika kwake kunaloseredwa m’buku la Yesaya. Pa Yesaya 66:7, 8, timaŵerenga kuti: “Mkazi [Ziyoni] asanamve zoŵaŵa, anabala mwana; kupweteka kwake kusanadze, anabala mwana wamwamuna. . . . Ziyoni anamva zoŵaŵa, pomwepo anabala ana ake.” Chodabwitsa kwambiri nchakuti, Ziyoni, gulu lakumwamba la Mulungu, anali kudzabala “mwana wamwamuna” asanayambe kumva zoŵaŵa za kubala. Mu 1914, Ufumu Waumesiya unabadwa kumwamba. (Chivumbulutso 12:5.) Pambuyo pake, nkhondo yadziko yoyamba inaloŵetsamo mitundu yambirimbiri, ndipo Akristu odzozedwa anavutika kwambiri ndi nsautso ndi chizunzo. Potsirizira pake, m’chaka cha 1919, mtundu wauzimu, “mwana mwamuna,” unabadwa padziko lapansi. Motero Ziyoni “anabala ana ake,”​—ziŵalo zodzozedwa za “mtundu wolungama” watsopano​—ndipo ameneŵa anakonzekeretsedwa kaamba ka ntchito yaumboni yomakulakula nthaŵi zonse.​—Mateyu 24:3, 7, 8, 14; 1 Petro 2:9.

4. Kodi nchifukwa ninji mtundu wolungama wa Mulungu wakhala ukulimbikira kuti usunge umphumphu?

4 Kuyambira pa kukhalapo kwake, mtundu umenewu wakumana ndi ziyeso zowopsa pa umphumphu wake. Chifukwa ninji? Pamene Ufumu wakumwamba unabadwa, Satana ndi ziŵanda zake anachotsedwa kumwamba ndi kuponyedwa padziko lapansi. Mawu aakulu analengeza kuti: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku. Ndipo iwo anamlaka iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa, ndi chifukwa cha mawu a umboni wawo; ndipo sanakonda moyo wawo kungakhale kufikira imfa.” Satana anakwiya nazo kwambiri zimene zidachitikazo ‘nachoka kumka kuchita nkhondo ndi otsala a mbewu yake [ya mkazi], amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.’ Poyang’anizana ndi ziukiro zowopsa za Satana, Akristu odzozedwa anachirimika. Kufikira lerolino, ziŵalo zachangu za mtundu wolungama wa Mulungu zimasonyeza chikhulupiriro m’mwazi woombola wa Yesu ndipo zimapitirizabe kupatsa Yehova yankho lotsutsa wotonza wamkulu mwa kusunga umphumphu “kungakhale kufikira imfa.”​—Chivumbulutso 12:1, 5, 9-12, 17; Miyambo 27:11.

5. Kodi ndi mkhalidwe wa maganizo wabwino wotani wa Mboni zamakono umene wawathandiza kusunga umphumphu?

5 Mu 1919, pamene kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu kwamakono kunayamba, Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova la panthaŵiyo, anali ochepa m’chiŵerengero koma olimba m’chikhulupiriro. Ziŵalozo zinakhala maziko a ‘mudzi wolimba; wokhala ndi chipulumutso monga machemba ndi malinga.’ Chidaliro chawo chinali mwa “[Ya, NW] Yehova [amene ali] thanthwe lachikhalire.” (Yesaya 26:1, 3, 4) Monga Mose wakale, izo zinalengeza kuti: “Ndidzalalika dzina la Yehova; nenani kuti Mulungu wathu ndi wamkulu. Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.”​—Deuteronomo 32:3, 4.

6. Kodi ndi m’njira yotani imene Yehova wadalitsira anthu ake m’masiku ano otsiriza?

6 Chiyambire nthaŵiyo, zipata za kakonzedwe ka Ufumu wa Mulungu zakhala zili chitsegukire pamene choyamba otsala a Akristu odzozedwa a 144,000 anasonkhanitsidwa ndipo tsopano khamu lalikulu la “nkhosa zina” likudziphatika m’kulengeza zifuno za Ufumu wa Yehova. (Yohane 10:16) Chotero, kungalengezedwe mwachisangalalo kuti: “Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.” (Yesaya 26:15) Pamene tikuunguza munda wa dziko lonse lerolino, timaona mawuwo kukhala oona chotani nanga! Mwa mphamvu ya mzimu woyera, umboni wa Ufumu wa Kristu ulinkudza waperekedwa “kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Kukula kwa chifutukuko chimenecho kungaonedwe m’Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1994 la Mboni za Yehova Padziko Lonse, lomwe lili pamasamba 12 mpaka 15.

Chiŵerengero Chapamwamba Chatsopano cha Ofalitsa

7, 8. (a) Kodi pali umboni wotani wakuti anthu a Mulungu ‘atanimphitsa zingwe za mahema awo’? (b) Mwa kuyang’ana pa Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1994, kodi ndi maiko ati amene mukuona kuti ‘akukuza malire awo’ kwambiri?

7 Talingalirani mbali zapadera za lipotilo. Chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa a Ufumu m’munda chinafika pa 4,914,094! Nkosangalatsa chotani nanga kuona kusonkhanitsidwa kopitirizabe kwa “khamu lalikulu . . . ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera”! Inde, awanso adzisonyeza kukhala osunga umphumphu. ‘Atsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa,’ akumayesedwa olungama chifukwa cha kusonyeza chikhulupiriro m’nsembe yadipo ya Yesu.​—Chivumbulutso 7:9, 14.

8 Makamaka chiyambire 1919, chilangizo chaperekedwa ku gulu la Yehova kuti: “Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.” (Yesaya 54:2) Mwa kulabadira zimenezo, ntchito yolalikira ikupitirizabe kosaleka, ngakhale ku Yukon wozizira kwambiri, kumalire a Alaska, kumene kagulu ka apainiya olimba mtima kakupirira kuzizira kumene kumafika pa -45 kapena -50 digiri Celsius kwa milungu yambiri. M’zaka zaposachedwapa makamu akhala akupita mofulumira ndi mwaunyinji kumtundu wa Yehova wosunga umphumphu. Zipata zatseguka motakata kuti ameneŵa alandiridwe kuchokera ku maiko a ku Asia akunja kwa Dziko Lachikristu, kuchokera ku madera amene kale anali mizati ya Chikomyunizimu, kuchokera m’maiko ambiri a mu Afirika, ndi kuchokera ku malo ena Achikatolika, onga Italy, Spain, Portugal, ndi South America. Anthu othaŵa kwawo atsegula munda wina. Mwachitsanzo, ku England, Mboni zikusamalira zosoŵa za mafuko 13 olankhula zinenero zakunja.

“Chitani Ichi”

9. (a) Kodi chiŵerengero cha opezeka pa Chikumbutso cha 1994 chikusonyeza chiyani? (b) Kodi ndi maiko ena ati amene ali ndi ziŵerengero zapamwamba kwambiri za opezeka pa Chikumbutso?

9 Mbali ina yapadera ya lipoti la chakalo ndiyo opezeka pa Chikumbutso. Imfa yake itayandikira, Yesu anayambitsa Chikumbutso cha imfa yake ndipo anauza otsatira ake kuti: “Chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.” (1 Akorinto 11:24) Kunali kosangalatsa mu 1994 kuona anthu 12,288,917​—kuposeratu pa kuŵirikiza kaŵiri chiŵerengero cha ofalitsa okangalika​—akusonkhana pamodzi kumvera lamulolo, monga akudya kapena monga openyerera. M’maiko ena, opezeka pa Chikumbutso ogaŵidwa pa wofalitsa mmodzi anali ochulukirapo. Ofalitsa 4,049 ku Estonia, Latvia, ndi Lithuania anakondwera kukhala ndi opezeka pa Chikumbutso 12,876, kuŵirikiza katatu kuposa chiŵerengero cha ofalitsa. Ndipo ku Benin, opezeka pa Chikumbutso 16,786 anali chiŵerengero choŵirikiza pafupifupi kasanu kuposa ofalitsa. Mpingo wina wa ofalitsa pafupifupi 45 unali ndi opezekapo 831!

10. (a) Kodi chiŵerengero chapamwamba cha opezeka pa Chikumbutso chikuika thayo lotani pa ife? (b) Fotokozani zimene zingachitike pamene munthu amene anapezeka pa Chikumbutso alandira thandizo lowonjezera.

10 Mboni za Yehova zili zokondwa kuti anthu ambiri okondwerera anagwirizana nawo pa chochitika chofunika chimenecho. Tsopano zikufuna kuthandiza anthuwa kukula kwambiri m’chidziŵitso chawo cha choonadi ndi chikondi chawo pa icho. Ena angachite monga momwe anachitira Alla ku Russia. Alla anali kuphunzira ndi mlongo wina mpainiya wapadera koma sanali kupita patsogolo kwenikweni, chotero phunzirolo linaimitsidwa. Komabe, Alla anavomera chiitano cha kukapezeka pa Chikumbutso. Msonkhanowo, umene uli ndi tanthauzo lalikulu kwambiri, unamkhudza mtima kwambiri mkaziyo. Atabwerera kunyumba, anataya mafano ake onse napempha thandizo kwa Yehova. Patapita masiku aŵiri, mlongo wachipainiya uja anachezera Alla kuti akaone mmene Chikumbutso chinamsangalatsira. Panakhala makambitsirano obala zipatso. Phunziro la Alla linayambidwanso. Posapita nthaŵi, iye anayamba kukhala ndi phande m’ntchito yaumboni. Chochitika chimenechi chikusonyeza kufunika kwa maulendo obwereza kwa awo amene amapezeka pa Chikumbutso. Ambiri adzachita mofanana ndi Alla.

“Osaleka Kusonkhana Kwathu Pamodzi”

11-13. (a) Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’mayendedwe okhulupirika a mtundu wolungama? (b) Kodi nchifukwa ninji Akristu oona afunikira kupezeka pamisonkhano?

11 Chikumbutso ndicho msonkhano wofunika koposa pampambo wa zochitika za Mboni za Yehova, koma sindiwo msonkhano wokha umene ulipo. Mlungu uliwonse Mboni za Yehova zimasonkhana pamodzi momvera mawu a mtumwi Paulo akuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Izo zikugwirizana ndi mtundu wolungama wa Yehova umene ukudziŵika ndi mayendedwe ake okhulupirika. Mayendedwe okhulupirika amaphatikizapo kupezeka pamisonkhano mokhulupirika.

12 Malinga ndi umboni, zimenezi zamvetsetsedwa bwino lomwe ku Philippines, kumene avareji ya opezeka pamisonkhano ya pa Sande m’dziko lonselo ili 125 peresenti ya chiŵerengero cha ofalitsa. Nakonso, kagulu ka Mboni ndi anthu okondwerera ku Argentina kamamvetsetsa zimenezo. Iwo amakhala pamtunda wa makilomita 20 kuchokera pa Nyumba Yaufumu. Komabe, woyang’anira dera akusimba kuti palibe ndi mmodzi yemwe amene amaphonya misonkhano kusiyapo atadwala. Amayenda maola anayi pangolo kapena pakavalo, ndipo m’nyengo yachisanu amapita kunyumba mumdima usiku.

13 Pamene mapeto a dongosolo ili akuyandikira kwambiri, moyo ukuvutirapo, mavuto akuchuluka, ndipo kupezeka pamisonkhano nthaŵi zonse kungakhalenso kovuta kwambiri. Koma m’mikhalidwe yoteroyo, tifunikira kwambiri chakudya chauzimu ndi mayanjano achikondi koposa ndi kalelonse zimene zimangopezeka pamisonkhano imeneyo.

“Chita Nawo”

14. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimaona utumiki wawo kukhala wofulumira, ndipo kodi ndi zotulukapo zotani zimene zikusonyeza zimenezi?

14 Chaka chatha, Tchalitchi cha Katolika ku Italy chinatcha ntchito ya Mboni za Yehova kukhala “kutembenuza anthu kwachipongwe.” Koma kunena zoona, zimene Mboni zimachita sizili zachipongwe. M’malo mwake, utumiki wawo uli chisonyezero cha chikondi chawo chachikulu kaamba ka anansi awo. Ulinso umboni wa kumvera kwawo mawu a Paulo akuti: “Lalika mawu; chita nawo pa nthaŵi yake, popanda nthaŵi yake.” (2 Timoteo 4:2) Kufulumira kwa nthaŵi kumasonkhezera Mboni za Yehova kukhala zachangu mu utumiki wawo, monga momwe tikuonera m’kuthera kwawo maola okwanira 1,096,065,354 mu 1994 zikumalalikira kwa anansi awo, kupanga maulendo obwereza, ndi kuchititsa maphunziro a Baibulo 4,701,357. Ambiri anakhala ndi phande mu utumiki waupainiya, zimene zikusonyeza kuti mzimu waupainiya uli wamoyo ndi wamphamvu. Avareji ya apainiya 636,202 padziko lonse ikutsimikizira zimenezi.

15, 16. (a) Kodi ndimotani mmene achichepere ndi achikulire omwe asonyezera mzimu waupainiya? (b) Mwa kuyang’ana pa dziko limodzi ndi limodzi pa Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1994, kodi mpati pamene mukuona ziŵerengero zazikulu kwambiri za apainiya?

15 Pakati pa apainiya ameneŵa pali achichepere ambiri. Ena ku United States akutumikira tsopano monga apainiya okhazikika pamene ali pasukulu yasekondale, gawo lawo lalikulu likumakhala anzawo a m’kalasi. Achichepere ameneŵa apeza kuti upainiya ndiwo njira yabwino koposa yodzitetezera iwo eni ku anamgoneka, chisembwere, ndi chiwawa zimene zili zofala m’masukulu ambiri m’dzikolo. Achichepere ena ambiri ali ndi chonulirapo cha kuchita upainiya atatsiriza sukulu. Irina, ku Ukraine, anachita upainiya wothandiza m’zaka zonse zimene anali pasukulu yasekondale akumadzikonzekeretsa iye mwini kaamba ka kuchita upainiya atamaliza maphunziro. Pamene anamaliza sukulu, banja lake linati lidzamthandiza pa zandalama kotero kuti iye awaimireko m’ntchito yaupainiya wokhazikika. Ndalama nzovuta kupeza ku Ukraine. Koma Irina akuti: “Ndikudziŵa kuti ndikuchita ntchito imene idzadzetsa moyo osati kwa ine ndekha komanso kwa awo amene ndimalalikirako.” Nkosangalatsa kuona achinyamata ambiri lerolino akulingalira monga Irina. Kodi pangakhale njira ina yabwino imene iwo ‘angakumbukirire Mlengi wawo masiku a unyamata wawo’ kuposa imeneyi?​—Mlaliki 12:1.

16 Apainiya ochuluka ali okalamba. Wina akusimba kuti mkati mwa nkhondo yadziko yachiŵiri, atate wake ndi mchimwene wake anaphedwa pamene anali kumenya nkhondoyo, ndipo amayi ake ndi mchemwali wake anawomberedwa mfuti m’komboni ina. Pambuyo pake mkaziyo anafedwa mwana wake wamwamuna. Tsopano, mu ukalamba wake ndi thanzi lake lodwalira, Yehova wampatsa banja lalikulu kwambiri mumpingo Wachikristu kuposa limene anataya. Ndipo amapeza chimwemwe kuthandiza ena monga mpainiya wokhazikika.

17, 18. Kodi ndimotani mmene aliyense wa ife, mpainiya kapena wofalitsa, angasonyezere mzimu waupainiya?

17 Ndithudi, saliyense amene akhoza kukhala mpainiya. Yehova amakondwa kwambiri kulandira chachikhumi chathu chonse, zinthu zabwino koposa zimene tingapereke, zilizonse zimene ife tingapereke. (Mlaliki 3:10) Indedi, tonsefe tingakulitse mzimu wa apainiya achangu ameneŵa ndi kuchita zonse zimene mikhalidwe yathu ilola, kupititsa patsogolo mbiri yabwino.

18 Mwachitsanzo, ku Australia, tsiku la April 16 linasankhidwa kukhala tsiku lapadera la umboni wa m’khwalala. Ofalitsa ndi apainiya analichirikiza kwambiri, monga momwe chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa 58,780 m’mweziwo chinasonyezera. Ndiponso, magazini 90,000 anagaŵiridwa kuposa m’mwezi umodzimodziwo wa chaka chathacho. Patsiku lapadera, mlongo wina anagaŵira magazini kwa mwamuna wina, ndipo pamene anali kulemba dzina lake ndi keyala kuti akabwerereko kulondola chikondwerero, iye anapeza kuti mwamunayo anali wachibale wake! Iye anali mlongo wake mwa amayi ake aakulu ndipo sanaonanepo kwa zaka 30. Ndithudi zimenezo zinachititsa maulendo obwereza osangalatsa kwambiri!

Sungani Umphumphu Kufikira Mapeto

19. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika mwamsanga kuti mtundu wolungama wa Yehova usunge umphumphu kufikira mapeto?

19 Kuli kofunika mwamsanga kuti onse amene ali mu mtundu wolungama wa Mulungu asunge umphumphu wawo pamene dziko la Satana likuloŵa m’zoŵaŵa zake za imfa. Posachedwa, mtundu woyera wa Yehova udzamva chiitano chakuti: “Idzani, anthu anga, loŵani m’zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthaŵi kufikira mkwiyo utapita.” Mosapeŵeka, dzikoli lokhala ndi liwongo la mwazi lidzalandira chiweruzo cha Mulungu. “Pakuti taonani, Yehova adza kuchokera ku malo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwawo; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.” (Yesaya 26:20, 21) Aliyense wa ife achirimiketu monga Mkristu wosunga umphumphu wogwirizana ndi mtundu wolungama wa Yehova. Ndiyeno tidzakondwa kupeza moyo wosatha mu Ufumu wa Kristu, padziko lapansi kapena kumwamba.

Kodi Mukukumbukira?

◻ Kodi “mtundu wolungama” unabadwa liti?

◻ Kodi nchifukwa ninji anthu a Mulungu afunikira chipiriro m’masiku ano otsiriza?

◻ Kodi nchiyani chimene ziŵerengero zapamwamba za ofalitsa ndi maola ochuluka otheredwa mu utumiki zikusonyeza pa Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1994?

◻ Kodi nchifukwa ninji kupezeka pamisonkhano kuli kofunika kwambiri pamene dzikoli likuyandikira kwambiri mapeto ake?

◻ Kodi nchifukwa ninji onse amene akugwirizana ndi mtundu wolungama wa Mulungu ayenera kusunga umphumphu?

[Tchati pamasamba 12-15]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1994 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Chithunzi patsamba 18]

Osunga umphumphu mu mtundu wolungama wa Yehova adzapeza moyo wosatha wangwiro

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena