Olengeza Ufumu Akusimba
Yehova Ali Wolimba Kuposa Adani Ake
MDYEREKEZI ndi ziŵanda zake ayesayesa kwa nthaŵi yaitali kuti adodometse ntchito yolalikira mbiri yabwino mwa kugwiritsira ntchito chipembedzo chonyenga ndi kulambira mizimu. Baibulo limanena za cholinga choipa cha Satana pa 2 Akorinto 4:4 pamene limati ‘mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano wachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiŵalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.’
Koma Yehova Mulungu ali wolimba kuposa Satana. Palibe chilichonse chimene adani a Yehova angachite kuti alepheretse chifuniro chake chaumulungu kukwaniritsidwa, chimene chili chakuti “anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:4) Malipoti otsatirawa ochokera kwa olengeza Ufumu mu Australia akusonyeza zimenezi.
◻ Pambuyo polekana ndi chipembedzo kwa zaka 20, mkazi wina anayamba kuŵerenganso Baibulo. Chikondwerero chake chodzutsidwanso pa Baibulo chimenechi chinamchititsa kukhala ndi mafunso ambiri, motero anapemphera kwa Mulungu kuti amthandize kupeza mayankho. Iye anafuna kufunafuna choonadi, koma anadziŵa kuti kubwerera ku chipembedzo chake chakale sikukathetsa vuto lake. M’malo mwake, anayamba kufunafuna kwakeko mwa kupita ku sitolo ya mabuku ogwiritsiridwapo kale ntchito nafunsa ngati iwo anali ndi mabuku alionse onena za chipembedzo.
Mwinisitolo wamkazi anakumbukira kuti anali ndi buku lina lachipembedzo, osati m’sitolomo, koma kunyumba. Mutu wa bukulo unali wakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mkaziyo anaŵerenga bukulo mwachidwi ndipo anapeza mayankho pa mafunso ake ambiri onena za Baibulo. Atafunafuna Mboni za Yehova m’buku la manambala a mafoni, potsirizira pake anakambitsirana nazo ndipo anayamba phunziro la Baibulo lokhazikika.
◻ Mkazi wina wachichepere analipira ku nyuzipepala ya kwawo kuti imsatsire malonda a chithumwa. Chilengezo chosatsa malondacho chinachitchula kukhala ‘chithumwa chamakedzana champhamvu yadzaoneni.’ Mkazi wina wa Mboni za Yehova anaona chilengezocho. Iye anaganiza za kuimba lamya ku nambala yosonyezedwa ndi kulankhula kwa mkaziyo za magwero a mphamvu yolingaliridwa kukhala ndi chithumwacho. Chinatsatirapo chinali makambitsirano a lingaliro la Baibulo pa machitachita auchiŵanda. Mkazi wachichepere wa chithumwayo anaulula kuti dzulo lakelo, anali atapemphera kwa Mulungu kuti amthandize pa mavuto ake ndi ziŵanda. Mboniyo inapanga makonzedwe a makambitsirano enanso palamya.
Pamene iye anaimba lamya, mkazi wachichepereyo sanali panyumba. Amayi ake anayankha lamyayo ndi kunena kuti: “Sindidziŵa kuti munamuuza chiyani mwana wanga, koma chimene chachitika ndi chozizwitsadi!” Iye anafotokoza kuti pambuyo pa kukambitsirana palamya koyamba kuja, mwana wake wamkaziyo anataya zithunzithunzi zake zonse zausatana ndi mabuku ndi kuyamba kuŵerenga Baibulo.
Posapita nthaŵi, makonzedwe anapangidwa akuti akachezere mkazi wachichepereyo. Iye kamodzinkamodzi anavomereza phunziro la Baibulo lokhazikika ndi Mboni za Yehova. Anayambanso kuyanjana ndi Mboni mwa kufika pamisonkhano yawo Yachikristu. Apanso, Yehova anagonjetsa ziŵanda mwa kuŵalitsa chidziŵitso cholongosoka cha choonadi cha Baibulo.