Ripoti la Olengeza Ufumu
Kuchokera ku Tondovi Kumka ku Chimwemwe
YEHOVA ali Mulungu wachimwemwe. (1 Timoteo 1:11) Iye amafuna omtumikira kukhalanso achimwemwe. Motero, ngati mmodzi wa atumiki ake wachita tondovi, Yehova adzamthandiza kupirira vutolo ndipo nthaŵi zina ngakhale kupezanso mkhalidwe wachimwemwe. Chokumana nacho chotsatirachi chochokera ku Uruguay chimalongosola mwafanizo zimenezi.
Mlongo wina ankayembekezera pakiliniki m’Montevideo kaamba ka zotulukapo pambuyo popimidwa ndi X-ray. Dona wina wokhala pafupi naye anali kuchita mantha ponena za chimene dokotala akamuuza monga chotulukapo cha kupimidwa kochitidwa pa iye. Mlongoyo anauza mkazi ameneyo kuti kuyambira pamene iye anakhala Mboni ya Yehova, sanawope chirichonse. Komabe donayo, ananena kuti sanayanje Mboni za Yehova chifukwa chakuti izo zinayembekezera muyezo wapamwamba koposa kuchokera kwa anthu.
Ndiyeno mlongoyo anauza mkaziyo mmene chidziŵitso cha chowonadi cha Baibulo chinamthandizira. Iye anaferedwa mwana wamkazi wazaka 18 zakubadwa ndipo anagwera m’kuchita tondovi kwambiri kwazaka zisanu ndi zitatu. Akatswiri amaganizo limodzinso ndi mankhwala odya ndalama sizinamthandize kuthetsa kuchita tondoviko. Kangapo, iye anatero, anasungidwa m’chipatala, koma panalibe kuwongokera kulikonse. Banja lake linasamaliridwa ndi antchito ake chifukwa chakuti iye sanakhoze kuwachitira kalikonse. Anayesa kudzipha chifukwa chakuti anataya chikondwerero m’moyo. Palibe chirichonse chinawonekera kukhala chothandiza.
Ndiyeno, anauza donayo, tsiku lina Mboni za Yehova zinadza ndikumsiyira mabuku Abaibulo. Zimenezo zinadzutsa chikondwerero chake m’Mawu a Mulungu, ndipo anayamba kuŵerenga Baibulo lonse. Kusintha kunayamba kuchitika mwa iye. Anayamba kudzuka m’mamaŵa ndikuyamba kusamalira banja lake. Pomalizira pake anasankha kusamalira nyumba iye mwini naapeza kuti anakhoza kutero. Kunali ngati kuti sanali wovutika konse! Izi zinampangitsa kumva ali wachimwemwe kwambiri.
Iye sanabwererenso kwa katswiri wamaganizo. Chikhumbo chake chakukhala ndi moyo chinasonkhezeredwa ndi chidziwitso chake cha Mawu a Mulungu, ndipo chimenechi chinatsimikizira kukhala mankhwala abwino koposa. Anafunafuna Mboni za Yehova, ndipo zinayamba kuphunzira naye mokhazikika. Anayambanso kufika pamisonkhano, ndipo posapita nthaŵi anabatizidwa. Posavutitsidwanso ndi tondovi, tsopano akupeza chisangalalo m’kutumikira Yehova.
Donayo m’chipinda choyembekezerera anamvetsetsa mwatcheru. Ndiyeno anati kwa mlongoyo: “Kwanthaŵi yakutiyakuti, Mboni za Yehova zakhala zikukambitsirana nane; koma ngati ine nthaŵi ina mtsogolo, ndikhaladi mmodzi wa Mboni za Yehova, kudzakhala chifukwa cha zimene mwangondiuza kumene. Kukumvetserani kuli ngati kuyamba kuwona kuunika m’malo amdima.”
Anthu ambiri kuzungulira dziko akuwona kupanda pake kwa kuyesa kuthetsa mavuto a moyo iwo okha, ndipo akutembenukira kwa Yehova Mulungu. Ngachimwemwe chotani nanga kuphunzira za kudza kwa dziko latsopano la Mulungu m’mene aliyense adzakhala wachimwemwe, ndipo kuchita tondovi kudzakhala chinthu chakale!—Miyambo 16:20.