Lipoti la Olengeza Ufumu
“Wodala Ndiwopeza Nzeru”
MWAMBI umenewu watsimikizira kukhala wowona ku Korea, kumene tsopano kuli Mboni za Yehova zachimwemwe zoposa 71,000. (Miyambo 3:13) Ndipo tangolingalirani, 42 peresenti ya atumiki ameneŵa ali muutumiki wanthaŵi yonse! Zokumana nazo zotsatirazi zidzasonyeza kuti chimwemwe ndicho mkhalidwe wa awo amene amafunafuna nzeru yowona.
Mkazi wina ku Pusan anakhala akupita kutchalitchi china cha Dziko Lachikristu kwa zaka 16. Iye anaona machitachita ambiri osakhala a m’malemba kwakuti anayamba kuganiza kuti mwina kulibe Mulungu. Komabe, chamkatikati ankadziŵa kuti Mulungu aliko, motero anapemphera mowona mtima kwa Mulungu kuti apeze tchalitchi chowona ngati chinaliko. Mwadzidzidzi panthaŵiyi analingalira za Mboni za Yehova, ndipo anakumbukira kuti tchalitchi chake chinawanyoza ndi kuchenjeza ofika kutchalitchi za iwo chifukwa chakuti Mboni sizinakhulupirire Utatu, helo wamoto, ndi ziphunzitso zina za Dziko Lachikristu. Kodi iwo sanali tchalitchi chowona? Mothandizidwa ndi mnansi wake, anapeza malo a Nyumba Yaufumu. Tsiku lotsatira, anafika pamsonkhano.
Iye anachita chidwi ndi dongosolo labwino la msonkhanowo. Panalibe kukuwa konyanyuka kapena kuimba kotengeka maganizo monga momwe zinaliri kutchalitchi kwake. Anadziŵikitsidwa kwa Mboni ina imene inali yofunitsitsa kuphunzira naye Baibulo, ndipo phunziro loyamba linatenga maola angapo chifukwa cha mafunso ake ambiri. Paphunziro lachiŵiri, ananena kuti akusiya tchalitchi chimene anali ndipo akakhala Mboni. Anauza mlongoyo kuti sakafunikira kuphunzira nayenso, chifukwa akakhala akufika pamisonkhano. Komabe, anasonyezedwa kufunika kwa kukhala ndi phunziro laumwini la Baibulo kuwonjezera pakufika pamisonkhano. Anavomereza lingalirolo, namamatira kuphunziro lake, ndipo m’kupita kwanthaŵi anabatizidwa.
Tsopano iye ngwachimwemwe kwambiri kuti wapeza nzeru ya Mulungu wowona, Yehova, ndipo ali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano la Mulungu.
Mkulu Wankhondo Wopuma Pantchito Aphunzira Chowonadi
Mkazi wina wa mkulu wankhondo anabatizidwa mu 1962. Poyamba mwamuna wake anamtsutsa, koma pambuyo pake anasiya, ndipo kwazaka 28, abale osiyanasiyana anaphunzira naye modukizadukiza, akumayesa kudzutsa chikondwerero cha chowonadi mwa iye. Iye anafika pamisonkhano ina ndi misonkhano yachigawo, koma anali munthu wozengereza kuona chowonadi mwamphamvu. Mu 1990 iye ndi mkazi wake anapita ku Japan, kumene analoŵa msonkhano wachigawo. Panthaŵi imeneyi anamvetsera mosamalitsa nkhani—chinthu chimene anali asanapangepo. Anadabwa ndi nkhani zokambidwa molimba mtima zovumbula chipembedzo chonyenga, ndipo zimenezi zinamtseguladi maso kuti awone chinyengo cha Dziko Lachikristu. Iye anachita chidwi ndi dongosolo ndi chimwemwe cha anthu a Mulungu ku Japan, zimene zinali zofanana ndi zimene anawona ku Korea. Atabwerera ku Korea, anayamba kuphunzira Baibulo mwakhama ndipo potsirizira pake anabatizidwa.
Chotero pambuyo paubatizo wake kodi iye anayenera kuchitanji? Anasiya malo ake antchito monga mkulu wa hotelo ya alendo yotchuka ndi kugwirizana ndi mkazi wake muutumiki wanthaŵi yonse waupainiya. Iye akulingalira kuti kukhala mpainiya wokhazikika ndiko njira yabwino koposa yolipirira zaka 28 zimene anawononga akumazengereza.
Tsopano akuzindikira kuti mwambi wakuti “wodala ndiwopeza nzeru” ngwogwiranso ntchito kwa iye!