Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 9/1 tsamba 23
  • Nkhosa za Yesu Zimva Mawu Ake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nkhosa za Yesu Zimva Mawu Ake
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Mbiri Yabwino Kuchokera ku Norway
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Wodala Ndiwopeza Nzeru”
    Nsanja ya Olonda—1993
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kuchokera ku Tondovi Kumka ku Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 9/1 tsamba 23

Lipoti la Olengeza Ufumu

Nkhosa za Yesu Zimva Mawu Ake

PAMENE ntchito yolalikira ikufutukukira kumbali zonse za dziko lapansi, Yehova kupyolera mwa angelo ake akutsogoza atumiki ake kwa anthu onga nkhosa. Iwo amamva mawu a Yesu naphunzira kumtumikira ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Yesu anati pa Yohane 10:27, 28: “Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo ine ndizizindikira, ndipo zinditsata ine. Ndipo ine ndizipatsa moyo wosatha.” Tawonani mmene owona mtima anamvera mawu a Yesu ku Madagascar.

Mmodzi wa Mboni za Yehova anagaŵira kope la bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi ndi Your Youth​—Getting the Best Out Of It kwa sing’anga amene anabwera kudzapima atate wake odwala.

Dokotalayo anali Mprotesitante ndi wotsutsa Mboni kwambiri, koma anaŵerenga bukhulo napenda malemba m’Baibulo lake. Mkazi wake, Mkatolika amenenso ali dokotala, anaŵerenga bukhu la Youth nthaŵi zingapo chifukwa ananena kuti linawonekera kwakukulukulu kukhala lolembedwera iye. Malongosoledwe a Sosaite ozikidwa pa Baibulo onena za tanthauzo la 1914 anawachititsa chidwi onse aŵiri. Mwamunayo anapeza Mboni imene inampatsa mabukuwo. Mboniyo inampatsanso bukhu la Life​—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? ndi kupanga makonzedwe akumchezetsa iye ndi mkazi wake kuti akayankhe mafunso awo. Pamene anawachezetsa, anayamba phunziro Labaibulo lokhazikika ndi okwatiranawo ndi ana awo atatu. Chidziŵitso chawo cha Baibulo chinakula mofulumira.

Pambuyo pa phunziro loyamba, banja lonse linayamba kufika pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu ndipo mwamsanga pambuyo pake linalembetsa m’Sukulu Yauminisitala Wateokratiki. Mkhalidwe wa ana unawongokera kwambiri. M’phunziro lawo Labaibulo, anaphuzira kuti kusunga masiku akubadwa ndi maholide ena achipembedzo sikunali Kwachikristu; chotero, anasiya kuwasunga. Mwamunayo anakana kupatsa mwazi wake kwa wachibale, ngakhale kuti nkhaniyo inali isanapendedwe paphunziro Labaibulo. Posapita nthaŵi yunifomu yake ya karati inazimiririka m’wadirobu; anaitumiza kwa wosoka zovala kuti akamsokere zovala za ana ake. Anatentha magazini ndi mabuku ake onse onena za kupenda nyenyezi. Patangopita miyezi itatu yokha kuchokera pamene anayambira kuphunzira, onse aŵiri mwamunayo ndi mkazi wake anachoka m’matchalitchi awo nasonyeza chikhumbo cha kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira. Iwo tsopano ngobatizidwa.

◻ Mkazi wina ku Thailand anali kufunafuna chowonadi. Ngakhale kuti anali Mbudha, sanali konse wodzipereka kuchipembedzo chake chifukwa chakuti anawona chinyengo chachikulu ndi umbombo. Ndiponso, panali miyambo yosiyanasiyana imene anaipeza kukhala yonyansa. Anatopa nazo zonsezo.

Ndiyeno, mnansi wina anapereka lingaliro lakuti ayese Akristu namtengera kutchalitchi cha Pentekoste. Komabe, mkati mwamapemphero, mkaziyo anali ndi chikhumbo champhamvu chakuchoka ndi kupita kunyumba chifukwa cha phokoso, popeza kuti onse amene analipo anali kupemphera mofuula. Imeneyo inali nthaŵi yake yomalizira kupita kutchalitchi chimenecho.

Pambuyo pake, anayesa tchalitchi cha Roma Katolika. Komabe, atapitako kwanthaŵi zingapo, anawonanso chinyengo ndi umbombo, limodzi ndi moyo wa mwanaalirenji wa wansembe. Anaipidwa nasiya kupitako. Wansembeyo anafuna kudziŵa chifukwa chimene anasiira. Atamva chifukwa chake, anati motonyola: “Ngati ufuna kuphatikana ndi anthu osamalitsa, pita kwa Mboni za Yehova.” Mkaziyo anafunsa kuti: “Kodi ali kuti?” Wansembeyo anayankha nati: “Ali pafupi ndi malo oyang’anira zamadzi.” Tsiku lotsatira mkaziyo anawafunafuna mosaphula kanthu. Ngakhale kuti anagwiritsidwa mwala, analingalirabe Mboni za Yehova mosalekeza.

Tsiku lina anamva mmodzi wa anansi ake akuuza mnzake motonyola kuti: “Posachedwapa udzakhala mmodzi wa Mboni za Yehova!” Atamva zimenezo, mkaziyo anapita mofulumira kwa mnansiyo nafunsa kuti: “Kodi kuno kuli Mboni za Yehova?” “Inde,” anayankha motero. “Ena adzabwera chakonkuno kulalikira kunyumba ndi nyumba. Mudzawazindikira ndi kavalidwe kawo kabwino ndi kaudongo.” Atauzidwa zimenezo anathamanga kukawafunafuna. Poyamba sanawapeze, koma pobwerera kunyumba kwake, anawona akazi aŵiri ovala mwaudongo akukambitsirana ndi munthu wina. Anafika pafupi nawafunsa ngati anali Mboni za Yehova. Pamene anati ndiwo, mkaziyo anachonderera kuti: “Chonde idzani kunyumba kwanga. Ndifuna kukamba nanu.”

Phunziro Labaibulo linayambidwa, ndipo mosasamala kanthu za chitsutso ndi chitonzo cha ziŵalo zabanja, dona ameneyu wayamba kufika pamisonkhano ndi kuchitira umboni kwa achibale ake.

Indetu Yesu amadziŵa nkhosa zake ndipo akuzisonkhanitsa m’gulu lake kuti zikapulumuke kuloŵa m’dziko latsopano lolungama.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena