Ripoti la Olengeza Ufumu
Mbiri Yabwino Kuchokera ku Norway
ZOKUMANA nazo zabwino zambiri zikupezedwa ndi olengeza a Ufumu oposa 9,500 a mbiri yabwino mu Norway. Anthu owona mtima akuzindikira uthenga wa Baibulo wolengezedwa ndi Mboni za Yehova monga chowonadi ndi yankho kumapemphero awo, monga momwe zikuwonedwera m’zokumana nazo zotsatirazi.
◻ Okwatirana aŵiri achichepere anapemphera kwa Mulungu kuti awathandize kupeza chifuno m’moyo. Mlungu umodzi pambuyo pake, Mboni za Yehova zinafikira, ndipo mkaziyo anaziitanira m’nyumba. Mwamunayo anali atachenjezedwa kusayanjana ndi Mboni, chotero iye anatuluka kunja kwanyumba kukatsuka galimoto lake. Mkaziyo anabadwira mu Lebanon ndipo anali ndi vuto lachinenero, chotero Mbonizo zinamsonyeza dzina la Yehova m’Baibulo lake la Chiarabu. Milungu iŵiri pambuyo pake Mbonizo zinabwererako, ndipo mwamunayo anatulukiranso kunja kukatsuka galimoto lake. Mbonizo zinafunsa mkaziyo ngati anaganizira kuti mwamuna wake akakhoza kupezekapo nthaŵi yotsatira imene iwo akabwera kotero kuti akatembenuze, ndipo mkaziyo analonjeza kumpempha.
Paulendo wachitatu, galimoto lija linali loyera kwenikweni kwakuti mwamunayo sanalingalire kuti akaligwiritsira ntchito monga chodzikhululukira chotulukira panja, chotero anakhalabe ndi kufunsa mafunso ambiri kuti apeze kusiyana pakati pa Mboni ndi tchalitchi Chaboma. Kuchezerako kunatenga maola atatu, ndipo broshuwa inagawiridwa kwa okwatiranawo. Pamene Mbonizo zinachoka, mkazi uja anapita kukagona koma mwamuna uja anayamba kuiŵerenga broshuwayo, ndi kuŵerenga malemba onse. Pakati pausiku iye anadzutsa mkazi wake ndi kuti: “Iwe uyenera kuŵerenga.” Mkaziyo anauka, ndipo anaŵerengera limodzi kufikira 5 koloko m’mawa. Pozindikira kuti anapeza chowonadi, iwo anakondwera kwadzaoneni ndi kupemphera kwa Yehova, kugwiritsira ntchito dzina lake. Phunziro lokhazikika la Baibulo linayambidwa ndi iwo, ndipo anayamba kupezeka pamisonkhano. Mwamunayo analeka ntchito yake yankhondo, ndipo anachoka m’tchalitchi ndi kuleka kusuta fodya. Tsopano ngobatizidwa ndipo akutumikira Yehova mwachimwemwe limodzi ndi abale ndi alongo awo padziko lonse.
◻ Alongo aŵiri mu uminisitala wawo wakunyumba ndi nyumba mu Norway anakumana ndi mkazi wina yemwe anasonyeza chikondwerero. Iye anawauza kuti akabwerereko ndi kukapempha ngati akakhoza kuitana akazi ena. Paulendo wotsatira, akazi ena anayi analipo. Mmodzi wa iwo anali wokangalika kwenikweni m’tchalitchi. Iye anati chiyambire pamene anali wachichepere, iye anafuna kumvera lamulo la Yesu la kupanga ophunzira. Ichi chinampangitsa kupita ku Afirika ndi mwamuna wake pa projekiti yokathandiza. Akazi onsewa anali ndi mafunso ambiri, ndipo chinakonzekeretsedwa kuti alongowo adziwafikira m’milungu iŵiri iliyonse. Amnyumba zapafupi anaitanidwa, ndipo ena anapitirizabe kubwera pamene ena ake analeka, koma chiŵalo chokangalika chatchalitchi chija chinayamikira kuti iye ankaphunzira chowonadi. Tsiku lina, pamene minisitala watchalitchi chake ananena kuti akachilikiza nkhondo ndi kuti anakhulupirira m’chiphunzitso cha Utatu, iye anachoka m’tchalitchicho. Iye anayamba kupezeka pamisonkhano ya Mboni za Yehova ndipo mwamsanga anayamba kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira. Mwamsanga pambuyo pake iye anabatizidwa. Pomalizira pake tsopano, pambuyo pa zaka 30, iye angasangalale m’kulabadiradi lamulo la Yesu la kupanga ophunzira.—Mateyu 28:19.
Yehova akudalitsa abale mu Norway mu utumiki wawo wopatulika limodzi ndi omvetsera ku mbiri yabwino!