Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 4/1 tsamba 31
  • Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Hong Kong
  • Britain
  • South Pacific
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Muzilola Kuti Yehova Azikutsogolerani
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Otsimikiza Mtima Kutumikira Yehova!
    Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1989
w89 4/1 tsamba 31

Ripoti la Olengeza Ufumu

Chikondi Chigwirizanitsa Mabanja

UMODZI wa banja ungafikiridwe kikha pamene ukwati wazikidwa pa chikondi chotsogozedwa ndi kupanda dyera. Chikondi choterocho chimachokera kwa Yehova, Mulungu wachikondi, chotero chiri chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23; 1 Yohane 4:8) Zokumana nazo zotsatirazi zimachitira chitsanzo mmene chikondi chozikidwa pa chidziŵitso cha Baibulo chagwirizanitsira mabanja.

Hong Kong

◻ Mu Hong Kong mpainiya anayamba phunziro la Baibulo la panyumba ndi mkazi wa panyumba ndi ana ake akazi aŵiri. Mwamunayo analongosola kudera nkhaŵa kuti mkaziyo angakhale akudziloŵetsa m’gulu loipa la chipembedzo. Mpainiyayo analingalira kwa mkaziyo kuti aitane mwamuna wake kupezekapo pa phunziro ndi kugamulapo kaamba ka iyemwini, chimene mwamunayo anachita. Pa nthaŵiyo, mkaziyo anayamba kupezeka pa misonkhano, koma anali ndi vuto la kuphunzitsa ana ake. Iye ankakhoza kunyoza wachikulirekoyo nthaŵi zonse ndi kuipitsa wachichepereyo. Kenaka chinadziŵika kuti iye ndi mwamuna wake anali ndi mavuto. Kukangana kwawo kaŵirikaŵiri kunatulukira m’chiwawa, ndipo nthaŵi zambiri apolisi anafunikira kuitanidwa. Mpainiyayo anagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu amphamvu kuwaphunzitsa iwo mmene angasonyezere chikondi chaumulungu mu ukwati wawo. Mwamsanga njira zakale ndi zizoloŵezi zinayamba kusintha. Onse aŵiri anakhala opezeka pa msonkhano okhazikika, ndipo mkhalidwe wachimwemwe koposa unafalikira panyumbayo. Mwamunayo analeka kusuta fodya ndipo tsopano waloŵa mu Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki. Mkaziyo tsopano ali wofalitsa wobatizidwa.

Umodzi wa banja unafikiridwa mwa kusonyeza chikondi, chipatso cha mzimu wa Mulungu.

Britain

◻ Chokumana nacho chochokera ku Britain chimachitira chitsanzo mmene Yehova amadalitsira mwamuna yemwe amasonyeza chikondi, kuleza mtima, ndi chipiriro m’kuchita ndi mkazi wake. Pamene mwamunayo ankabwera m’chowonadi zaka 12 zapitazo, chitsutso choipa cha mkazi wake chinamtsogolera mkaziyo kupeza chisudzulo cha lamulo. Ngakhale kuli tero, mwamunayo anapitiriza kusonyeza kwa mkaziyo kukoma mtima, kutsimikizira kuti iye anali wosamaliridwa mwa chuma, kuchita ntchito zazing’ono kaamba ka iye pa maziko okhazikika. Pambuyo pa zaka zinayi ndipo mosasamala kanthu za chitsutso chake chakale, mwamunayo anagamulapo kutchula chowonadi kwa mkaziyo kachiŵirinso. Pamene iye analingalira kuti mlongo aphunzire Baibulo ndi iye, mkaziyo anavomereza, zochulukira ku kudabwitsidwa kwa mwamunayo. Potsirizira pake anatenga kaimidwe kake kaamba ka chowonadi ndipo anabatizidwa. Mwamunayo sanataye nkomwe chikondi chake kaamba ka mkaziyo, ndipo pamene iye anatsimikizira kuti wapanga chowonadi kukhala chake, anafunsa mkazi wake kubwereranso mu ukwati ndi iye. Mkaziyo anali wosangalatsidwa, osayembekezera mwamunayo nkomwe kuchita chimenechi m’chiyang’aniro cha mkhalidwe wake woipa wa kumbuyo. Iwo akhala okwatirananso tsopano kwa chifupifupi zaka zisanu ndi zitatu, ndipo onse aŵiri akupita patsogolo bwino lomwe m’chowonadi.

South Pacific

◻ Zoposa zaka 20 zapitazo, mwamuna wachichepere pa chisumbu mu Tuvalu mu South Pacific analembera Watch Tower Society kufunsa kaamba ka mabukhu. Panalibe Mboni pa chisumbucho pa nthaŵiyo. Mosasamala kanthu za icho, iye anaŵerenga mabukhuwo pa iyewini ndi kuzindikira iwo kukhala chowonadi. Mkazi wake, ngakhale kuli tero, anatsutsa mwaukali ku chikhulupiriro chake chatsopano, chotero iye anachileka icho.

Posachedwapa, pamene mabukhu anakhalako mu chinenero cha ku Tuvalu, mkaziyo anafikira kukhala ndi zofalitsidwa zina ndipo anali wokhoza kuziŵerenga izo iyemwini. Iye tsopano anazindikira chowonadi ndipo anadandaula kwa mwamuna wake kuti: “Zaka zonsezi unali ndi kuwunika, koma sunakuike iko powonekera. Nchifukwa ninji sunalongosole mpang’ono pomwe kwa ine chifukwa chimene unakhulupirira kuti Mboni zinali zolondola?” Tsopano ogwirizana m’chowonadi cha Baibulo, okwatirana aŵiri amenewa anayamba kuyanjana ndi Mboni.

Pamene ana awo aakazi aŵiri, omwe anali kupita ku sukulu mu Fiji, anabwerera kunyumba, makolowo anadziŵitsa iwo za chigamulo chawo cha kukhala Mboni za Yehova. Iwo analimbikitsa atsikanawo kugwirizana nawo m’phunziro la Baibulo, koma kukudabwitsidwa kwawo, iwo anapeza kuti atsikanawo anali atayamba kale kupezeka pa misonkhano mu Fiji. Banjalo mwachimwemwe linalandira chowonadi pamodzi, ndipo atatewo, amayiwo, ndi mmodzi wa atsikanawo akhala ofalitsa a Ufumu.

Ndi chimwemwe chotani nanga kuwona mmene chowonadi cha Baibulo ndi chikondi chimagwirizanitsira mabanja kuzungulira pa dziko lonse.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena