Kodi Moyo Ngwamtengo Wapatali Motani kwa Inu?
MNYAMATA wina wachichepere anafa mwa kulumpha kuchokera pa chipinda chachisanu ndi chitatu cha nyumba yosanja yaitali. Anali ataŵerenga buku limene linalongosola za imfa ya kudumpha kukhala “yosapweteka kapena yosavutitsa kapena yosachititsa mantha; m’malo mwake, imamveka bwino.” Mlembi wa buku limeneli, lofalitsidwa ku Japan, ananena kuti iye anali kungosonyeza “kudzipha monga chimodzi cha zosankha m’moyo.”
Anthu amene amadzipha si iwo okha amene amasonyeza kusalemekeza moyo lerolino. Nawonso oyendetsa galimoto mosasamala samalemekeza kwambiri moyo. Ena amamwadi moŵa ndi kuyendetsa galimoto, ambiri akumafulumizitsa imfa yawo.
Ena amasonyeza mmene samaŵerengerera moyo wawo kwambiri ndi mmene amakondera kwambiri chisangalalo. Osuta fodya amakana kuleka fodya, ngakhale kuti kusuta fodya kungaphe munthu ndipo kwatchedwa kuti kudzipha kwapang’onopang’ono. M’malo mwa kusunga chiyero m’dziko lopenga ndi chisembwere lino, ambiri amalondola njira yauchiwerewere imene kaŵirikaŵiri imatsogolera ku imfa.
Mosazindikira nkomwe, ena amadzichotsera zaka za moyo mwa kudyetsa, kumwetsa, kulimbitsa thupi kosakwanira, ndi kufunafuna chikondwerero. Mlembi Wachijapani Shinya Nishimaru anachenjeza kuti: “Zizoloŵezi za kudya kosalamulirika zimasokoneza kugwira ntchito kwa thupi, ndipo kufunafuna kwambiri ubwino ndi chisangalalo kumatsopa nyonga ya anthu.” Ena ali ndi malingaliro ofanana ndi anthu aja a mu nthaŵi zakale amene anati: “Tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa maŵa tidzafa.”—Yesaya 22:13; 1 Akorinto 15:32.
Inde, kusalemekeza moyo nkofala lerolino. Chifukwa chake, kungafunsidwe kuti, Kodi moyo ngwamtengo wapatali motani kwa inu? Kodi moyo uyenera kutetezeredwa mosamalitsa pamtengo uliwonse? Kodi pali kanthu kenanso kamtengo wapatali kuposa moyo wathu womwe ulipowu?