Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 2/1 tsamba 30
  • “Sindinaonepo Zonga Zimenezi!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Sindinaonepo Zonga Zimenezi!”
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 2/1 tsamba 30

“Sindinaonepo Zonga Zimenezi!”

MU 1993 nthambi ya Watch Tower Society ku Argentina inapemphedwa kutumiza nthumwi chikwi chimodzi ku Santiago, Chile, ku Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa “Chiphunzitso Chaumulungu” wamasiku anayi. Imeneyi inali nthaŵi yoyamba imene Mboni Zachiajentina zinaitanidwa kupita monga gulu lalikulu ku msonkhano wa ku dziko lina.a Kodi chotsatirapo chinali nchiyani? Oposa 8,500 anafunsira, mwa amene nthumwi 1,039 zinasankhidwa.

Mabasi okwanira 14 anachitidwa haya kuyenda paulendo umenewu wa makilomita 1,400 kuchokera ku Buenos Aires kufika ku Santiago. Kuona malo okongola kunachititsa ulendowo wa maola 26 kukhala wosangalatsa kwambiri. Podutsa Andes Mountains, nthumwizo zinapyola pafupi ndi Aconcagua, phiri lalitali koposa ku Chigawo Chadziko Chakumadzulo, la mamita 6,960. Zosaiŵalika makamaka zinali kutsika kuloŵa m’Chile panjira yocholima ndi yokhotakhota. Oyendetsa mabasiwo anaomberedwa m’manja kwambiri kwanthaŵi yaitali chifukwa cha luso lawo la kuyendetsa mabasi m’malo ovuta amenewo!

Komabe, zokongola koposa zinali kukapezeka pamsonkhanopo. M’dziko limene muli kulimbana kwa mitundu ndi udani wa mafuko, kunali kotsitsimula chotani nanga kuona khamu logwirizana la opezekapo 80,000 akumaiko 24​—ubaledi wa padziko lonse! Podzionera okha umodzi pakati pa osonkhanawo, ena a oyendetsa mabasiwo anasonyeza chikhumbo cha kuphunzira zambiri ponena za Mboni za Yehova. “Sindinaonepo zonga zimenezi!” wina mwa iwo anatero.

[Mawu a M’munsi]

a Ziletso za boma m’Argentina kuyambira mu 1949 kufikira mu 1982 sizinatheketse zimenezo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena