Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 2/1 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 2/1 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Kodi Afilisti otchulidwa m’Baibulo anali ayani?

Baibulo kaŵirikaŵiri limanena za anthu otchedwa Afilisti, amene anali kukhala m’Kanani pamene anthu akale a Mulungu analanda Dziko Lolonjezedwa. Kwa nthaŵi yaitali, Afilisti akale ameneŵa anatsutsa anthu a Mulungu, monga momwe imasonyezera nkhani ya kulimbana kwa Davide ndi Goliati, chimphona ndi ngwazi Yachifilisti.​—1 Samueli 17:1-3, 23-53.

Baibulo limasonyeza kuti Afilisti akalewo anachokera ku Kafitori kummwera koma chakumadzulo kwa gombe la Kanani. (Yeremiya 47:4) Kodi Kafitori anali kuti? The International Standard Bible Encyclopedia (1979) imati: “Ngakhale kuti umboni sumapereka yankho lokwanira, akatswiri amakono amatchula chisumbu cha Krete (kapena Krete ndi Aegean Isles, imene miyambo yake ili yofanana) kukhaladi malo amenewo.”​—Voliyumu 1, tsamba 610.

Mogwirizana ndi zimenezi, New World Translation of the Holy Scriptures imati pa Amosi 9:7: “‘Kodi simuli ngati ana a Kusi kwa ine, ana a Israyeli inu?’ atero Yehova. ‘Kodi sindine amene ndinatulutsa Israyeli iyemwini ku dziko la Igupto, ndi Afilisti ku Krete, ndi Suriya ku Kiri?’”

Sizidziŵika pamene anthu akunyanja akale ameneŵa anasamuka ku Krete kupita kuchigawo cha Kanani chimene chinatchedwa Philistia, gombe lakummwera koma chakumadzulo pakati pa Yopa ndi Gaza. Anthu ameneŵa akuchita ngati kuti analimo kale m’dera limeneli la madambo lakugombe m’masiku a Abrahamu ndi Isake.​—Genesis 20:1, 2; 21:32-34; 26:1-18.

Afilisti anapitiriza kukhala chisonkhezero champhamvu m’deralo patapita nthaŵi yaitali kuchokera pamene Israyeli analoŵa m’dzikolo limene Mulungu adawalonjeza. (Eksodo 13:17; Yoswa 13:2; Oweruza 1:18, 19; 3:3, 4; 15:9, 10; 1 Samueli 4:1-11; 7:7-14; 13:19-23; 1 Mafumu 16:15) Kufikira ngakhale mu ulamuliro wa Uziya, mfumu ya Yuda, Afilisti anakhalabe m’midzi yawo ya Gati, Yabine, ndi Asidodi. (2 Mbiri 26:6) Midzi yawo ina yotchuka m’mbiri ya Baibulo inali Ekroni, Askeloni, ndi Gaza.

Alexander Wamkulu anagonjetsa mudzi wa Afilisti wa Gaza, koma m’kupita kwa nthaŵi, Afilisti mwachionekere analeka kukhala mtundu wapawokha. Profesa Lawrence E. Stager analemba mu Biblical Archaeology Review (May/​June 1991) kuti: “Afilisti nawonso anatengedwa undende ku Babulo. . . . Komabe, palibe cholembedwa chonena za zimene zinachitikira Afilisti otengedwa undendewo. Awo amene angakhale atatsala m’Askeloni pambuyo pa kulakika kwa Nebukadinezara mwachionekere anataya mtundu wa fuko lawo. Iwo angozimiririka m’mbiri.”

Dzina lamakono la Palestina latengedwa ku mawu Achilatini ndi Achigiriki, amene amafikanso ku liwu Lachihebri la “Philistia.” Matembenuzidwe ena a Baibulo m’chinenero cha Chiarabu amagwiritsira ntchito liwu lotanthauza “Afilisti” limene limasokonezedwa mosavuta ndi liwu la Apalestina amakono. Komabe, Today’s Arabic Version imagwiritsira ntchito liwu losiyana la Chiarabu, motero ikumasiyanitsa Afilisti akale ndi Apalestina amakono.

[Chithunzi patsamba 31]

Mabwinja a ku Askeloni

[Mawu a Chithunzi]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena