Luntha la Kulenga—mphatso yaikulu yochokera kwa Mulungu
YEHOVA amakondwera ndi ntchito zake za kulenga. (Salmo 104:31) Chikhutiro chachikulu chimene amapeza m’ntchito ya kulenga chasonyezedwa pa Genesis 1:31: “Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.”
Yehova sanasunge kwa iye yekha chimwemwe chimenechi. Anapatsa Yesu mwaŵi wa kukhala mtumiki, kapena njira, mwa imene zinthu zonse zinalengedwera. (Yohane 1:3; Akolose 1:16, 17) Monga “mmisiri,” Yesu ‘anakondwera pamaso [pa Yehova] nthaŵi zonse.’—Miyambo 8:30, 31.
Koma luso la kulenga silili kumwamba kokha. “Lili m’chibadwa cha mtundu wa anthu,” analemba motero Eugene Raudsepp m’buku lake lakuti How Creative Are You? Zimenezi si malunji, pakuti munthu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Genesis 1:26) Chotero Yehova wapatsa mtundu wa anthu maluso okhutiritsa a kulenga.—Yakobo 1:17.
Chotero, nkosadabwitsa kuti Baibulo limathokoza kuimba, kuvina, kuomba, kuphika, umisiri, ndi ntchito zina za luntha. (Eksodo 35:25, 26; 1 Samueli 8:13; 18:6, 7; 2 Mbiri 2:13, 14) Bezaleli, mmisiri, anagwiritsira ntchito luso lake “kulingirira [zipangizo, NW]” zothandiza pomanga chihema. (Eksodo 31:3, 4) Mbusa Yabala angakhale ndiye amene anayamba kupanga hema, chipangizo chopangidwa mwaluntha choyenerera umoyo wosamukasamuka. (Genesis 4:20) Davide sanali chabe woimba ndi wopeka nyimbo, komanso anali mmisiri wa ziŵiya zatsopano zoimbira. (2 Mbiri 7:6; Salmo 7:17; Amosi 6:5) Miriamu angakhale analinganiza kuvina kwa chisangalalo kokondwerera chilanditso chozizwitsa cha Aisrayeli kupyola pa Nyanja Yofiira.—Eksodo 15:20.
Kaŵirikaŵiri luntha la kulenga nlofunika kwambiri pa kuchirikiza kulambira koona. Yesu anagwiritsira ntchito luntha la kulenga kupeka mafanizo ndi maphunziro a zochitika popereka uthenga wake. Otsatira ake nawonso amalimbikitsidwa “kuchititsa m’mawu ndi m’chiphunzitso.” (1 Timoteo 5:17) Inde, ntchito yawo yolalikira sili mwambo chabe. Lili luso limene limafuna njira zophunzitsira za luntha la kulenga. (Akolose 4:6) Zimenezi nzofunika kwambiri makamaka pophunzitsa ana a munthuwe.—Deuteronomo 6:6, 7; Aefeso 6:4.
Motero, Yehova amagaŵana ndi ena chimwemwe chimene kulenga kumampatsa. Ha, imeneyo ndi mphatso yaikulu chotani nanga!