Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 4/15 tsamba 7-9
  • Chimwemwe Chikuyembekezera Aja Amene Apeza Choonadi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimwemwe Chikuyembekezera Aja Amene Apeza Choonadi
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ziphunzitso Zoona za Baibulo Zimapatsa Chimwemwe
  • Makhalidwe Oona a Baibulo Amadzetsa Chimwemwe
  • Chimwemwe Chiyenera Kuchikulitsa
  • Zimene Mungachite Ngati Mwamuna Kapena Mkazi Wanu Ali Wosakhulupirika
    Nsanja ya Olonda—2010
  • ‘Pitirizani Kuyenda M’choonadi’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Pezani Chimwemwe mwa Kukhala Wopatsa!
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Chimwemwe Ndi Khalidwe Limene Mulungu Amapereka
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 4/15 tsamba 7-9

Chimwemwe Chikuyembekezera Aja Amene Apeza Choonadi

MU KACHIPINDA kake ka m’denga, mwamuna wina Wachifinishi anapezamo buku lakuti The Divine Plan of the Ages. Panthaŵi yomweyo iye anayamba kuliŵerenga, ndipo posapita nthaŵi anati payekha, ‘Ichi ndicho choonadi; ichi ndicho choonadi.’ Potsika m’kachipinda ka m’dengako, anauza mkazi wake kuti, “Ndapeza chipembedzo choona.”

Njira imene mwamunayu anapezera choonadi ndi yachilendo, koma Mboni za Yehova zambiri zingasimbe za chochitika chofanana. Zonse zingakuuzeni za chimwemwe chimene chimadza ndi kupeza choonadi. Zochitika zotsatirazi zimasonyeza zimenezo.

Ziphunzitso Zoona za Baibulo Zimapatsa Chimwemwe

Margarita Königer anakulira ku Munich, mu Germany, mkati mwa Nkhondo Yadziko II. Kuona nyumba zikuphulitsidwa ndi kutenthedwa ndi mabomba kunali kozoloŵereka kwa iye. Mlongo wake anamwalira m’nkhondoyo. Atapita kumapemphero a tchalitchi cha Katolika, anali kumva mapemphero operekedwa kaamba ka asilikali Achijeremani ndi führer, Hitler. Ndipo pambuyo pa nkhondoyo, analipiriridwa ndi boma kuti apite ku koleji ku United States monga mbali ya programu yosinthana ophunzira sukulu. Iye anaona kuti anthu anali aubwenzi kwa iye, motero anazizwa kuti nchiyani chimene chinasonkhezera anthu kusakhulupirirana ndi kudana panthaŵi ya nkhondo, amene chikhumbo chawo chachibadwa chili kukhala pamodzi mwamtendere. Atabwerera ku Munich, anakumana ndi Mboni za Yehova, ndipo mwa kuphunzira nawo Baibulo, anapeza mayankho pa mafunso akewo. Iye anati: “Ndinasonyezedwa m’Baibulo kuti magulu a mizimu yoipa akuloŵetsedwamo . . . Baibulo limawatcha ‘olamulira a dziko,’ ndipo, kwenikweni, limati Satana ‘akunyenga dziko lonse.’  . . . Mwa kuona machitidwe opanda umulungu ndi audyerekezi a mitundu ndi anthu, yankho limeneli lili lanzeru ndi lokhutiritsa chotani nanga!”​—Aefeso 6:12; Chivumbulutso 12:9.

Margarita akupitiriza: “Ndinakhala ndi chimwemwe chachikulu pamene ndinadziŵa za makonzedwe a Mulungu othetsera mavuto a dziko lapansi. Sikudzakhala mwa lingaliro la munthu ayi, kapena mwa boma laumunthu, monga momwe aphunzitsi a dziko asonyezera. M’malo mwake, Baibulo limasonyeza kuti boma latsopano lakumwamba lidzayendetsa zinthu pa dziko lapansi. . . . Yesu Kristu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: ‘Ufumu wanu udze.’ . . . Ndinayamba kuona kuti ufumu umenewu uli boma lenileni ndi kuti ndilo njira yokha yopezera mtendere weniweni wa padziko lonse.” Kwa zaka pafupifupi 30, Margarita watumikira monga mmishonale m’maiko asanu a mu Afirika​—akumathera zaka 19 zapitazo pa kukalengeza choonadi kwa anthu odzichepetsa a ku Ouagadougou, Burkina Faso.

Si Margarita yekha amene wakhala ndi chochitika chotere. Ambiri achita mofananamo pamene aona kuti atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu a kumbali zonse ziŵiri pankhondo amapepherera chilakiko kwa Mulungu. Anthu oona mtima amaona nzeru yake ya malongosoledwe a Baibulo akuti Mulungu alibe chochita ndi nkhondo za anthu koma kuti izo zimachitika chifukwa chakuti “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” Ofunafuna choonadi ameneŵa amaphunzira kuti Akristu oona sayenera kukhala “a dziko lapansi” koma ayenera kukhala achete pankhani zimenezi. Poona kuti Mboni za Yehova zatenga kaimidwe kotere, okondwerera achatsopano ameneŵa amakhutiritsidwa kuti apeza choonadi. Otereŵa amakula m’chiyembekezo ndi chimwemwe pamene apeza chidziŵitso chowonjezereka chonena za chifukwa chake Mulungu walola kuipa ndi mmene posachedwapa adzabweretsera mikhalidwe yamtendere ndi yolungama pa dziko lapansi kupyolera mu Ufumu wake.​—1 Yohane 5:19; Yohane 17:16; Mateyu 6:9, 10.

Makhalidwe Oona a Baibulo Amadzetsa Chimwemwe

Daniel Rosero wa ku Ecuador anaona kuti moyo unali wopanda pake, motero anayamba kumwa. Kutchalitchi chake kumene anali kupita anamuuza kuti chokha chimene anali kuyembekezera ndicho imfa ndi moto wa helo. Poyankha iye anati, “Popeza kuti ndidzapsa, lekani ndiziukhuta!” Anali ndi banja la anthu asanu ndi atatu limene sanali kusamalira, ndipo nthaŵi zonse anali kumenyana ndi mkazi wake, Delia. Nthaŵi ya kusintha kwa zinthu inafika mmaŵa wina pa Sande pamene Mboni za Yehova zinawachezera ndi kuyamba nawo phunziro la Baibulo. Panthaŵi yoyamba pamene Daniel anapezeka pa msonkhano wadera wa Mboni za Yehova, anazindikira kuti anapeza choonadi. Iye akuti: “Gululi linandichititsa kaso kwambiri. Anthu anali kumvana bwino, anthu ambirimbiri pamodzi. Ndinali kuchimva chikondi pakati pa khamulo. Panalibe wosuta. Panalibe wolankhula mawu oipa. . . . Ndikukumbukira kukhala ndikulingalira kuti, ‘Ichi ndicho choonadi!’ Sikunali kuwopa imfa kapena kuwopa mapeto a dziko kumene kunandisonkhezera. Chinali chiyero cha gululo.”

Banja lonse la a Rosero linakhala Mboni za Yehova. Moyo wa banja lawo ndi mkhalidwe wawo wa ndalama unawongokera pamene anagwiritsira ntchito makhalidwe a Baibulo. Delia Rosero akuti: “Ndithokoza kwenikweni choonadi cha Baibulo. Sindidziŵa kuti ana anga akanakhala otani popanda Mawu a Mulungu. Onse asanu ndi aŵiri ngobatizidwa ndi okhazikika. Choonadi chandipatsa moyo watsopano kwenikweni, chimwemwe chatsopano.”

Chochitika cha banja la Rosero sichili chokha. Ambiri m’nthaŵi yathu amasautsika ndi mavuto. Chimodzi cha zochititsa zake nchakuti miyezo ya makhalidwe yoperekedwa m’Baibulo siimatsatiridwanso ndi ambiri, monga momwe inatsatiridwira ndi mibadwo yakumbuyoku. Zipembedzo zambiri zatsatiranso mkhalidwe umenewu, mwa kulolera kapena chifukwa cha kulingalira kuti pamene nthaŵi zikusintha makhalidwe akale samagwiranso ntchito. Chotero, mofanana ndi ena, banja la a Rosero linapupulika popanda chitsogozo cha Baibulo. Komabe, pamene anthu odzichepetsa oterowo azindikira lingaliro la Mulungu la makhalidwe ndi moyo wa banja, mosataya nthaŵi amagwiritsira ntchito zimene amaphunzira. Kuchokera m’nkhani zawozi, tingaone zotulukapo zabwino za kuchita motero.

Chimwemwe Chiyenera Kuchikulitsa

Komabe, izi sizitanthauza kuti Mkristu adzakhala wokondwa nthaŵi zonse. Ndithudi, zovuta zimene anthu onse amakumana nazo, zonga ulova, matenda, ndi imfa, zimagweranso Akristu. Akristu ayeneranso kumenya nkhondo yolimbana ndi kupanda ungwiro kwawo ndi zifooko zawo. Nkhani ya m’Baibulo imanena kuti Loti ‘analema mtima ndi mayendedwe onyansa a oipa’ a mzinda wa Sodomu. Akristu okhulupirika sangaleke kumva mofananamo pamene akuona mikhalidwe yonyansa yofalikirayo.​—2 Petro 2:7, 8.

Komabe, aja amene apeza choonadi ali ndi mwaŵi. Mwachitsanzo, wokhulupirira amene akulira wina amene wamwalira sayenera ‘kulira monga otsalawo amene alibe chiyembekezo.’ Chisoni chake sichidzakhala chopanda malire. Zilinso motero ndi mavuto ena. Munthu amene wapeza choonadi amadziŵa kuti zovuta za nthaŵi ino zili zakanthaŵi chabe. Chiyembekezo chimapeputsako zinthu popirira zovuta. Njira ya moyo yolinganizika imathandizanso.​—1 Atesalonika 4:13.

Paulo anapatsa Akristu chilimbikitso ichi: “Kondwerani mwa Ambuye nthaŵi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.” (Afilipi 4:4) Izi zimasonyeza kuti pamene kuli kwakuti tonsefe tikhoza kupeza chimwemwe, kulinso kotheka kusakhala nacho. Nkhaŵa za dziko lakale lino zingakhaledi chopinga. Ndiponso, Baibulo limatiuza kuti tifunikira kukulitsa chimwemwe, chimodzi cha zipatso za mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Ngati mupitirizabe kupeza chidziŵitso cha choonadi ndi kukumbukira za chuma chauzimu chimene icho chakupatsani ndipo chikukupatsanibe, chimwemwe chanu sichidzazilala. Chidzakulirapo nthaŵi zonse pamene tikuyandikira nthaŵi imene Mulungu ‘adzapukuta misozi yonse’ pamaso pa anthu ndipo pamenepo “sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.”​—Chivumbulutso 21:4.

[Zithunzi patsamba 8]

Ambiri amakondweretsedwa ndi chimwemwe ndi kulinganizika kwabwino pa misonkhano ya Mboni za Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena