Kukwera Phiri Lalitali Kuposa Mapiri a Himalaya
MAPIRI A HIMALAYA! Kodi mumaganiza chiyani mukamva mawuwo? Nsonga za mapiri zowopsa, zamadzi oundana zokhala ndi mikuntho yamphamvu? Mzimu wachipambano, mutaimirira pamwamba pa phiri lalitali koposa pa dziko lapansi? Kwa ife ambiri, kukwera Mount Everest, mu Himalaya Mountains ku Nepal, nkosatheka. Komabe, lerolino anthu ambiri ku Nepal akukwera phiri lalitali kuposa Mapiri a Himalaya! Tisanadziŵe zambiri za ulendo umenewu wokwera phiri lalikululo, tiyeni tipende Ufumu wa Nepal waung’onowo koma wokongola.
Nepal—Ufumu wa Mapiri
Ufumu wa Nepal ngwapadera chifukwa chakuti uli umodzi wa maufumu oŵerengeka otsala padziko lonse ndiponso chifukwa chakuti suuli ufumu wandale, koma wachipembedzo. Nepal ndiye boma lokha la Chihindu padziko lonse. Unyinji wa nzika zake 20 miliyoni ndi Ahindu. Komabe, anthu ake anachokera m’mafuko osiyanasiyana. Amene akhala kudera lakumpoto lamapiri makamaka ali mbadwa za Atibeti ndi Aburma, pamene kuli kwakuti anthu okhala kummwera m’madambo makamaka ali mbadwa za Aindiya ndi Aaryan. Chinepali ndicho chilankhulo cha boma cha dzikolo ndi chilankhulo cha anthu ake pafupifupi 60 peresenti. Otsalawo amalankhula zilankhulo za mafuko ena zoposa 18.
Nepal ali ndi maonekedwe ochita ngati rectangle, makilomita 880 kuchokera kummaŵa mpaka kumadzulo ndi makilomita 200 kuchokera kumpoto mpaka kummwera. Mapiri a Himalaya ochititsa kakasi amenewo, amene amapanga malire akumpoto, amaphatikizapo Mount Everest, phiri lalitali koposa padziko lonse la mamita 8,848, ndi mapiri ena asanu ndi atatu oposa mamita 8,000. M’chigawo chapakati cha Nepal muli mapiri aafupipo ndi nyanja ndi zigwa. Kummwera kwenikweni, kumalire ndi India, kuli Tarai wachonde, chigawo chachikulu chaulimi.
Kathmandu, likulu lake, amene ali m’chigawo chapakati, amakondedwa kwambiri ndi alendo odzaona malo. Ali ndi ndege za maulendo odutsa pamwamba pa mapiri aataliwo, maulendo opita ku mapaki a zinyama, ndi malo ena ambiri okaona. Nepal nthaŵi zina amatchedwa chigwa cha milungu chifukwa chakuti chipembedzo nchofunika kwambiri m’moyo wa anthu ake. Ndiponso chipembedzo ndicho chifukwa china chimene anthu ambirimbiri padziko lonse akupitira ku “phiri” lalitali kuposa Mapiri a Himalaya.
Pafupifupi zaka 2,700 zapitazo, mneneri Wachihebri Yesaya anauziridwa kulosera kuti “masiku otsiriza . . . phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri . . . Anthu ambiri adzamka, nati, Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova . . . Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yesaya 2:2, 3) Panopa kulambira Yehova koyera kokwezekako, Mlengi ndi Mfumu ya chilengedwe chonse, kukufaniziridwa ndi phiri, lokwezeka pamwamba pa mitundu ina ya kulambira konga mapiri. Ndiko nkhani ya ntchito ya maphunziro a padziko lonse amene akuthandiza anthu anjala ya choonadi kuphunzira za njira za Yehova. Kodi ntchito imeneyi inayamba bwanji ku Nepal?
Chiyambi Chochepa
Msilikali wina wa British Army m’Nkhondo Yadziko II anali kufunafuna chipembedzo choona. Makolo ake, Achinepali ndiponso Ahindu, anakhala Akatolika. Pamene anali kukula, anaona kupanda pake kwa kupembedza mafano, anakana ziphunzitso zonga cha moto wa helo, nayamba kupenda zikhulupiriro za matchalitchi Achiprotesitanti. Koma sanakhutire nazo.
Atagwidwa undende ndi Ajapani m’Burma, yemwe panthaŵiyo anali Rangoon, msilikali ameneyu anapemphera kuti apulumuke nsautso za mumsasa wachibalo kuti akapitirize kufunafuna kwake kulambira koona. Pambuyo pake, anathaŵa omgwira ake ndipo anathandizidwa ndi mphunzitsi wina amene m’nyumba mwake anapezamo kabuku kakuti Where Are the Dead?, kolembedwa ndi J. F. Rutherford. Pozindikira choonadi, iye mofunitsitsa anavomera kuphunzira pamene Mboni za Yehova zinamfikira ku Rangoon mu 1947. M’miyezi yoŵerengeka, iye anabatizidwa, posapita nthaŵi nayenso mkazi wake wachichepere anabatizidwa. Iwo anasankha kubwerera ku India, nakakhala kwawo ku Kalimpong, kumapiri akumpoto koma cha kummaŵa. Ana awo aŵiri anabadwira ndi kuphunzira kumeneko. M’March 1970, anasamukira ku Kathmandu.
Malamulo a Nepal analetsa kutembenuza anthu. Aliyense wopezedwa akulalikira chimene anayesa chipembedzo chachilendo anali kuponyedwa m’ndende kwa zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo munthu amene anakhala wa chipembedzo chotero anali kuweruzidwa kukhala zaka zitatu m’ndende ndi kulipiritsidwa faindi yaikulu. Chotero umboni unayenera kuchitidwa mosamala. Utumiki wa kunyumba ndi nyumba unatanthauza kufika panyumba ina, ndiyeno kuchoka kupita kudera lina ndi kufika panyumba ina kumeneko. Mwachionekere, umboni wamwamwaŵi unathandiza kwambiri pa kufalitsa uthenga wabwino.
Zotulukapo zake zinali zochedwa. Ndi anthu pafupifupi mamiliyoni khumi, mundawo unaoneka kukhala wolefula kwambiri. Mbewu za choonadi zinabzalidwa pamene banja limeneli lokha linachitira umboni kwa mabwenzi, achinansi, eni ntchito, ndi antchito anzawo. Iwo nthaŵi zonse anali kuchitira misonkhano m’nyumba mwawo ndipo ankaitanira okondwerera kudzagwirizana nawo. Potsirizira pake, m’March 1974, pambuyo pa zaka zinayi za kuwoka ndi kuthirira kosaleka, chipatso choyamba m’Nepal chinaonekera—ndipotu chinachokera kosayembekezera!
Atafika panyumba ina, wofalitsa analankhulana ndi mwamuna wina wachuma amene anali mlembi kwa wam’banja lachifumu. “Lankhulani ndi mwana wanga wamwamuna,” mwamunayo anatero. Mwanayo anavomera kuphunzira Baibulo. M’kupita kwa nthaŵi anasintha ntchito yake, popeza anali kugwira ntchito m’nyumba ya juga. Atate wake, Mhindu wodzipereka, anamtsutsa. Komabe, mnyamata ameneyu anaima kumbali ya Yehova. Chotulukapo chake? Atate wake anadzasiya kumtsutsa, ndipo kagulu ka achibale ake apafupi kanalandira choonadi cha Baibulo. Iye tsopano akutumikira monga mkulu mumpingo Wachikristu.
Kuti akhale olimba mwauzimu ndi kulabadira lamulo la Malemba la kusaleka kusonkhana kwawo pamodzi, a kagulu kakang’ono kameneko ku Kathmandu anali kuchitira misonkhano m’nyumba nthaŵi zonse. Koma abalewo anaphonya kwambiri misonkhano yaikulu. Amene anakhoza anapita ku India ku misonkhano—ulendo wautali ndi wokwera mtengo wodutsa mapiri.
Inali nthaŵi yosangalatsa chotani nanga pamene programu yonse ya msonkhano wachigawo inachitikira m’nyumba imene anachitira misonkhano! Talingalirani abale anayi, kuphatikizapo wa panthambi ya India, akumasamalira programu yonseyo! Ngakhale seŵero la m’Baibulo linachitika. Motani? Masilaidi anatengedwa pa kuyeseza komaliza ku India. Ku Nepal, masilaidi ameneŵa anaonetsedwa pamalo oonetsera, limodzi ndi mawu apatepi. Omvetsera anawakonda. Kodi omvetserawo anali angati? Anthu 18!
Chithandizo chakunja pa ntchito yolalikira chinali chochepa. Ntchito ya umishonale inali yosatheka, ndipo kunali kovuta kwa alendo kulembedwa ntchito. Komabe, Mboni ziŵiri Zachiindiya zinapeza ntchito ku Nepal panthaŵi zosiyana, zikumakhala zaka zingapo ku Kathmandu ndi kuthandiza kulimbikitsa mpingo wopangidwa chatsopanowo. Pofika 1976 munali ofalitsa Ufumu 17 m’Kathmandu. Mu 1985 abale anamanga Nyumba Yaufumu yawoyawo. Itatha, misonkhano yachigawo ya pachaka, limodzi ndi misonkhano ina, inayamba kuchitikira mmenemo nthaŵi zonse. Nyumbayo inalidi malo a kulambira koyera m’gawo lakutali lamapiri limenelo.
Kufutukuka Ngakhale Panali Zovuta
M’zaka zimenezo zoyambirira, ntchito yolalikira, yochitidwa mosamala kwambiri, sinachititse akuluakulu a boma kunyumwa kwambiri. Komabe chakumapeto kwa 1984, ziletso zinayamba kuikidwa. Mbale wina ndi alongo atatu anagwidwa ndi kuikidwa m’lumande kwa masiku anayi asanamasulidwe ndi chenjezo la kusapitiriza ntchito yawo. M’mudzi wina, anthu asanu ndi anayi anagwidwa pamene anali kuphunzira Baibulo m’nyumba zawo. Asanu ndi mmodzi anaponyedwa m’ndende nakhalamo masiku 43. Enanso angapo anagwidwa, koma popanda kuzenga mlandu.
Posachedwapa mu 1989, abale ndi alongo onse pa Phunziro Labuku Lampingo lina anagwidwa, nasungidwa m’lumande masiku atatu, ndi kumasulidwa. Nthaŵi zina, anapemphedwa kusayina chikalata chakuti iwo sadzalalikiranso. Iwo anakana. Ena anamasulidwa atasayina kokha chikalata chakuti anali okonzekera kulandira chilango ngati adzagwidwanso akulalikira.
Ngakhale panali zovuta zotero, abalewo anapitirizabe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mwachangu. Mwachitsanzo, mu 1985, chaka chimodzi kuyambira pamene boma linayamba kuloŵerera m’nkhaniyo, chiŵerengero cha olalikira chinawonjezeka ndi 21 peresenti. Ofalitsa 35 anathera avareji ya maola 20 pamwezi akumalankhula kwa ena za kulambira koyera.
M’kupita kwa nthaŵi, zinthu zinayamba kusintha m’ndale ku Nepal. Akuluakulu a boma anayamba kuzindikira kuti Mboni za Yehova sizinali zowopseza. Kwenikweni, ntchito yawo yophunzitsa Baibulo inachitira anthu zabwino ndi zolimbikitsa, ikumawakhalitsa nzika zabwinopo. Akuluakulu a boma anaona kuti kuona mtima, kugwira ntchito kwambiri, ndi makhalidwe abwino olungama anagogomezeredwa kukhala zofunika zazikulu kwa olambira Yehova.
Umboni wabwino unaperekedwa pamene mkazi wina yemwe anali Mhindu wodzipereka anakhala Mboni nakana kuthiridwa mwazi. Madokotala anadabwa ndi kaimidwe kake kolimba ndi kodziŵa zimene akuchita. Mkazi ameneyu anathandizidwa kuphunzira choonadi ndi brosha lakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! Ngakhale kuti banja lake linamtsutsa ndi kumseka, iye anabatizidwa mu 1990 pamene anatsala pang’ono kukwanitsa zaka 70 zakubadwa. Pambuyo pake anathyoka mwendo ndiponso, pokhala ndi zovuta zina m’thupi, anafunikira opaleshoni yaikulu. Kwa milungu iŵiri iye sanagonjere madokotala ndi achibale pomkakamiza kulandira mwazi. Potsiriza, madokotala anachita opaleshoniyo bwinobwino popanda mwazi. Ngakhale kuti tsopano sangathe kuyenda monga poyamba, mlongo wokhulupirika ameneyu amakhala pachipata cha nyumba yake masiku onse mmaŵa ndipo amapempha odutsa panjira kukhala naye pansi ndi kumvetsera uthenga wabwino wosangalatsa.
Nepal Lerolino
Kodi Nepal lerolino ngwotani? Mboni za Yehova zili ndi ufulu wokulirapo wa kulambira mofanana ndi abale awo padziko lonse. Kuyambira pamene wokwera phiri mmodzi kapena aŵiri anayamba kugwirizana ndi aja amene anali kukwera phiri la kulambira koona, anthu ambirimbiri anena kuti, “Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova.” Pofika 1989 panali avareji ya 43 ya ochita ntchito yolalikira mwezi uliwonse, ndipo 204 anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu chakacho.
Ndiyeno, monga momwe kunalonjezedwera, Yehova anayamba kufulumiza kusonkhanitsidwa kwa ofuna choonadi ku nyumba yake. (Yesaya 60:22) Posachedwapa mpingo wachiŵiri unapangidwa m’Kathmandu, ndipo tsopano kuli timagulu tiŵiri patokha kunja kwa likululo. Mu April 1994, panali Akristu 153 amene anapereka lipoti la ntchito yolalikira—chiwonjezeko cha 350 peresenti pambuyo pa zaka zochepera pa zisanu! Iwo anachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 386 ndi anthu okondwerera. Pa Chikumbutso mu 1994, panali chiŵerengero chosangalatsa cha opezekapo 580. Patsiku la msonkhano wapadera, 635 anadzaza holoyo, ndipo 20 anadzipereka kuti abatizidwe. Chotero kuwonjezeka kwakukulu kwa Mboni za Yehova padziko lonse kukuchitikanso ku Nepal wamng’onoyo.
M’zaka zaposachedwapa mabuku otulutsidwa m’chilankhulo cha Chinepali awonjezeka kwambiri mu unyinji wake, akumathandiza odzichepetsa kugwiritsa choonadi. Otembenuza ophunzitsidwira ku ofesi ya nthambi ya India maluso akutembenuza ndi mmene angagwiritsirire ntchito makompyuta, tsopano akutumikira kwa nthaŵi yonse ku Kathmandu. Pokhala okonzekera kufutukuka, anthu ateokrase okwera mapiri ku Nepal akupita patsogolo!
Kukwera Pamwamba Kuposa Mapiri a Himalaya
Nanunso mungasangalale ndi ulendo wokwera phiri lalitali kuposa Mapiri a Himalaya. Mukachita zimenezo, simudzangogwirizana chabe ndi aja a ku Nepal komanso mamiliyoni “ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Limodzi nawo, mudzakondwa kulangizidwa ndi Mlengi wa mapiri aatali onga aja a ku Nepal. Mudzaona Mlengiyo ‘akuwongola zinthu,’ ndipo mudzakhoza kuyang’ana kutsogolo ku moyo wosatha pa dziko lapansi loyera ndi lokongola.—Yesaya 2:4, NW.
[Mapu patsamba 24]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kathmandu
Mount Everest
[Chithunzi patsamba 25]
Kunja kwa Nyumba Yaufumu ku Kathmandu
[Chithunzi patsamba 26]
Anepali ambiri akupindula ndi maphunziro a Baibulo