Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 8/15 tsamba 23-27
  • Mabanja Okhulupirika Afulumiza Chiwonjezeko ku Sri Lanka

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mabanja Okhulupirika Afulumiza Chiwonjezeko ku Sri Lanka
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Kuchita Ntchito Yaikulu
  • Banja Ladongosolo Limadzetsa Chitamando
  • Chitsutso Chigwirizanitsa Banja pa Kulambira Koona
Nsanja ya Olonda—1995
w95 8/15 tsamba 23-27

Mabanja Okhulupirika Afulumiza Chiwonjezeko ku Sri Lanka

WODZIŴIKA monga Ceylon kufikira 1972, Sri Lanka ndi chisumbu chokongola cha magombe a mitengo ya mingwalangwa, mitandadza ya mapiri, ndi zipululu zazing’ono. Kuzitunda, kuli Adam’s Peak yotalika mamita 2243, imene ili malo opatulika a zipembedzo zinayi zazikulu.a Chapafupipo pali World’s End, mtandadza wa mapiri umene uli ndi therezi locholima mamita oposa 1500. Malowo ali ena a malo okongola koposa a Sri Lanka.

Asri Lanka okwanira 18 miliyoni ali ndi mbiri yosangalatsa ya kumene anachokera. Chiyambire zaka za zana lachisanu B.C.E., anthu a fuko la Indo-European akumpoto kwa India akhala pachisumbucho. Ndiwo Asinihalizi, amene tsopano akupanga zigawo zitatu mwa zinayi za anthu ake. Ndiyeno, kufikira pafupifupi zaka za zana la 12, kunabwera Atamili kuchokera kummwera kwa India; ameneŵa tsopano akukhala makamaka kumpoto ndi kummaŵa kwa chisumbucho. Nawonso Apwitikizi, Adatchi, ndi Abritishi adzetsa masinthidwe chiyambire masiku autsamunda. Ndiponso, amalinyero amalonda ochokera ku ndomo za Arabia ndi Malaya akhala pamodzi ndi anthu akumeneko. Kulinso midzi ya Azungu, Aparsi, Atchayina, ndi ena.

Kuwonjezera pa mafuko osiyanasiyana, chinenero ndi chipembedzo ku Sri Lanka zimasonyezanso kusiyanasiyana kwa anthu ake. Zinenero zazikulu pachisumbucho ndizo Chisinihalizi, Chitamili, ndi Chingelezi. Asri Lanka ambiri amalankhula zinenero ziŵiri mwa zitatuzo. Mafuko nawonso ali ndi mbali yaikulu pa chipembedzo cha anthuwo. Asinihalizi ochuluka ndi Abuda, pamene Atamili ochuluka ndi Ahindu. Ochokera ku Arabia kapena ku Malaya kaŵirikaŵiri amatsatira Chisilamu, ndipo Azungu ambiri amapita kumatchalitchi a Dziko Lachikristu, Achikatolika ndi Achiprotesitanti.

Kuchita Ntchito Yaikulu

Zonsezi zimapatsa Mboni za Yehova ku Sri Lanka ntchito yaikulu. Mbonizo zimalimbikira kutsatira lamulo la Yesu lakuti: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 24:14) Kuwonjezera pa kulimbana ndi zinenero zingapo, ofalitsa uthenga wabwinowo angalankhule ndi Abuda, Ahindu, anthu a m’matchalitchi a Dziko Lachikristu, limodzi ndi okana Mulungu​—pamaola oŵerengeka akulalikira.

Kuti akhale ogwira mtima mu utumiki wawo, ofalitsawo ayenera kunyamula magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ndi mabuku ena a Baibulo m’Chitamili, Chisinihalizi, ndi Chingelezi. Amene ali ndi mphamvu amanyamula ngakhale Mabaibulo azinenero zimenezo. Posachedwa ofalitsawo anakondwera kwambiri pamene mabrosha akuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? ndi Our Problems​—Who Will Help Us Solve Them? ndi trakiti lakuti Kodi Dzikoli Lidzapulumuka? anatuluka m’zinenero zitatu panthaŵi imodzi. Zimenezo zinawonjezera zipangizo za ntchitoyo.

Mbonizo zakhala zikugwira ntchito zolimba chiyambire 1912, pamene Charles Taze Russell, amene anali pulezidenti wa International Bible Students Association panthaŵiyo, anachezera Ceylon panthaŵi yaifupi chabe. Komabe, chiwonjezeko chachikulu chinadzafika ndi kubwera kwa omaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower mu 1947. Chiyambire nthaŵiyo, ofalitsa ku Sri Lanka aona zotulukapo zabwino za ntchito yawo yolalikira. Mu 1994 ofalitsa Ufumu 1,866 anachititsa avareji ya maphunziro a Baibulo apanyumba 2,551 mwezi uliwonse. Ndipo chiŵerengero cha 6,930 opezeka pa Chikumbutso chinali kuŵirikiza pafupifupi kanayi chiŵerengero cha ofalitsa m’mipingo yonse. Linali dalitso lalikulu chotani nanga!

Poyerekeza ndi maiko ena, chifutukuko ku Sri Lanka chingaoneke ngati chikuchedwa. Chochititsa china chikuoneka kukhala chigwirizano cholimba cha m’mabanja. Komanso, zimenezo zingakhale zaphindu. Pamene kazembe Wachiroma Korneliyo analandira choonadi, banja lake linakhala kumbali yake. (Machitidwe 10:1, 2, 24, 44) Buku la Machitidwe limatchulanso mabanja ena olimba Achikristu, kuphatikizapo la Lidiya, Krispo, ndi mlonda wa Paulo ndi Sila m’ndende.​—Machitidwe 16:14, 15, 32-34; 18:8.

Ndithudi, chigwirizano cholimba cha m’mabanja chingakhale ndi zotulukapo zabwino ngati pali dongosolo labwino ndi chipiriro cholimba. Poganiza za mawu a Yesaya 60:22, mmishonale wanthaŵi yaitali Ray Matthews akuti: “Zikuoneka kuti Yehova akufulumiza zinthu panthaŵi yake tsopano, osati chabe mwa anthu payekhapayekha komanso m’mabanja.”

Banja Ladongosolo Limadzetsa Chitamando

Ndithudi mabanja okhulupirika motero aliko ku Sri Lanka lerolino. Mwachitsanzo, kuli banja ladongosolo kwambiri la a Sinnappa lokhala ku Kotahena, chigawo cha Colombo, likulu la Sri Lanka. Ngakhale kuti Marian, mutu wa banjalo anamwalira posachedwa, Annamma mkazi wake, ndi 12 mwa ana awo 15, azaka kuyambira 13 mpaka 33, akupitiriza kutumikira Yehova monga banja. Panthaŵi yolemba nkhaniyi, asanu ndi atatu mwa anawo anali obatizidwa, ndipo atatu anali mu utumiki wanthaŵi yonse, akumatumikira monga apainiya okhazikika. Ena atatu analembetsa utumiki waupainya wothandiza panthaŵi ndi nthaŵi. Pakati pa achichepere a banjalo, anayi anali ofalitsa osabatizidwa. Ndiponso, adzukulu anayi, ngakhale kuti anali aang’ono kwambiri, anali kuphunzira Baibulo ndi kupezeka pamisonkhano Yachikristu pa Mpingo wa Colombo North wa Mboni za Yehova.

Munali mu 1978 pamene Annamma anamva uthenga wa Ufumu nthaŵi yoyamba pamene analandira kope la Nsanja ya Olonda. Phunziro la Baibulo linayambitsidwa, ndipo atamaliza buku lothandiza kuphunzira Baibulo lakuti Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya, Annamma anapatulira moyo wake kwa Yehova Mulungu nabatizidwa, motero akumaikira chitsanzo choyamba ambiri m’banja lake.

Mofanana ndi mwamuna wankhondo Korneliyo, Annamma ali ndi dongosolo labwino m’banja lake. “Tinali kukonzekera misonkhano Yachikristu ya mpingo ndi yaikulu​—kuwonjezera pa sukulu,” Annamma akukumbukira. “Zovala zinali zovuta, koma pokhala ndi dalitso la Yehova tinakhoza kusoka zovala zatsopano za msonkhano waukulu uliwonse. Banja lonse linkafikapo litavala bwino ndi lokhuta​—ndiponso likumwetulira.”

Ana amakonda kukumbukira dongosolo la banja lawo. Kuti athandize banja lonse kupezeka pamisonkhano Yachikristu, ana okulirapo onse anali kupatsidwa mathayo apadera. Mwachitsanzo, Mangala anali kuchapa zovala, ndipo Winnifreda anali kuzisita. Winnifreda, amenenso anathandiza kuveka ana aang’ono, akuti: “Aliyense anaonekadi bwino pochoka panyumba.”

Panalinso makonzedwe auzimu adongosolo kwambiri. Pushpam mwana wamkazi, amene ndi mpainiya wokhazikika tsopano, akukumbukira kuti: “Tsiku lililonse, banja lathu linali kukonda kuŵerenga Baibulo ndi kupenda lemba la Baibulo latsiku ndi tsiku pamodzi.” Annamma akuwonjezera: “Mwana aliyense ali ndi kope lake la Baibulo, Nsanja ya Olonda, ndi zofalitsa zina. Ndimamvetsera kwambiri ndemanga zawo zonse pamisonkhano. Kutakhala kofunika, ndimakawalimbikitsa ndi kuwawongolera kunyumba. Usiku timakhala pamodzi kumaliza tsiku lathulo ndi pemphero la banja.”

Ana okulirapo amamthandiza kwambiri Annamma pakupereka maphunziro abwino Achikristu ku banja lonse. Komabe, ndandanda yawo yokhala ndi zochita zochuluka simapinga chifuno chawo cha kukauza ena za uthenga wabwino. Onse pamodzi, apabanjalo amachititsa maphunziro a Baibulo apanyumba 57 kwa achinansi awo. Rajan mkamwini akuti: “Banjali limachititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo. Mkazi wanga, Pushpam, wakhala kale ndi mwaŵi wa kuona mmodzi wa ophunzira ake akupatulira moyo wake kwa Yehova.”

Zinabutsa mavuto ku Kotahena pamene banja lalikulu limenelo linachoka m’Tchalitchi cha Roma Katolika. Ngakhale kuti wansembe iye mwini sanafikire banjalo kukafufuza chifukwa chake, anapempha anthu a m’tchalitchi kufunsa. Panatsatira makambitsirano angapo, makamaka a chiphunzitso cha Utatu. Annamma nthaŵi zonse anadalira Yehova ndi Baibulo pochirikiza chikhulupiriro chake. Lemba limene anakonda kwambiri m’makambitsirano ameneŵa linali Yohane 17:3.

Banja la a Sinnappa limasonyeza bwino lomwe kuti dongosolo labwino ndi kuyesayesa kwakhama kungakhale ndi zotulukapo zokhutiritsa. Mwa kuyesayesa kwawo kwachangu, mbadwo watsopano wa ofalitsa Ufumu ukukula, kudzetsa chitamando kwa Yehova.

Chitsutso Chigwirizanitsa Banja pa Kulambira Koona

Banja la a Ratnam limakhala ku Narhenpitya, chigawo china cha Colombo, makilomita angapo kuchokera ku banja la a Sinnappa. Nawonso kale anali Aroma Katolika. Mu 1982, Mboni zomwe zinali mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba zinakumana ndi Balendran mwamuna wa Fatima, mwana wamkazi mkulu pa onse. Banja lonselo linayamba kuphunzitsidwa Baibulo. Posapita nthaŵi ana awo atatu anayamba kufunsa Agogo aakazi a Ignasiamal za dzina la Mulungu. Pamene anawo anapereka yankho lakuti “Yehova,” anadzutsa chidwi cha Agogowo, ndipo anayamba kuphunzitsidwa Baibulo. Pambuyo pake, aŵiri mwa ana awo aakazi, Jeevakala ndi Stella, anayamba kupezekapo paphunzirolo, ndipo pofika 1988 onse atatu anabatizidwa.

Mkati mwa zonsezi, Balendran ndi Fatima anagaŵira choonadi kwa mphwake wina wa Fatima, Mallika, ndi mwamuna wake Yoganathan. Pofika mu 1987 banja limeneli linabatizidwa, ndipo lakhomereza mwa ana awo aŵiri kukonda Yehova komakula. Pushpa, mphwake winanso wa Fatima, anatsatira. Anadzipatulira ndi kubatizidwa mu 1990. Pamene anali ku Tokyo, mwamuna wake, Eka, anali mumpingo Wachingelezi, ndipo Pushpa anathandiza mwana wawo wamng’ono wamwamuna, Alfred, kuleredwa m’njira ya Yehova.

Motero, anayi mwa ana khumi a banja la a Ratnam aima kumbali ya kulambira koona. Nzosangalatsa kuti enanso atatu akupita patsogolo ndithu m’maphunziro awo aumwini a Baibulo. Mwa adzukulu 11, mtsikana mmodzi, Pradeepa, ngwobatizidwa. Ana ena asanu ndi aŵiri akuphunzitsidwa nthaŵi zonse pamaphunziro a Baibulo a banja lawo. Ndiponso, akuchititsa maphunziro a Baibulo apanyumba okwanira 24 kwa achinansi awo ofuna.

Zonsezi sizinali zapafupi kuchitika. Poyamba, banja linali kutsutsa. Atate, a Muthupillai, ndi achimwene awo sanafune aliyense wa pabanja pawo kupita kumisonkhano ku Nyumba Yaufumu kapena kuchita ntchito yolalikira poyera. Pamene kuli kwakuti nthaŵi zina anachita zimenezi pofuna kudzitetezera, a Muthupillai akuwonjezera: “Ndinali wodziperekeratu kwa ‘oyera mtima’ ndipo sindinafune banja langa kusiya Tchalitchi cha Katolika.” Komabe, iwo tsopano akhulupirira kuti banja lawo likulambira Mulungu woona chifukwa chakuti akuona mapindu amene chikhulupiriro chawo chadzetsa ku banja lawo.

Mwachitsanzo, tsiku lina mwini malo amene iwo akukhalapo, Mbuda, anayesa kuwachotsa pamalo ake mwa kugwiritsira ntchito mankhwala. Anafika usiku naika zipatso za lime “zamankhwala” kuzungulira nyumba. Mantha anagwira achinansi okhulupirira malaulo, amene onse anali kuyembekezera tsoka lina lake kugwera banja la a Ratnam. Komabe, pamene Ignasiamal anapeza zimenezo, iye ndi ana anangochotsa zipatsozo mopanda mantha​—ndipo palibe choipa chimene chinawagwera. Kuchita kwawo mopanda manthako kunakhala umboni wabwino m’deralo, kukumachititsa anthu kuwapatsa ulemu kwambiri. Stella anakhoza kuyambitsa maphunziro a Baibulo apanyumba aŵiri chapafupi. Atalimbikitsidwa ndi zimenezi, nayenso mpongozi wawo Nazeera anavomereza phunziro la Baibulo.

Poona madalitso ochuluka amene banja lake lakhala nawo, Ignasiamal akuti: “Ndili wokondwa kwambiri kuona kukula kwauzimu m’banja. Yehova watidalitsa chifukwa chakuti chitsutso chafooka, ndipo umodzi wa banja lathu wakula.”

Mabanja aakulu ameneŵa akhala dalitso chotani nanga. Awonjezera mawu awo pa aja a mabanja aang’ono, mabanja a kholo limodzi, ndi Akristu omwe ali mbeta amene akuyesetsa kufulumiza kulengezedwa kwa uthenga wabwino wa Ufumu mu “dziko loŵala,” malinga ndi tanthauzo la dzinalo Sri Lanka. Pamodzi ndi Akristu anzawo padziko lonse, Mboni za ku Sri Lanka zikuyembekezera mwa chidwi kubwezeretsedwa kwa Paradaiso, amene tingakumbukire ngakhale tsopano lino poona magombe ndi mapiri a Sri Lanka wokongolayo.

[Mawu a M’munsi]

a Phompho lalikulu lili komweko Asilamu amati ndi phazi la Adamu, Abuda amati ndi la Buddha, Ahindu amati ndi la Siva, ndipo nthano za tchalitchi zimati ndi la “Saint” Thomas.

[Zithunzi pamasamba 24, 25]

Ambiri ku Sri Lanka akulabadira ulaliki ndi chiphunzitso Chachikristu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena