Olengeza Ufumu Akusimba
Akristu Oona Adzazunzidwa
CHIYAMBIRE masiku a Abele, atumiki a Yehova ambiri apirira chizunzo chachipembedzo. (Luka 11:49-51) Ndipo nzosadabwitsa, pakuti Baibulo limachenjeza kuti “onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo”! (2 Timoteo 3:12) Motero, lerolino m’maiko oposa 25, Mboni za Yehova nzoletsedwa ndipo zikupirira chizunzo.
M’maiko ena, mmene Mboni za Yehova sizili zongoletsedwa komanso zimazunzidwa ndi anthu achipembedzo, ofalitsa uthenga wabwino oposa 12,000 apitiriza kugwira ntchito mwachangu, akumaphunzira Baibulo ndi anthu oposa 15,000. Zoonadi, ntchito yawo yolalikirayo ikuchitidwa mochenjera. Iwo makamaka amachita misonkhano yawo Yachikristu m’nyumba, ndipo amasamala poitanira anthu okondwerera kumisonkhano imeneyo.
Posachedwapa boma lalola zochita za Mboni pamlingo wokulirapo, zimene tsopano zikuchita mbali yaikulu ya ntchito yawo popanda chidodometso chachikulu. Komabe, magulu osiyanasiyana achipembedzo asonkhezera mavuto.
Mu mzinda wina gulu lachiwawa la anthu otengeka maganizo ndi chipembedzo 200 linapita kunyumba kumene Mboni za Yehova 50 zinasonkhana. Ena a m’gulu lachiwawalo ananyamula miyala namafuula ndi mawu achipembedzo. Cholinga chawo chenicheni chinali cha kuukira Mbonizo ndi kuwononga nyumbayo. Mwachionekere atsogoleri achipembedzo anali kuyang’anitsitsa pa kusonkhanako kwa nthaŵi yakutiyakuti ndipo anayembekezera kupeza nthaŵi yoyenera ya kuukira. Gulu lachiwawalo linali litatsala pang’ono kuloŵa panyumbapo pamene apolisi 15 anafika ndi kulamulira khamulo kumwazika. Zimenezi zinadabwitsa Mbonizo, popeza kuti panalibe aliyense amene anali ndi nthaŵi yodziŵitsa apolisi.
Komabe, nthaŵi zina, otsutsawo akhozadi kuchita zimenezo. Mboni zingapo zaimbidwa mlandu ndi kulangidwa mwa kuikidwa m’ndende. Mlandu wina wa kukhothi unatenga zaka zambiri, ndipo mwachionekere oweruza analibe nawo chidwi. Komabe, chifukwa cha kusonkhezera kwa atsogoleri achipembedzo akumaloko, nkhaniyo inaloŵanso m’khothi, ndipo Mboniyo inalangidwa mwa kuikidwa m’ndende.
Kumalo ena gulu lina la Mboni linasonkhana m’nyumba ina kudzakumbukira Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Pambuyo pake madzulowo apolisi angapo anagwira mwini nyumba ndi mkulu amene anachititsa msonkhanowo. Anamenyedwa kwambiri ku polisi. Kufunsa kwankhanza kunatenga maola angapo. Mmodzi wa Mbonizo anapiriranso chizunzo cha kuviikidwa m’chitsime cha madzi ozizira.
Kodi nchifukwa ninji apolisi anali kuukira motero? Kachiŵirinso gulu la anthu otengeka maganizo ndi chipembedzo, mothandizidwa ndi atsogoleri achipembedzo akumaloko, linasonkhezera zochita za apolisizo. Pambuyo pake mkulu wapolisi anavumbula kuti iye sanavomere za kumanga anthuwo. Anapepesa, ndipo anthu amene anali ndi thayo la kumenyako analangidwa.
Kuzungulira padziko lonse Mboni za Yehova zikupitiriza kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ngakhale poyang’anizana ndi chitsutso cha chiwawa. Amamvera chilangizo cha Yesu chakuti: “Taonani, ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa afisi; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.”—Mateyu 10:16.
[Chithunzi patsamba 31]
Abele anali woyamba kuzunzidwa