Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 9/1 tsamba 32
  • ‘Ha, bwenzi onse akanakhala ngati iwo!’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Ha, bwenzi onse akanakhala ngati iwo!’
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 9/1 tsamba 32

‘Ha, bwenzi onse akanakhala ngati iwo!’

Ameneŵa anali mawu a wolemba nkhani m’danga la m’nyuzipepala ya Luxembourg Letzebuerger Journal. Kodi iye anali kulankhula za ayani?

Iye anali atafika kuchokera ku Poland kumene anapita kukakumbukira chimasuko cha Auschwitz cha chaka cha 50 ndipo anaona kuti panali gulu lina limene linavutika kwambiri kumeneko limene silinatchulidwe. M’nkhani yake ya pa February 2, 1995, anasonyeza gulu limeneli kukhala Mboni za Yehova ndipo analemba kuti: “Ndende yokhaulitsa kwambiri kapena misasa yachibalo, ngakhale kufa mozunzika m’ndende za njala kapena kuphedwa ndi nkhwangwa kapena makako sikunawachititse kukana chikhulupiriro chawo.” Anawonjezera kuti: “Ngakhale alonda a SS ankhanzawo anazizwa ndi kulimba mtima kumene Mboni za Yehova zinafa nako.”

Mboni za Yehova sizinafune kufa. Koma, monga mmene analili Akristu a m’zaka za zana loyamba, zikwi za iwo anasankha kufa m’malo mwa kugonja pa malamulo Achikristu. Chikhulupiriro chotero chinawasonyeza kukhala osiyana kwambiri m’masiku othetsa nzeruwo a Ulamuliro wa Nazi.

Wolembayo anamaliza ndi kuti: “Ha, bwenzi anthu onse akanakhala ngati Mboni za Yehova!” Ngati akanatero, nkhondo yachiŵiri yadziko siikanachitika.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena