Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 11/1 tsamba 2-4
  • Kodi Pali Angelo Pakati Pathu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali Angelo Pakati Pathu?
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchita Chidwi ndi Angelo
    Galamukani!—1999
  • Kupenda Nkhanizo
    Galamukani!—1999
  • Mmene Angelo Angakuthandizireni
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Muli ndi Mngelo Wokuyang’anirani?
    Nsanja ya Olonda—1998
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 11/1 tsamba 2-4

Kodi Pali Angelo Pakati Pathu?

Zinachitika mofulumira. Maganizo atamchulukira ndipo wosaona kumene anali kupita, Marilynn anayenda mosagundira mtima kuloŵa m’njanji. Mwadzidzidzi, anamva mkokomo waukulu. Anatukula mutu, ndi kupeza kuti anali ataima mwachindunji ndi sitima imene inali kubwera! Marilynn anauma thupi, wogwidwa ndi mantha. Sitimayo inali pafupi kwambiri kwakuti anaona maso otuzuka ndi nkhope ya mantha ya woyendetsa wake. Marilynn sanaiŵale zimene zinachitika kenako. “Zinali monga ngati kuti chimphona china chinandikankhira kumbuyo,” iye anatero. “Ndinanyamuka panjanjipo ndi kugwera m’mapulusa a malasha amene anali m’mbali mwake.” Marilynn anadzuka atasupuka pang’ono kuti athokoze womlanditsa wake​—koma palibe aliyense amene analipo! Kodi malingaliro ake anali otani? “Mngelo wanga wondiyang’anira anapulumutsa moyo wanga,” akutero Marilynn. “Kodi akanakhalanso ndani?”

DZIKO lokayikirali mwadzidzidzi likuonekera kukhala likulingalira kwambiri za angelo. M’zaka zaposachedwapa, zolengedwa zakumwamba zakhala nkhani zosonyezedwa pawailesi yakanema, pa mafilimu, ndipo ngakhale seŵero la ku Broadway. Mabuku onena za angelo ali pampambo wa mabuku ogulidwa koposa achipembedzo. Pali makalabu, maseminale, ndi manyuzipepala onena za angelo. Magulu alinganizidwa kuti akuthandizeni​—monga momwe nkhani ina ikunenera​—kusonkhezera “‘kuchirikiza angelo’ kwanu.”

Amene akupezerapo mwaŵi mosavuta pa magulu onena za angelo ndiwo amalonda ofuna phindu amene amasonyeza zinthu zamalonda zosatha. “Chinthu chilichonse chimene pali angelo nchodzetsa phindu,” akutero mmodzi wa eni sitolo wina ku United States. Kuwonjezera pa mabuku ochuluka, iye akundandalika “mafano a angelo, anaphini, zidole, masikipa, zithunzithunzi za pakhoma ndi makhadi amalonje”​—zonsezo zikumabweretsa zimene atolankhani akuzitcha “mapindu akumwamba.”

Koma zimenezi sizili chinthu chopyola chabe, akuterotu ochirikiza za angelo. Kuti achirikize mawu awowo, amapereka maumboni ambirimbiri​—zochitika “zenizeni za m’moyo” ndi angelo. Ena amanena kuti anaona mngelo ali monga munthu. Ena anaona kuunika, anamva mawu, anazindikira za kukhalapo kwawo, kapena anali ndi chisonkhezero chimene akhulupirira kuti chinali chaungelo. Ambiri mofanana ndi Marilynn, amanena kuti mngelo anawapulumutsa.

Kodi nchiyani chimene chikuchitika? “Ndikuganiza kuti mkhalidwe wauzimu ukubukanso,” akutero Joan Wester Anderson, amene walemba mabuku aŵiri ponena za zokumana nazo “zachilendo.” Alma Daniel, amene anathandiza kulembedwa kwa buku lina, akufotokoza mowonjezereka. Iye akunena kuti angelo “tsopano akulangizidwa kudzidziŵikitsa kotero kuti anthu ambiri afikiridwe mitima. Chomwe tikuwaonera kaŵirikaŵiri nchakuti iwo akufuna kuti zinthu zikhale choncho. Akuchita zimenezo.”

Kodi zimenezi zilidi choncho? Kapena kodi pali chinthu china chimene chikusonkhezera anthu kuchita chidwi ndi angelo? Kuti tidziŵe, tifunikira kupenda Mawu a Mulungu. Baibulo lili ndi choonadi ponena za angelo, monga momwe titi tionere.

[Mawu a Chithunzi patsamba 2]

Tsamba 3 ndi 4: The New Tesatament: A Pictorial Archive from Ninteenth-Century Sources, yolembedwa ndi Don Rice/​Dover Publications, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena