Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 12/15 tsamba 22-23
  • Taonani! Nyumba ya Ufumu mu Niue

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Taonani! Nyumba ya Ufumu mu Niue
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Chosankha cha Kupitiriza
  • Mzimu wa Chigwirizano ndi Wochereza
Nsanja ya Olonda—1995
w95 12/15 tsamba 22-23

Taonani! Nyumba ya Ufumu mu Niue

NIUE ndi kachisumbu kakang’ono m’nyanja ya South Pacific, makilomita 2,160 kumpoto koma chakummaŵa kwa New Zealand. Malinga ndi brosha la apaulendo, dzina lakuti Niue limachokera ku mawu aŵiri, Niu, kutanthauza “mtengo wa ngole,” ndi e, kutanthauza “taonani,” kapena “onani.” Broshalo limati: “Malinga ndi nthano, alendo odzakhala a ku Polynesia ananena mawu ameneŵa atangofika pamene anaona mitengo ya ngole yomera m’dzikoli.”

Lerolino, Mboni za Yehova ku Niue nzachimwemwe kuuza alendo kuti: “E! Fale he Kautu ha mautolu!” kutanthauza, “Taonani! Nyumba Yathu ya Ufumu!” Kodi nchifukwa ninji iwo ali ndi chimwemwe chachikulu chotero ponena za nyumba imeneyi? Mboni za Yehova kulikonse nzachimwemwe ponena za Nyumba zawo za Ufumu, makamaka ngati omanga ake anali iwo eniwo. Koma kumanga Nyumba ya Ufumu pa chisumbu chakutali chotero pakatikati pa nyanja yaikulu ya South Pacific ndi nkhani inanso. Ndiponso, chisumbu cha Niue chimangokwanira makilomita 260 mbali zonse zinayi, ndipo pali anthu okwanira 2,300 okha pachisumbu chonse.

Panali nkhaŵa ya amene adzamanga Nyumba ya Ufumuyo. Mpingo umodzi chabe umene uli ku Niue uli ndi Mboni 32 zokha. Zipangizo zonse zofunika koposa, zonga ngati malole, akatapila, ndi makako, ndi za boma. Ndiponso, milimo yonse​—zitsulo, njerwa, milimo yopangira tsindwi, zamagetsi ndi mipope, zolankhuliramo ndi mipando​—mwachionekere inayenera kuchokera ku New Zealand ndi amtengatenga amene amangobwera kamodzi pa milungu isanu iliyonse. Ndiyeno, nthaka ya miyala ya chisumbucho idzachititsa kumanga kukhala kovuta, ndipo nyumbayo idzayenera kumangidwa moti nkuchirimika pa anamondwe a m’madera otentha. Indedi, inali ntchito yolimba kwa aliyense!

Komabe, ntchitoyi inali yosiyana kwambiri ndi zina. Kwa Mboni za Yehova, Nyumba ya Ufumu ndiyo malo a kulambira koona, ndipo iwo amayang’ana kwa Yehova Mulungu kaamba ka chitsogozo ndi thandizo. (Salmo 56:11; 127:1) Abale Achikristu ku New Zealand, kuphatikizapo a mumpingo wolankhula Chiniue ku Auckland, anapereka thandizo ku kagulu ka Mboni ku Niue, akumapereka chichirikizo chochokera pansi pa mtima pantchito ya kumangayo.

Chosankha cha Kupitiriza

Mu June wa 1994 pamalo a chimango cha Nyumba ya Ufumu ku Rotorua, New Zealand, chiitano chinaperekedwa kwa aja ofuna kugaŵanamo mu ntchito ya chimango cha ku Niue. Modabwitsa, abale ndi alongo Achikristu 200 anadzipereka. Mwa ameneŵa, anthu 80 anasankhidwa, kuphatikizapo akalipentala, antchito ya zitsulo, oika mipope ya madzi, opanga tsindwi, oika pulasitala, opaka utoto, odziŵa za magetsi, odziŵa za zolankhuliramo, antchito za konkiri, oyala njerwa, ndi antchito wamba.

Abale anapanga makonzedwe onse ndi kupitiriza, akumadalira pa Yehova. Mmodzi wa akulu aŵiri apampingo ku Niue, wamalonda wakumaloko, anayamba kupanga makonzedwe a kubweretsa katundu wonse wofunika. Makonzedwe a mtengo wapadera wa ulendo wa pandege ndi mtengo wa nyumba zokhala kaamba ka antchito ochokera kunja, amene anadzipereka kulipira zowonongedwa zawo, ndipo masiku a kumanga anasankhidwa. Ntchitoyo inali kudzamalizidwa pamasiku 20, kuyambira pa March 4 mpaka pa March 23, 1995, pamene Nyumba ya Ufumu inali kuzapatuliridwa.

“Ndinada nkhaŵa kwa nthaŵi yoyamba pamene ndinaona malowo,” anatero woyang’anira ntchito, amene anachokera ku New Zealand mlungu umodzi ntchito isanayambe kuti adzalinganize zinthu. “Nthaka yonse ndi miyala yokhayokha. Kudzatenga milungu iŵiri kukumba maziko a m’ngondya.” Koma anali atachepetsa Mboni zakumaloko, anavomereza zimenezo pambuyo pake. “Abale a ku Niue amadziŵa makhalidwe a miyala,” anatero. “Amadziŵa poumenya kotero kuti zidutswa zazikulu zigamuke.” Maziko a m’ngondya anamalizidwa pamasiku aŵiri!

Pa March 4 ndege yoyamba yodzaza ndi Mboni za ku New Zealand inafika, ndipo ntchito ya konkiri inamalizidwa. Pamene magulu a antchito anafika motsatizanatsatizana, mbali zosiyanasiyana za ntchitoyo zinamalizidwa. Ntchito inkayamba ndi nthaŵi ya 7:00 a.m. mwa kukambitsirana lemba latsiku la m’Baibulo mwachidule. Abale ena anagwira ntchito kwa maola 12 m’temperecha yofika pa 36 digiri Celsius. Pomalizira pake, pofika pa March 23, malo ozungulira anali atakongoletsedwa bwino. Chikwangwani chokongola chopangidwa ndi mtengo wa mango chinadziŵikitsa nyumbayo monga “Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova.”

Mzimu wa Chigwirizano ndi Wochereza

Mbali yaikulu imene inachititsa kutheka kwa ntchitoyo inali kugwirizana kwa anthu a ku Niue. Anthu a pamudzipo, atayambukiridwa ndi mzimu wa chochitikacho, anapereka chakudya ndi ndalama. Ambiri anaona kumanga kwa nyumbayo monga ntchito yawo. Akuluakulu a boma ndi amalonda anachita mautumiki ambiri osayembekezereka. Zipangizo zofunika zinalipo, panalinso fakitale yopaliramo matabwa. Kampani yamtengatenga inasintha njira ya sitima yake yapamadzi kuti atsimikizire kuti zinthu zofunika zikufika panthaŵi yake.

Alendo anayamikiradi ntchito yaikulu ndi kuchereza kwa Mboni za ku Niue, zimene zinagaŵana ndi ena nyumba zawo ndi zinthu zawo. “Alongo akumeneko anali abwinodi,” anatero wantchito yomanga wina. Kuwonjezera pa chakudya chamasana chotentha tsiku ndi tsiku, alongo anatipatsa chakudya chofisula chophikidwa mmaŵa uliwonse panthaŵi ya 6:30. Ena anadzuka ndi 4:30 a.m. kukonza chakudya. Wantchito yomanga wina anati: “Ndiganiza kuti tinali kukhala bwino kwambiri kuno ku Niue kuposa mmene timakhalira kunyumba zathu.”

Pa March 10 Niue Star inachita lipoti pa chochitikachi m’nkhani ya patsamba loyamba ya mutu wakuti “Nyumba ya Ufumu Yoyamba mu Niue” ndi chithunzithunzi cha anthu a ku New Zealand ndi a ku Niue akugwira ntchito pamalowo. Inasimba kuti ukulu wa nyumbayo unali mamita 280 mbali zonse zinayi ndipo ikhoza kuloŵa anthu 70 mpaka 100. Nkhaniyo inawonjezera kuti: “Ntchito yake kwenikweni ingathe [pamilungu] iŵiri, koma iyi idzatenga nthaŵi. Pakali pano, masiku aŵiri chabe pambuyo poyamba ntchito, maziko, maferemu a zipupa, phaso ndi tsindwi zaikidwa, nthaŵi yake isanakwane.”

Wamalonda wina ananena kuti akanakondwa kuti anthu onse a pa Chisumbu cha Niue aone ntchitoyo ndi kutengapo phunziro. Iye anati anakhulupirira kuti zimenezi zingaonetse anthu onse zimene zingachitidwe ngati pali chikondi ndi mgwirizano.

Khamu la anthu 204 linabwera pa kupatuliridwa kwake. Chimene chinali chogwira mtima kwambiri kwa onse amene anapezekapo chinali kuyerekezera kumanga Nyumba ya Ufumu akumaimba ndi kuvina kochitidwa ndi abale, alongo, ndi ana a ku Niue. Chiyamiko chinaperekedwa kwa gulu lomanga ndi kwa Yehova, amene mzimu wake unasonkhezera maganizo, mitima, ndi manja kuchita ntchitoyo.​—Yesaya 40:28-31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena