Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 12/15 tsamba 32
  • Mlandu wa Mboni za Yehova Ugamulidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mlandu wa Mboni za Yehova Ugamulidwa
  • Nsanja ya Olonda—1995
Nsanja ya Olonda—1995
w95 12/15 tsamba 32

Mlandu wa Mboni za Yehova Ugamulidwa

PAMBUYO pa kusunthira masiku a kuzenga mlandu kutsogolo mobwerezabwereza, Court of Appeals ku Thessalonica, Greece, pomalizira pake inakumana pa June 8, 1995, kuti limve mlandu wa Mboni za Yehova zinayi zachikazi. Zinapatsidwa mlandu wotani? Kutembenuza anthu, kumene malamulo Achigiriki aletsa kwa zaka zoposa makumi asanu.

Komabe, pofika panthaŵi pamene khoti linakumana, mboni yaikulu ya mlanduwo​—wansembe amene anasumira akazi anayiwo mlandu​—sinalinso ndi moyo. Wansembe wina anayesa kupereka umboni m’malo mwake, koma khoti silinavomereze pempho lake. Motero, si kodabwitsa kuti mlanduwo unatha mphindi 15 zokha! Woweruza anafunsa mboni zina za mlanduwo napeza kuti oimbidwa mlanduwo analibe liwongo la kutembenuza anthu mopanda lamulo. Chigamulocho chikusonyeza kuti makhoti Achigiriki ngofunitsitsa kulemekeza ndi kusunga chigamulo chimene chinaperekedwa mu 1993 ndi European Court of Human Rights.

Zinali zodabwitsa kwenikweni kuona akazi atatu amene anaimira umboni mlanduwo akufikira Mboni zopatsidwa mlanduzo, kuziyamikira ndi mtima wonse. “Tikupepesa kaamba ka zonse zimene zachitika,” mmodzi wa iwo anatero. Anapitiriza kuti: “Sindife amene tinachititsa. Wansembe anatikakamiza kukupatsani mlandu. Tsopano popeza salinso ndi moyo, tikufuna kuti mubwere kumudzi kwathu ndi kunyumba zathu.”

Motero, Yehova waperekanso chipambano chodabwitsa kwa anthu ake ku Greece. Malamulo onena za kutembenuza anthu anapangidwa ku Greece mu 1938 ndi 1939. Mu 1993 European Court of Human Rights inalamula kuti kugwiritsira ntchito lamulo limeneli kuzunzira Mboni za Yehova nkolakwika.​—Onani Nsanja ya Olonda, September 1, 1993, masamba 27-31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena