Chipambano M’khoti
MU April wa 1995, panali chipambano chachikulu m’khoti. Nkhani yake inayamba pa January 28, 1992, pamene Luz Nereida Acevedo Quiles wazaka 24 anagonekedwa m’chipatala cha El Buen Pastor ku Puerto Rico kaamba ka opaleshoni. Atangoloŵa m’chipatalamo, ananena ndi kulemba kuti monga mmodzi wa Mboni za Yehova, sadzavomereza kuikidwa mwazi. (Machitidwe 15:28, 29) Antchito a m’chipatala amene anali okhudzidwa, kuphatikizapo dokotala amene anali kumsamalira anali kudziŵa bwino lomwe za zosankha zake.
Masiku aŵiri pambuyo pa opaleshoni yake, Luz anataya mwazi wochuluka kwambiri ndipo anakhala ndi matenda aakulu a kusoŵa mwazi m’thupi chifukwa cha kuchucha mwazi kumeneko. Dokotala amene anali kumyang’anira panthaŵiyo, Dr. José Rodríguez Rodríguez, anaona kuti njira yokha yomthandizira inali kumuika mwazi. Motero, popanda mwini wake kudziŵa kapena kuloleza, dokotalayo anapempha chilolezo cha khoti cha kuika mwazi Luz.
Ngakhale kuti Luz ankadziŵa bwino lomwe zimene zinali kuchitika ndipo ankatha kudzilankhulira, Dr. Rodríguez Rodríguez analimbikira kunena kuti panalibe nthaŵi yoti apeze chilolezo cha wina aliyense chifukwa cha kukula kwa matendawo. Loya wachigawo chimenecho, Eduardo Pérez Soto, anasaina fomuyo, ndipo woweruza wachigawocho, Wolemekezeka Ángel Luis Rodríuez Ramos, anapereka chilolezo cha khoti choika mwazi.
Motero, pa January 31, 1992, Luz anaperekedwa ku chipinda cha opaleshoni, kumene anaikidwa mwazi. Mkati mwa kuikidwa mwaziko, anamva antchito a m’chipatala ena akuseka. Ena ankalankhula mozaza kuti zimene zinali kuchitika zinali kuti iye akhale bwino. Anayesayesa ndi mphamvu zake zonse—koma osaphula kanthu. Pomalizira pake, Luz anali atalandira mabotolo anayi a mwazi.
Nkhani ya Luz sinali yoyamba kapena yomaliza ponena za Mboni za Yehova ndi kuikidwa mwazi ku Puerto Rico. Zisanamchitikire zimenezi, pafupifupi zilolezo za khoti 15 za kuika mwazi m’thupi motsutsana ndi chifuno cha Mboni za Yehova zachikulire zinali zitaperekedwa, ndipo zinanso zaperekedwa kuchokera pamenepo. Momvetsa chisoni, m’chochitika china chilolezo cha khoti chinatsatiridwa, ndipo wodwala wina anaikidwa mwazi mokakamiza atakomoka.
Komabe, nkhondo ya Luz sinathere m’chipinda cha opaleshoni. Mu October 1993 Commonwealth of Puerto Rico inasumiridwa mlandu. Mlanduwo unali mu Superior Court, ndipo pa April 18, 1995, mlanduwo unagamulidwa ndipo Luz anapambana. Khoti linanena kuti chilolezo cha kuika mwazi chinali “chosemphana ndi konsichushoni ndipo chinalanda mwini mlandu kuyenera kwake kwa kuchita mwaufulu chipembedzo chake, kusasokonezedwa ndi kudzisankhira zochita ndi thupi lake popanda lamulo.”
Chigamulo chimenechi chinali chapadera, popeza inali nthaŵi yoyamba kuti khoti ku Puerto Rico ligamule mokomera Mboni za Yehova pankhani ya kuikidwa mwazi. Chigamulocho chinachititsa zochitika zina zambiri. Panakhala makambitsirano ndi atolankhani a nyuzipepala yodziŵika koposa, atolankhani a wailesi, ndi a wailesi yakanema.
Usiku umenewo wailesi inaulutsa programu ya kufunsa mmodzi wa maloya a Luz. Omvetsera anapemphedwa kuimbirako foni ndi kufunsa mafunso. Madokotala ambiri ndi maloya anaimbirako foni ndi kusonyeza kukondwa kwawo pankhaniyi. Wina amene anaimbirako foni ananena kuti: “Sayansi siinathe kutsimikiza kuti kuika mwazi m’thupi kungapulumutse moyo, ndipo kulingalira motero ndi kulakwa.” Ananenanso kuti: “Posachedwapa, kuika mwazi kudzalembedwa m’mbiri monga kutayika kwina kwakukulu ndi kuphophonya kwa zamankhwala kwamakono.”
Profesa wa zamalamulo wina wolemekezeka pambuyo pake anaimbira foni ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ndipo ananena kuti anakhutira kwambiri ndi chimene anatcha “chipambano chachikulu.” Anawonjezera mwakunena kuti chigamulo cha khoti chimenecho chinachirikiza zoyenera za lamulo, osati za Mboni za Yehova zokha, koma za nzika zonse za Puerto Rico.