Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 1/15 tsamba 31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Pali Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja?
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Sangalalani ndi Moyo Wabanja
    Sangalalani ndi Moyo Wabanja
  • Banja—Nlofunika kwa Munthu Aliyense!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Muziyamikira Mwayi Wanu Wokhala M’banja la Yehova
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 1/15 tsamba 31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Aefeso 3:14, 15, (NW) amanena kuti kwa Mulungu nkumene “banja lililonse kumwamba ndi padziko lapansi limatenga dzina.” Kodi kumwamba kuli mabanja, ndipo kodi banja lililonse la anthu mwanjira ina limatenga dzina lake kuchokera kwa Yehova?

Kumwamba kulibe mabanja onga amene ali padziko lapansi, okhala ndi atate, amayi, ndi ana​—onse okhala paubale mwakuthupi. (Luka 24:39; 1 Akorinto 15:50) Yesu ananena bwino lomwe kuti angelo sakwatira, ndipo palibe chimene chimasonyeza m’njira ina iliyonse kuti amakhala ndi ana.​—Mateyu 22:30.

Komabe, Baibulo limanena mophiphiritsira za Yehova Mulungu monga mwamuna wa gulu lake lakumwamba; ngwokwatira m’lingaliro lauzimu. (Yesaya 54:5) Gulu lakumwamba limenelo limabereka ana, monga angelo. (Yobu 1:6; 2:1; 38:4-7) Motero, m’njira imeneyi, kuli banja lauzimu labwino kwambiri kumwamba.

Ndiponso, kumwamba kukupangika banja lophiphiritsira latsopano, lopangidwa ndi Yesu Kristu ndi mkwatibwi wake, mpingo wa anthu 144,000. (2 Akorinto 11:2) Ambiri a odzozedwa ameneŵa anamwalira kale, ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba. Ena akali amoyobe padziko lapansi. Onse mokondwera akuyembekezera “ukwati wa Mwanawankhosa” wakumwamba. Baibulo limagwirizanitsa ukwati umenewo ndi nthaŵi ya chisautso chachikulu chikudzacho​—kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, ndiyeno kuchotsedwapo kwa dongosolo lonse la Satana.​—Chivumbulutso 18:2-5; 19:2, 7, 11-12; Mateyu 24:21.

Ponena za mabanja apadziko lapansi, mtumwi Paulo pa Aefeso 3:15 sakutanthauza kuti banja lililonse limatenga dzina lake mwachindunji kuchokera kwa Yehova. M’malo mwake, Paulo mwachionekere anali kulingalira za mfunda umene umasunga dzina. Yoswa 7:16-19 amapereka chitsanzo. Pamenepo Yehova anali kuulula tchimo la Akani. Choyamba, liwongo linaikidwa pa fuko la Yuda. Ndiyeno m’fukomo mlandu unapezeka pabanja la Azari. Pomalizira pake, banja la Akani linavumbulidwa. Akani pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake anaonedwa, kapena kunenedwa, monga mbali ya nyumba (kapena banja) ya Zabidi, agogo ake a Akani. Ndiyeno banja limenelo la Zabidi linali mfunda umene unasunga dzina la kholo lawo Zera.

Kwa Ahebri, mizera ya mibadwo yotero inali yofunika kwambiri, yambiri ya iyo inandandalikidwa m’Baibulo. Mulungu anachirikiza kusunga kwawo maina kumeneko mwa kupanga makonzedwe akuti wina azipitiriza ndi dzina la banja kudzera mwa Kuloŵa Chokolo pamene kunali kofunika.​—Genesis 38:8, 9; Deuteronomo 25:5, 6.

Monga chitsanzo china cha mabanja aakulu otero kapena mifunda, talingalirani Yesu monga mwana wa Davide. Mosakayikira iye sanali mbadwa ya Mfumu Davide mwachindunji, anali asanabadwe kufikira zaka mazana ambiri Davide atamwalira. Komabe, chizindikiro cha Mesiya chinali chakuti iye adzakhala wa m’banja la Davide, monga mmene Ayuda onse anadziŵira. (Mateyu 22:42) Yesu anali mumzera wa Davide kudzera mwa amake ndi atate wake omsunga omwe.​—Mateyu 1:1; Luka 2:4.

Koma kodi ndi motani mmene mabanja ameneŵa amatengera maina awo kuchokera kwa Yehova? Choonadi ndicho chakuti panali nthaŵi zingapo​—monga pankhani ya Abrahamu ndi Isake​—pamene Yehova mwachindunji anatcha mutu wa banja dzina. (Genesis 17:5, 19) Zimenezo zinali zochitika zapadera. Koma kwakukulukulu, Yehova samapatsa banja lililonse dzina limene limaperekedwa kwa ana.

Komabe, Yehova ndiye amene anayambitsa banja laumunthu pamene analamula Adamu ndi Hava ‘kubalana, kuchuluka ndi kudzaza dziko lapansi.’ (Genesis 1:28) Ndipo Yehova analola Adamu ndi Hava opanda ungwirowo kukhala ndi ana, motero akumayala maziko a mabanja onse aumunthu. (Genesis 5:3) Motero kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, Mulungu angatchedwe Myambitsi wa maina a mabanja.

Anthu ambiri lerolino alibenso chifukwa chosungira dzina la banja kwa mibadwo yambiri. Komabe, m’maiko onse Akristu amayamika Yehova kaamba ka makonzedwe a banja ndipo amamlemekeza mwa kuyesetsa kupanga mabanja awo kukhala achipambano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena