Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-21 tsamba 1-6
  • Sangalalani ndi Moyo Wabanja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sangalalani ndi Moyo Wabanja
  • Sangalalani ndi Moyo Wabanja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Banja Linayambira
  • Kodi Njira Yakuchipambano Ndiiti?
  • Kupangitsa Moyo Wabanja Kukhala Wabwino
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Pali Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja?
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
Onani Zambiri
Sangalalani ndi Moyo Wabanja
T-21 tsamba 1-6

Sangalalani ndi Moyo Wabanja

Kodi mabanja angakhaledi achimwemwe?

Kodi nzotheka motani?

Kodi mumadziŵa mabanja ena aliwonse amene alidi ogwirizana ndi achimwemwe monga mmene akuwonekera patrakiti lino? Kulikonse mabanja akusweka. Chisudzulo, kusatsimikizirika kwa ntchito, mavuto akholo limodzi, kugwiritsidwa mwala—zonsezi zimathandizira vutolo. Katswiri wina wamoyo wabanja anadandaula kuti: “Kufikira tsopano, zoneneratu za kulephera kwa banja nzodziŵika kwa aliyense.”

Kodi nchifukwa ninji lerolino mabanja amakanthidwa ndi mavuto aakulu otero? Kodi tingasangalale motani ndi moyo wabanja?

Mmene Banja Linayambira

Kuti tiyankhe mafunso ameneŵa, tifunikira kudziŵa chiyambi cha ukwati ndi banja. Pakuti ngati zimenezi zinali ndi Woyambitsa—Mlengi—ziŵalo za banja ziyenera kuyang’ana kwa iye kaamba ka chitsogozo, popeza kuti iye ndithudi akadziŵa bwino koposa mmene tingasangalalire mokwanira ndi moyo wabanja.

Mokondweretsa, ambiri amakhulupirira kuti kakonzedwe kabanja kanalibe Woyambitsa. The Encyclopedia Americana imati: “Akatswiri ena ngokhoterera kukulingalira chiyambi cha ukwati ku kutsanzira chitsanzo chakakonzedwe ka kukhala ziŵiriziŵiri kwa zinyama zotsika kwa anthu.” Komabe, Yesu Kristu ananena za kulengedwa kwa mwamuna ndi mkazi. Iye anagwira mawu cholembedwa choyambirira cha Baibulo monga magwero ndipo anati: “Chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.”—Mateyu 19:4-6.

Chotero Yesu Kristu ngwolondola. Mulungu wanzeru analenga anthu oyamba nalinganiza moyo wachimwemwe wabanja. Mulungu anagwirizanitsa anthu aŵiri oyambawo pamodzi muukwati ndipo anati mwamuna ‘ayenera kudziphatika kwa mkazi wake; ndipo adzakhala thupi limodzi.’ (Genesis 2:22-24) Pamenepotu, kodi kungakhale kuli kwakuti mavuto a banja lerolino ali kaamba ka kulondola mikhalidwe imene imaipitsa miyezo yokhazikitsidwa ndi Mlengi m’Mawu ake, Baibulo?

Kodi Njira Yakuchipambano Ndiiti?

Mosakayikira monga momwe mudziŵira, dziko lamakonoli limapititsa patsogolo kudzikondweretsa ndi kudzikhutiritsa. “Dyera nlabwino,” wazachuma wina anauza kalasi lina lomaliza maphunziro pakoleji mu United States. “Mungakhale wadyera ndipo komabe nkudzilingalira kukhala wabwino.” Koma kulondola chuma chakuthupi sikumadzetsa chipambano. Kunena zowona, kukondetsa zakuthupi ndicho chimodzi cha ziwopsezo zazikulu koposa kumoyo wabanja chifukwa zimadodometsa maunansi a anthu ndi kuthera anthu nthaŵi ndi ndalama. Mosiyana, talingalirani mmene miyambi iŵiri yokha ya Baibulo imatithandizira ife kuwona chimene chiri chofunika kaamba ka chimwemwe.

“Kuli bwino kudya masamba ndi anthu amene mumakonda koposa kudya nyama yabwino kwambiri pamene pali udani.”

“Kuli bwino kudya mkate wouma ndi mtendere wamaganizo koposa kukhala ndi phwando m’nyumba yodzala mavuto.”

Miyambo 15:17; 17:1, “Today’s English Version.”

Mawu amphamvudi, kodi sichoncho? Tangoganizani mmene dzikoli likanakhalira ngati banja lirilonse linamamatira kuzofunika zoyamba zimenezi! Baibulo limaperekanso chitsogozo cha mtengo wapatali chonena za mmene ziŵalo za banja ziyenera kuchitirana. Talingalirani zitsogozo zoŵerengeka zimene limapereka.

Amuna okwatira: ‘Kondani akazi anu monga thupi lanu.’—Aefeso 5:28-30.

Zosavuta, koma zogwira ntchito kwambiri! Baibulo limalamulanso amuna okwatira ‘kuchitira ulemu akazi awo.’ (1 Petro 3:7) Amachita zimenezi mwakupereka chisamaliro chapadera kwa iye, kuphatikizapo chikondi, kumvetsetsa, ndi chitsimikiziritso. Iye amaŵerengeranso malingaliro ake ndipo amamumvetsera. (Yerekezerani ndi Genesis 21:12.) Kodi simukuvomereza kuti banja lirilonse lidzapindula ngati mwamuna achitira mkazi wake nkhaŵa, monga momwe iye akafunira kuchitiridwa?—Mateyu 7:12.

Akazi Okwatiwa: ‘Mulemekeze kwambiri mwamuna [wanu].’—Aefeso 5:33.

Mkazi wokwatiwa amachititsa chimwemwe m’banja mwa kuthandiza mwamuna wake kukwaniritsa mathayo ake olemera. Zimenezi ndizo zimene zinalinganizidwa, popeza kuti Mulungu anagaŵira mkazi kukhala “womthangatira.” (Genesis 2:18) Kodi mungayerekezere dalitso lomwe lingakhale pamoyo wabanja pamene mkazi asonyeza mwamuna wake ulemu mwa kuchirikiza zosankha zake ndi kugwirizana naye kupeza zonulirapo za banja?

Anthu a Muukwati: “Amuna okwatira ndi akazi okwatiwa ayenera kukhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake.”—Ahebri 13:4, TEV.

Pamene atero, moyo wabanja umapinduladi. Kaŵirikaŵiri chigololo chimawononga banja. (Miyambo 6:27-29, 32) Pamenepo, mwanzeru, Baibulo limafulumiza kuti: “Kondwera ndi mkazi wako ndi kupeza chisangalalo chako ndi msungwana amene unakwatira . . . Nchifukwa ninji uyenera kupatsa chikondi chako kwa mkazi wina?”—Miyambo 5:18-20, TEV.

Makolo: ‘Phunzitsani [ana anu] poyamba njira [yawo].’—Miyambo 22:6.

Pamene makolo apatula nthaŵi ndi kusamalira ana awo, ndithudi moyo wabanja umawongokera. Motero, Baibulo limafulumiza makolo kuphunzitsa ana awo makhalidwe abwino ‘pokhala m’nyumba yawo ndi poyenda pamsewu ndi pogona ndi podzuka.’ (Deuteronomo 11:19) Baibulo limanenanso kuti makolo ayenera kusonyeza kuti amakonda ana awo mwa kuwalanga.—Aefeso 6:4.

Ana: “Ananu, mverani akukubalani mwa ambuye.”—Aefeso 6:1.

Ndithudi, m’dziko lino losayeruzika, sikokhweka nthaŵi zonse kumvera makolo anu. Komabe, kodi simukuvomereza kuti kuli kwanzeru kuchita chimene Woyambitsa banja amatiuza? Iye amadziŵa chimene chiri chabwino koposa kupangitsa moyo wabanja lathu kukhala wachimwemwe kwambiri. Chotero yesetsani kumvera makolo anu. Khalani otsimikizira kupeŵa ziyeso zambiri zadziko za kuchita chimene chiri choipa.—Miyambo 1:10-19.

Pamene chiŵalo chirichonse cha banja chigwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo, moyo wabanja udzapindula. Sikokha kuti banja lidzasangalala ndi moyo wabanja wabwino kwambiri tsopano lino koma lidzakhala ndi chiyembekezo chamtsogolo mwabwino kwambiri m’dziko latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) Chotero pangani kukhala chizoloŵezi cha banja kuphunzirira Baibulo limodzi! Mamiliyoni amabanja padziko lonse lapansi apeza chitsogozo choperekedwa m’bukhu la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja kukhala cha phindu lenileni.

Kusiyapo ngati kutasonyezedwa mwanjira ina, mawu onse a Baibulo ogwidwa muno ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.

[Mawu a Chithunzi patsamba 6]

Magwero a Zithunzithunzi: Ana amikango: Mwakukoma mtima kwa Hartebeespoortdam Snake and Animal Park.

[Maadilesi a Maofesi a Nthambi patsamba 6]

Ngati mungafune kudziŵa zambiri lemberani ku Watchtower, mwakugwiritsa ntchito adiresi yoyenera pansipa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena