Banja—Nlofunika kwa Munthu Aliyense!
ANTHU amakhulupirira kuti mtundu wa anthu umachita zinthu zofanana ndi zimene mabanja ake amachita. Mbiri imasonyeza kuti pamene mabanja asokonezeka, mtundu wonse wa anthu umayamba kuchepa mphamvu. Pamene makhalidwe oipa anafalikira m’mabanja a ku Greece wakale, chitukuko chake chinasokonezeka, zimene zinapangitsa kuti agonjetsedwe mosavuta ndi Aroma. Ufumu wa Roma unakhalabe wamphamvu nthaŵi yokhayo imene mabanja anakhalabe olimba. Koma patapita zaka mazana ambiri, moyo wa banja unafooka, ndipo mphamvu ya ufumuwo inachepa. “Chisungiko ndi ulemerero wa mabanja ndiponso wa moyo wa banja ndizo zinthu zofunika kwambiri pachitukuko, ndiponso ndizo zolinga za kugwira ntchito mwakhama,” anatero Charles W. Eliot, pulezidenti wakale wa Harvard University.
Ndithudi, banja nlofunika kwa munthu aliyense. Limathandiza kwambiri kuti mtundu ukhale wolimba ndiponso limathandiza pa ubwino wa ana ndi mibadwo yamtsogolo. Mosakayika konse, pali amayi ambirimbiri opanda amuna amene amayesetsa kulera ana a khalidwe labwino, ndipo amayi otere ayenera kuthokozedwa chifukwa cha khama lawo limeneli. Komabe, zimene ofufuza apeza zimasonyeza kuti nthaŵi zambiri ana amakhala ndi makhalidwe abwino ngati akulira m’mabanja a makolo onse aŵiri.
Pa kufufuza kwina kumene kunachitika ku Australia, anapeza kuti mwa achinyamata oposa 2,100 “achinyamata ochokera m’mabanja osweka anali ndi mavuto ochuluka aumoyo, ambiri anali kusonyeza zizindikiro za kusokonezeka maganizo, ndipo ambiri anali omwerekera pankhani ya kugonana kusiyana ndi ana ochokera m’mabanja a makolo onse aŵiri.” Pa kufufuza kumene kunachitidwa ndi National Institutes of Health Statistics ya United States anapeza kuti mwa ana ochokera m’mabanja osweka panali “20-30 peresenti oti angachite ngozi nthaŵi iliyonse, 40-75 peresenti oti angabwereze m’kalasi kusukulu, ndipo 70 peresenti oti angachotsedwe pasukulu nthaŵi iliyonse.” Ndipo woyang’anira wina wa kayendetsedwe ka zinthu anati “ana ochokera m’mabanja a kholo limodzi angachite zaupandu nthaŵi iliyonse kusiyana ndi ana okulira m’mabanja a makolo onse aŵiri.”
Banja Ndilo Pothaŵira
Makonzedwe a banja amapangitsa kuti panyumba pakhale popatsa chimwemwe, polimbikitsa, ndiponso posangalatsa kwa onse. “Chinthu chofunika kwambiri chodzetsa chimwemwe ndi ubwino wa munthu si ntchito, katundu, zosangulutsa kapena mabwenzi ayi koma banja,” anatero katswiri wina wa ku Sweden.
Baibulo limafotokoza kuti banja lililonse padziko lapansi linatchedwa dzina ndi Mlengi Wamkulu wa mabanja, Yehova Mulungu, popeza kuti ndiye amene anayambitsa makonzedwe a banja. (Genesis 1:27, 28; 2:23, 24; Aefeso 3:14, 15) Komabe, m’Malemba ouziridwa, mtumwi Paulo ananeneratu za kusweka koopsa kwa mabanja, kumene kunali kudzaipitsa makhalidwe a anthu onse okhala kunja kwa mpingo wachikristu. Iye anati “masiku otsiriza” adzadzaza ndi kusakhulupirika, kupanda “chikondi chachibadwidwe,” ndiponso kusamvera makolo, ngakhale pakati pa anthu “akukhala nawo maonekedwe achipembedzo.” Iye anapempha Akristu kuti adzipatule kwa anthu otero. Yesu ananeneratu kuti kutsutsidwa kwa choonadi cha Mulungu kudzagaŵanitsa mabanja.—2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 10:32-37.
Komabe, Mulungu watipatsa chithandizo. M’Mawu ake muli nkhani zambiri zonena za malangizo okhudza moyo wa banja. Amatiuza mmene tingapangire banja kukhala lachipambano ndi mmene panyumba pangakhalire malo osangalatsa kumene aliyense wapabanjapo ali ndi ntchito yochita kaamba ka ubwino wa ena.a—Aefeso 5:33; 6:1-4.
Kodi nkotheka kukhala ndi moyo wa banja wachimwemwe chotero masiku ano pamene banja lili pangozi yaikulu? Inde, nkothekadi! Mungathe kupangitsa moyo wa banja lanu kukhala ngati chitsime chosangalatsa ndiponso chotsitsimula cha m’chipululu, m’dziko lovuta kwambiri longa chipulululi. Koma zimenezi zimafuna kuti aliyense wa m’banjamo achitepo kanthu. Nawa malingaliro ena.
Kuthandiza Banja Lanu Kuti Lipulumuke
Kukhalira pamodzi ndiyo imodzi mwa njira zabwino kwambiri zopangitsa kuti banja likhalebe logwirizana. Onse a m’banjamo ayenera kuyesetsa kumachezera pamodzi panthaŵi yawo yopuma. Pangafunikire kudzimana kuti zimenezo zitheke. Mwachitsanzo, inu achinyamata mungafunikire kuti nthaŵi zina musakaonerere programu ina yapamtima ya pa TV, maseŵero ena, kapena kulephera kukayenda ndi mabwenzi anu. Inu atate, amene nthaŵi zambiri muli ochirikiza aakulu a banja, nthaŵi yopuma musaitenge ngati nthaŵi yochita zosangulutsa zanu zokha kapena zinthu zina. Linganizani zochita zinthu zina ndi banjalo, mwinamwake mmene mungakhalire pamodzi pamapeto a mlungu kapena patchuti. Inde, muyenera kulinganiza zinthu zimene aliyense adzasangalala nazo ndipo sadzaziiŵala.
Sikuti ana amangofunikira nthaŵi yolinganizidwa yocheza nawo ndi kuwaphunzitsa basi, imene ingakhale theka la ola kapena kuposapo, nthaŵi ndi nthaŵi. Iwo amafunikira kukhala nawo nthaŵi zambiri. Wolemba m’nyuzipepala yatsiku ndi tsiku wina wa ku Sweden analemba kuti: “Zaka zonse 15 zimene ndakhala mtolankhani, ndaona achinyamata ambiri oswa malamulo . . . Onse amasonyeza kuti sanali kukhala kwambiri ndi makolo awo: ‘Makolo anga analibe nthaŵi yokhala nane.’ ‘Sankamvetsera mpang’ono pomwe.’ ‘Ankakonda kuyendayenda.’ . . . Monga kholo, muli ndi ufulu wosankha utali wa nthaŵi imene mungakhale ndi ana anu. Chosankha chanu chidzadziŵika kuti nchoipa zaka 15 pambuyo pake pamene mwana wanu wazaka 15 adzasonyeza makhalidwe oipa.”
Kaonedwe Koyenera ka Ndalama
Onse a m’banjamo ayeneranso kukulitsa kaonedwe koyenera ka ndalama. Iwo ayenera kukhala ofunitsitsa kuthandiza mulimonse mmene angathere pazosoŵa za banja. Akazi ambiri amaloŵa ntchito kuti azipeza ndalama zothandizira banjalo, koma akazi okwatiwanu muyenera kukhala tcheru ndi zoopsa ndiponso ziyeso zimene mungakumane nazo. Dziko lino limakulimbikitsani kuti “muzidzikhutiritsa” ndi “kuchita zilizonse zimene mungafune.” Lingakupangitseni kukhala anthu odzidalira kopambanitsa ndiponso osakhutira ndi udindo wanu wopatsidwa ndi Mulungu monga mayi ndi osamala panyumba.—Tito 2:4, 5.
Ngati amayinu mukhala panyumba ndi kukhala monga wotsogolera ndi bwenzi la ana anu, zimenezo zidzapangitsa kuti mukhale ndi zomangira zolimba zimene zidzathandizira kuyanjanitsa banja lanu kaya pamavuto kapena pamtendere. Mkazi angathandizire kwambiri kupangitsa banja kukhala lachimwemwe, lachisungiko, ndiponso lothandiza. “Pamafunikira amuna zana limodzi kuti amange msasa, koma mkazi mmodzi angamange banja,” anatero wandale wina wa m’zaka za zana la 19.
Ngati onse m’banjamo agwirizana kuti azigula zinthu mogwirizana ndi ndalama zimene ali nazo, zingathandizire kupeŵa mavuto ambiri m’banjamo. Okwatirana angagwirizane kuti akhale ndi njira ya moyo yopepuka ndi kuika zinthu zaufumu pamalo oyamba. Ana ayenera kuphunzira kukhala okhutira ndi zimene ali nazo, osafuna zinthu zimene banjalo silingathe kugula. Chenjerani ndi chilakolako cha maso! Chilakolako chogula zinthu zimene sangathe ndiponso kutenga ngongole, zadzetsa mavuto aakulu m’mabanja ambiri. Mgwirizano wa banja ungapitirize ngati onse m’banjamo atamaperekako ndalama zochitira chinthu chinachake—kupita kutchuti, kugulira chinthu china chothandiza ndi kusangalatsa banjalo, kapena kupanga chopereka chothandizira mpingo wachikristu.
Aliyense wa m’banjamo “angachitepo” kanthu kuti athandizire kudzetsa moyo wa banja wachimwemwe mwa kuchita nawo ntchito yoyeretsa ndi kukonza—kusamala m’nyumba, kulima dimba, kusamala galimoto, ndi zina zotero. Aliyense wa m’banjamo, ngakhale ana, angapatsidwe ntchito zina. Ananu, yesetsani kusathera nthaŵi yanu pazinthu zachabe. M’malo mwake, kulitsani moyo wothandiza ndi kugwirizana ndi banja lanu; zimenezi zidzapangitsa ubwenzi ndiponso mayanjano enieni, zimene zimalimbikitsa umodzi wa banja.
Kufunika kwa Maphunziro a Baibulo
M’banja lachikristu logwirizana, amagogomezera za kufunika kwa phunziro lokhazikika la Baibulo. Makambitsirano a tsiku ndi tsiku a malemba a m’Baibulo ndi phunziro la mlungu ndi mlungu la Malemba Opatulika zili maziko a banja logwirizana. Ndi bwino kukambitsirana ziphunzitso ndi mapulinsipulo oyambirira a Baibulo mwa njira yosonkhezera mitima ya onse m’banjamo.
Maphunziro amenewo a banja ayenera kukhala ophunzitsa koma panthaŵi imodzimodziyo ayenera kukhala osangalatsa ndi olimbikitsa. Banja lina kumpoto kwa Sweden linali kupempha ana awo kuti azilemba mafunso amene anali nawo mlungu uliwonse. Mafunso ameneŵa anali kuyankhidwa paphunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu. Nthaŵi zambiri mafunsowo anali ozama ndiponso ochititsa chidwi ndipo anasonyeza kuti anawo anali kulingalira mozama ndi kumvetsetsa ziphunzitso za Baibulo. Ena mwa mafunsowo anali akuti: “Kodi Yehova amakulitsa zinthu nthaŵi zonse, kapena anangozikulitsa pachiyambi pokha?” “Kodi nchifukwa ninji Baibulo limanena kuti Mulungu analenga munthu ‘m’chifanizo chake’ pamene Mulunguyo si munthu?” “Popeza kuti Adamu ndi Hava sanavale nsapato ndipo analibe zovala, kodi iwo sanaume ndi chisanu cha m’Paradaiso?” “Popeza kuti usiku kumayenera kukhala mdima, kodi nchifukwa ninji timafunikira mwezi?” Ana ameneŵa tsopano anakula ndipo akutumikira Mulungu monga atumiki a nthaŵi zonse.
Posamalira mavuto a banja, makolonu mungachite bwino kuyesetsa kukhala othandiza ndiponso achimwemwe. Khalani olingalira ena ndiponso ololera, komatu osasinthasintha ponena za kutsatira mapulinsipulo ofunika. Ana anu ayenera kuona kuti malingaliro anu nthaŵi zonse amatsogozedwa ndi chikondi chanu cha pa Mulungu ndi mapulinsipulo ake olongosoka. Kusukulu ndi malo amene nthaŵi zambiri amakhala osokoneza maganizo ndiponso ochititsa tondovi, ndipo banja liyenera kulimbikitsa ana nthaŵi ndi nthaŵi kuti apirire pazisonkhezero zotero.
Makolonu, simuyenera kudzionetsa monga ngati ndinu angwiro. Vomerezani kulakwa ndipo pepesani ana anu ngati kuli koyenera kutero. Ananu, ngati Amayi ndi Atate anu avomereza kulakwa kwawo, pitirizani kuwakonda.—Mlaliki 7:16.
Ndithudi, banja logwirizana limathandizira kuti panyumba pakhale mtendere, chisungiko, ndiponso chimwemwe. Mjeremani wandakatulo wotchedwa Goethe nthaŵi ina anati: “Wachimwemwe kwambiri ndi munthu amene amapeza chimwemwe panyumba pake, kaya akhale mfumu kapena munthu wamba.” Makolo ndi ana oyamika amaona kuti banja ndilo malo okha ofunika kwambiri.
Zoonadi, banja lili pangozi yaikulu lerolino chifukwa cha zitsenderezo za dziko limene tikukhalamo. Koma popeza kuti banja linachokera kwa Mulungu, ilo lidzapulumuka. Banja lanu lidzapulumuka, ndipo inunso mudzapulumuka ngati mutsatira zitsogozo zolungama za Mulungu zodzetsa moyo wa banja wachimwemwe.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna kudziŵa zambiri pankhani imeneyi, onani buku lamasamba 192 lotchedwa Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.