Lambirani Yehova ndi Manja Oyera
MOUZIRIDWA, wamasalmo Davide anaimba kuti: “Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova.”—Salmo 26:6.
Polemba mawuŵa, Davide angakhale anali kunena za mwambo wa ansembe achilevi a mu Israyeli wa kukwera makwerero a guwa la nsembe ndi kuika nsembe zawo pamoto. Koma asanachite ntchito ya kulambira imeneyi, ansembe anafunikira kusamba m’manja ndi mapazi. Imeneyi sinali nkhani yaing’ono. Wansembe anayenera kufa akalephera kuchita chinthu choyambirira chimenechi!—Eksodo 30:18-21.
Kusamba mophiphiritsira kumachititsa kuyera kwauzimu ndi kwamakhalidwe. (Yesaya 1:16; Aefeso 5:26) Yehova amafuna kuti ‘tizungulire guwa lake la nsembe’ lerolino mwa kumtumikira. Koma amafuna kuti tichite zimenezo ndi manja oyera—monga mmene Davide ananenera, manja amene amasambitsidwa “mosalakwa.” Chimenechi si chofunika wamba, pakuti awo amene amachita chidetso sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. (Agalatiya 5:19-21) Umoyo wa ntchito zaumulungu sumapatsa munthu ufulu wa kuloŵa m’makhalidwe oipa. Nchifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.”—1 Akorinto 9:27.
Awo amene akufuna chiyanjo chaumulungu ndi chimwemwe chenicheni ayenera kutumikira Yehova ndi manja oyera. Monga Davide, iwo amayenda “ndi mtima woona ndi wolungama.”—1 Mafumu 9:4.