Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 2/15 tsamba 32
  • Choonadi Chonse cha Uthenga Wabwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Choonadi Chonse cha Uthenga Wabwino
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 2/15 tsamba 32

Choonadi Chonse cha Uthenga Wabwino

ZIDUTSWA zitatu zazing’ono kwambiri za malembo a pamanja a Uthenga Wabwino wa Mateyu, zodziŵidwa monga P64, zakhala m’manja mwa Magdalen College ku Oxford, England, kuyambira mu 1901. Kwa nthaŵi yakutiyakuti, akatswiri anakhulupirira kuti zinali za kumapeto kwa zaka za zana lachiŵiri C.E.

Posachedwapa, Carsten P. Thiede, katswiri wa malembo a pamanja a gumbwa wa ku Paderborn, Germany, anafufuza mwakuya P64, imene ili ndi mbali za mavesi 10 a m’Mateyu chaputala 26. Kodi zotulukapo zake zinali zotani? Polemba mu Zeitschrift für Papyrologie und Epigraphik (Magazini a Zamalembo Apamanja a Gumbwa ndi Amiyala), Thiede akufotokoza zidutswa za ku Oxford kukhala “chidutswa cha mpukutu wachikristu wa m’zaka za zana loyamba, mwinamwake (koma osati kwenikweni) zokhalako AD 70 isanakwane.”

Mawu a Thiede anachititsa zolankhulalankhula pakati pa aulutsi ndi pakati pa akatswiri openda malembowo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti limene limadziŵika monga gawo lakale koposa limene lilipo la malembo a m’Mauthenga Abwino ndilo P52, chidutswa cha Uthenga Wabwino wa Yohane wokhalako pafupifupi kuyambira mu 125 C.E., kapena m’zaka za zana lachiŵiri.

Sizikudziŵika kaya ngati deti latsopano lopatsidwa zidutswa za gumbwa P64 lidzavomerezedwa ndi anthu onse. Ngakhale zili tero, deti loyamba silimangopangitsa P64 kukhala zidutswa zakale kwambiri zimene zilipo; limaperekanso umboni wowonjezereka wakuti Uthenga Wabwino wa Mateyu unalembedwadi m’zaka za zana loyamba, mwinamwake ngakhale 70 C.E. isakwane, pamene mboni zambiri zoona ndi maso za zochitika m’moyo wa Yesu zinali zidakali ndi moyo ndi kuchitira umboni choonadi chonse cha Uthenga Wabwino.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Ndi chilolezo cha President and Fellows of Magdalen College, Oxford.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena