Uphungu Wanzeru pa Nthenda
HIPPOCRATES wafika podziŵika monga “woyambitsa zamankhwala zamakono.” Zambiri zimene Baibulo limanena pa nthenda zinalembedwa ndi Mose pafupifupi zaka chikwi iye asanakhaleko. Komabe, kwanenedwa motsimikiza kuti: “Ofufuza zamankhwala achidziŵitso kwambiri amene akuchita ntchito yabwino koposa tsopano akunena kuti Baibulo lili buku lasayansi lolondola kwambiri. . . . Nkhani zokhudza kugonana, kupenda nthenda, kuchiritsa, ndi mankhwala oletsa nthenda zotchulidwa m’Baibulo zili zopita patsogolo kwambiri ndi zodalirika kuposa ziphunzitso za Hippocrates, zimene zambiri zikali zosatsimikizirika, ndipo zina zili zosalondola konse.”—Dr. H. O. Philips, m’kalata yake kwa The AMA [American Medical Association] News, imene inafalitsidwa m’kope lake la July 10, 1967.
Ponena za sing’anga wachikristu Luka, amene analemba Uthenga Wabwino ndi buku la Machitidwe, Dr. C. Truman Davis anati: “Pamene akufotokoza za mankhwala, zimakhala zolondola kwenikweni. Luka akugwiritsira ntchito maina achigiriki okwanira makumi aŵiri ndi atatu opezeka m’mabuku a zamankhwala a Hippocrates, Galen ndi ena apanthaŵiyo.”
Thanzi ndi Chilamulo cha Mose
Kusunga Chilamulo kunadzetsa thanzi labwino nthaŵi zambiri. Mwachitsanzo, ilo linafuna kuti pamsasa wa asilikali iwo azifotsera tudzi, motero akumapereka chitetezo chabwino pa nthenda zoyambukira zonyamulidwa ndi ntchentche monga kamwazi ndi typhoid fever. (Deuteronomo 23:9-14) Chakudya ndi madzi zinatetezeredwa kuti zisaipitsidwe, Chilamulo chikumafotokoza bwino kuti chinthu chilichonse chimene panagwera cholengedwa ‘chodetsa’ chakufa chinakhala chodetsedwa ndipo panafunikira kuchitapo kanthu kena, kuphatikizapo kuswa chotengera chadothi chodetsedwacho.—Levitiko 11:32-38.
The Interpreter’s Dictionary of the Bible inanenetsa kuti: “Njira zoletsa nthenda zinali zofunika kwambiri pa chilamulochi, zimene potsatiridwa zinathandiza kwambiri kuletsa kubuka kwa nthenda za m’chakudya za polioencephalitis, m’mimba, kudwala ndi chakudya choipa, ndi njoka za m’mimba. Kugogomezera kwake kusunga bwino madzi kunali njira yabwino koposa yoletsera kubuka ndi kufalikira kwa nthenda zonga za amoebiasis, nthenda za m’mimba, chizuula, likodzo, ndi spirochetal jaundice. Njira zoletsa nthenda zimenezi, zimene zili mbali yofunika kwambiri pa zathanzi la anthu kulikonse, zinali zofunika koposa pa ubwino wa mtundu umene unali kukhala m’mikhalidwe yoipa m’chigawo chotentha cha dziko lapansi.”
M’buku lake lakuti The Bible and Modern Medicine, A. Rendle Short, M.D., ananena kuti pakati pa mitundu yozinga Israyeli wakale panali malamulo wamba, ngati analipo nkomwe, a zaukhondo wa anthu, ndipo anati: “Chotero nzodabwitsa kwambiri kuti m’buku longa Baibulo, limene amati silili lasayansi, mungakhale lamulo la zaukhondo, ndipo zodabwitsanso nzakuti mtundu umene unangotuluka mu ukapolo, umene adani anali kuugonjetsa kaŵirikaŵiri ndi kuutenga ukapolo nthaŵi ndi nthaŵi, ungakhale ndi mpambo wa malamulo anzeru ndi oyenera a thanzi m’mabuku ake a malamulo. Akatswiri otchuka azindikira zimenezi, ngakhale aja amene sachita chidwi ndi mbali ya Baibulo yokhudza chipembedzo.”
Malinga ndi Chilamulo, kalulu ndi nkhumba zinali nyama zina zimene Aisrayeli sanaloledwe kudya. (Levitiko 11:4-8) Ponena za zimenezi, Dr. Short akuti: “Zoona, timadya nkhumba, kalulu ndi kafumbwe, koma nyama zimenezi zimatha kukhala ndi nthenda za tizilombo ndipo zimakhala zabwino kokha ngati zaphikidwa bwinobwino. Nkhumba imadya zonyansa, ndipo imanyamula njoka mitundu iŵiri, trichina ndi njoka za m’mimba, zimene anthu angatenge. M’mikhalidwe yamakono ngozi yake njaing’ono m’dziko lino, koma ikanakhala yaikulu kwambiri m’Palestina wakale, ndipo kunali bwino kupeŵa chakudya chotero.”
Mapindu Ena a Thanzi
Kutsatira zofunika za Yehova zolungama pa khalidwe la kugonana kunalinso ndi zotulukapo zabwino kwa Aisrayeli mwauzimu, m’maganizo, ndi kuthupi. (Eksodo 20:14; Levitiko, chaputala 18) Akristu amene amasunga chiyero cha makhalidwe amapezanso mapindu a thanzi. (Mateyu 5:27, 28; 1 Akorinto 6:9-11) Kusunga miyezo yapamwamba ya makhalidwe ya m’Baibulo kumatetezera munthu pa nthenda zopatsana mwa kugonana.
Paulo analangiza Timoteo kumwa vinyo pang’ono chifukwa cha m’mimba mwake ndi kudwaladwala kwake. (1 Timoteo 5:23) Kufufuza kwamakono kumatsimikizira kuti vinyo ali ndi mphamvu yochiritsa. Dr. Salvatore P. Lucia, Profesa wa Zamankhwala, pa University of California School of Medicine, wanena kuti: “Ambiri amagwiritsira ntchito vinyo kuchiritsira nthenda za m’mimba. . . . Tannin yake ndi mphamvu yaing’ono ya vinyo yopha tizilombo zimauchititsa kukhala wothandiza kwambiri pochiritsa nchofu ya m’matumbo, mucous colitis, kubindikira kopota m’mimba, kutseguka m’mimba ndi nthenda zambiri za m’mimba zoyambukira.” Ndithudi, Paulo anauza Timoteo ‘kuchita naye vinyo pang’ono,’ osati kwambiri, ndipo Baibulo limaletsa kuledzera.—Miyambo 23:20.
Malemba amavomereza choonadi chakuti maganizo angayambitse nthenda m’thupi, ngakhale kuti ndi posachedwapa pamene ofufuza zamankhwala ambiri adziŵa kuti pali kugwirizana pakati pa mkhalidwe wa nthenda m’thupi ndi mkhalidwe wa mtima wa munthu. Miyambo 17:22 imati: “Mtima wosekerera uchiritsa bwino; koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa.” Mikhalidwe ya mtima yonga njiru, mantha, umbombo, udani, ndi zolinga zadyera zimavulaza, pamene kuli kwakuti pamakhala zotulukapo zabwino ndipo nthaŵi zina kuchira chifukwa chokulitsa ndi kusonyeza chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso, zipatso za mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22, 23) Komabe, Malemba samati matenda onse m’thupi amayamba ndi maganizo, ndipo samati kupima ndi kuchiritsa konse kwa asing’anga nkoipa ayi. Paulo anatcha Mkristu wokhulupirika Luka “sing’anga wokondedwa.”—Akolose 4:14.