‘Kodi Ndili Wofunika Pamaso pa Mulungu?’
“KODI Ndili Wofunika? Kodi Mulungu Amasamala?” Nkhani ya mu Christianity Today inali ndi mutu umenewo. “Ntchito yanga yambiri monga wolemba nkhani yasumikidwa pankhani ya kuvutika,” akutero Philip Yancey, mlembi wa nkhaniyo. “Ndimadzifunsa mafunso amodzimodzi mobwerezabwereza, monga ngati kuti ndikukhudza chironda chakale chimene sichikuchira kwenikweni. Ndimamva kwa omwe amaŵerenga mabuku anga, ndipo nkhani zawo zomvetsa chisoni zimapereka umboni wa zikayiko zanga.”
Mwinamwake inunso munadzifunsapo za chikondwerero cha Mulungu pa moyo wanu. Eya, mwina mumadziŵa Yohane 3:16, amene amanena kuti “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha.” Kapena munaŵerengapo Mateyu 20:28, amene amanena kuti Yesu anadza “kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” Ngakhale zili motero mungafunse kuti, ‘Kodi Mulungu amandiona? Kodi amasamala za ine monga munthu pandekha?’ Pali chifukwa chabwino chokhulupirira kuti amatero, monga mmene tidzaonera.