Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 4/15 tsamba 8-10
  • Mkupiti wa Umboni Wachipambano ku Greece

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mkupiti wa Umboni Wachipambano ku Greece
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Akuluakulu a Boma Alabadira
  • Maloya a Boma Alabadira
  • Osamalira Mabuku m’Malaibulale Alabadira
Nsanja ya Olonda—1996
w96 4/15 tsamba 8-10

Mkupiti wa Umboni Wachipambano ku Greece

MBONI ZA YEHOVA zatsutsidwa kwa nthaŵi yaitali ku Greece. Akuluakulu ena a polisi, a khoti, ndi a boma azunza Mboni, kaŵirikaŵiri chifukwa cha kuumirizidwa ndi atsogoleri achipembedzo cha Greek Orthodox. Nthaŵi zina apereka chifukwa cha lamulo la kuletsa kutembenuza ena la Greece, nthaŵi zina chifukwa chakuti Mboni zimakana kupita ku nkhondo kapena kulandira mwazi chifukwa cha zimene Baibulo limanena.​—Yesaya 2:2-5; Machitidwe 15:28, 29.

Pofuna kuthandiza akuluakulu a boma oona mtima ku Greece kuti azizindikire, Mboni pafupifupi 200 zimene boma la Greece linazindikira kukhala atumiki achipembedzo, ndiponso zina zimene zili mamembala m’zamalamulo, posachedwapa zinachita mkupiti wa m’dziko lonselo. Anagaŵira brosha lachifuno chapadera la mutu wakuti Jehovah’s Witnesses in Greece, ndiponso buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom. Anagaŵiranso mtolo wa zikalata zimene zimasonyeza kuti palibe maziko ovomerezeka mwalamulo a kuzunzira Mboni za Yehova. Mbonizo zinafikira akuluakulu a polisi, mameya, maloya a boma, ndi akuluakulu ena a boma.

Kodi nchiyani chinachitika? Zokumana nazo zabwino mazana ambiri. Lingalirani zitsanzo zina.

Mkulu wa siteshoni ina ya apolisi ku West Macedonia analandira abale nati: “Anthunu ndakudziŵani kwa nthaŵi yaitali, . . . ndipo ndimasirira dongosolo lanu. . . . Sindigwirizana ndi lamulo la kutembenuza anthu, ndipo ndikanakhala ndi mphamvu, ndikanalithetsa.”

Akuluakulu a m’masiteshoni apolisi osiyanasiyana m’mizinda yambiri ananena motere: “Ndimakuyamikirani chifukwa cha kutumikira anthu kumene mumachita.” “Gulu lanu silimapatsa ntchito apolisi; mumachita ntchito yothandiza anthu.” “Sitivutika nanu nkomwe. Timakulemekezani ndi kukuyamikirani.”

Ku Piraeus mkulu wina wa boma m’gulu la apolisi achitetezero anauza abale, akutuluka misozi m’maso mwake, kuti iyeyo amadziŵa kupemphera mogwiritsira ntchito dzina la Yehova Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu. Anadabwitsa kwambiri Mbonizo pamene anaziuza kuti anadziŵa kuti izo zidzazunzidwa Armagedo isanadze, ndipo angakonde kuti Mulungu adzamgwiritsire ntchito kuzithandiza panthaŵiyo! Anavomera pempho la abale la kudzakambitsirana naye zambiri.

Akuluakulu a Boma Alabadira

Meya wina ku Thessaly ponena buku la Proclaimers anati: “Liyenera kukhala ndi malo akeake m’laibulale ya konsolo​—malo oyamba!” Chotero iye anachotsa mabuku ena pashelefu ndi kuikapo buku la Proclaimers mosonyeza chikuto chake.

Kumpoto kwa Greece, meya wina analandira abale mwachikondi nati: “Inu ndinu anthu abwino kwambiri amene ndingakonde kukhala nawo m’konsolo yanga.” Meya wina wokoma mtima ku Euboe kumpoto anauza abale kuti: “Ine kale ndinali ofesala wa gulu la nkhondo. Koma anthunu​—ndimakuyamikirani kwambiri.” Anavomereza mokondwa mfundo zimene Mbonizo zinanena. Pamene zinamsonyeza mabuku ofalitsidwa ndi Watch Tower Society, iye anati: “Ngati ndikulonjezani kuŵerenga onse amene, kodi mungandipatse?” Iwo anayankha kuti: “Komatu​—ndi anu kumene!” Anakondwera ndipo sanafune kuti abalewo achoke.

Mumlaga wina wa ku Attica, meya analandira mwachimwemwe mabuku amene abale anagaŵira ndi kuwapempha kupitiriza kumbweretsera zofalitsa za Sosaite. Pamene anali kuchoka, anawauza kuti: “Anthu ali ogwiritsidwa mwala kwambiri ndi andale ndipo akufunafuna choonadi chenicheni kwina. Ndikukhulupirira kuti kuyambira tsopano mudzakhala otanganitsidwa kwambiri chifukwa chakuti muli ndi choonadi.”

Maloya a Boma Alabadira

Abale amene anafikira wachiŵiri kwa loya wa boma kumpoto kwa Greece akukumbukira kuti: “Anachita chidwi ndi zofalitsa zathu ndi nkhani zake, ndiponso zoyesayesa zimene timapanga kutsimikizira kuti anthu athu asasoŵe chochita pamene ayang’anizana ndi nkhani ya kuika mwazi. Potsirizira pake anatithokoza ndi kutiyamikira kwambiri chifukwa cha kuchitapo kanthu mwa kumfikira ndi kumdziŵitsa. Pambuyo pake, tinapeza kuti zaka zinayi kumbuyoko anaitana apolisi ndi kuwalamulira kugwira abale aŵiri amene anali mu utumiki wakumunda.”

Mboni ziŵiri zimene zili maloya zimene zinapita ku maofesi a maloya a boma ku Athens zinadabwa kuona loya wa boma wachikulire wotchuka ndi wolemekezedwa kwambiri akumafika kwa iwo. Anawatengera pambali ndi kuwauza kuti lamulo lotsutsa kutembenuza anthu lilibe maziko ndipo limadzetsa msokonezo m’makhoti a Greece. Iyeyo anawathokoza mwakugwirana nawo chanza mwamphamvu.

Kumpoto kwa Greece, loya wa boma wina anali waubwenzi kwambiri ndipo analandira mabuku. Pamene anali kutsegula masamba a buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza, anadabwa poona mitu yosiyanasiyana pampambo wake wa zamkati. Iyeyo anati: “Zimene bukuli likufotokoza, sindinazionepo mu Orthodox monse.”

Loya wina wa boma ku Boeotia anavomera kuti iye, kale, analamula kuika mwazi Mboni motsutsana ndi chifuniro chawo. Koma abalewo atakambitsirana naye za nkhaniyo, ananena kuti: “Sindidzalamulanso zotero mtsogolo!” Ananena kuti Hospital Liaison Committee yakumaloko iyenera kudziŵitsidwa kotero kuti njira zina zonse m’malo mwa mwazi zigwiritsiridwe ntchito. Analandira mokondwa buku la Achichepere Akufunsa.

Osamalira Mabuku m’Malaibulale Alabadira

Mabukuwo anaperekedwanso kwa osamalira mabuku m’malaibulale. Mu laibulale ina ku Athens, wosamalira mabuku mu laibulale wina waulemu analandira mabuku ndi kunena kuti: “Ndi bwino kuti mwatibweretsera mabuku anu chifukwa chakuti mabuku ochuluka omwe tili nawo mu laibulale yathu ngokutsutsani. . . . Wansembe wina anakwiya kwambiri poona mabuku anu mu laibulale. . . . Zilibe ntchito. Maganizo onse ayenera kumvedwa.”

Mkulu wina wa boma mu laibulale ya konsolo ku Crete, amene anadziŵa Mboni za Yehova m’malo ena a gulu la nkhondo, anauza abale kuti anachita chidwi ndi kukana kwa Mboni kukhala ndi phande mu nkhondo. Ankadzifunsa kuti, ‘Kodi anthuwa amawavutitsiranji?’ Analandira mabuku kwa abale nanena za mkupiti wawowo kuti: “Mwachita ntchito yabwino kwambiri ndipo mukanafunikira kuchita zimenezi zaka zapitazo. . . . Mu Greece muno muli tsankhu kwambiri.” Anapempha abalewo kudzamfikiranso msanga.

Pamkupiti umenewu wapadera, abale anagaŵira mabuku a Proclaimers oposa 1,000, mabrosha a Jehovah’s Witnesses in Greece 1,600, ndiponso mazana ambiri a mabuku ena ndi magazini. Chinthu chabwino kwambiri nchakuti iwowo anakambitsirana mwachindunji ndi akuluakulu a boma la Greece. Tsopano atumiki okhulupirika a Yehova ku Greece ndi padziko lonse akuyembekezera kuti akuluakulu a boma oona mtima ku Greece adzaona Mboni za Yehova mopanda tsankhu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena