Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 4/15 tsamba 31
  • Chifukwa Chake Iye Anagwiritsira Ntchito Dzina Lalikulukululo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chake Iye Anagwiritsira Ntchito Dzina Lalikulukululo
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 4/15 tsamba 31

Chifukwa Chake Iye Anagwiritsira Ntchito Dzina Lalikulukululo

“Ndachimwa, malinga ndi kunena kwa mmodzi wa otsutsana nane, poika liwulo ‘Yehova’ m’malo mwa ‘Ambuyeyo,’ limene laikidwa m’malo mwake kwa zaka mazana ambiri.”

Imeneyi inali ndemanga ya J. J. Stewart Perowne m’mawu oyamba a kope lachiŵiri la kutembenuza kwake buku la Masalmo, limene linafalitsidwa koyamba mu 1864. Womtsutsayo, polemba mu Saturday Review ya July 2, 1864, anakana kugwiritsiridwa ntchito kwa dzina la Mulungu m’matembenuzidwewo, popeza kuti silinali kugwiritsiridwanso ntchito m’matchalitchi achiyuda kapena achikristu. Iye ananena kuti dzinalo Yehova nlogwirizanitsidwa kwambiri ndi Ayuda ndi kuti ayenera kugwiritsira ntchito dzina lina, monga lakuti “Ambuye” kapena “Mulungu,” “limene silili lakumalo akutiakuti kapena logwirizanitsidwa ndi mtundu wina.”

Perowne sanagwirizane ndi mfundo zimenezi, popeza kuti iye ‘sanafune kuchotsa lembo ngakhale limodzi lililonse’ la vumbulutso la Mulungu kwa munthu. Iye moyenera anaumirira kuti otembenuza amene amatembenuza dzina la Mulungu lachihebrilo kuti “Ambuye” amalephera kusiyanitsa pa mawu aŵiri achihebri.

Ndiponso, Perowne ananenetsa kuti panali anthu olemba mabuku odziŵa bwino kwambiri amene anayanja kubwezeretsa dzina la Mulungu pamalo pake. Iye anagwira mawu wolemba ndakatulo wachingelezi wotchuka Samuel Taylor Coleridge kuti:

“Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupitiriza kutembenuzira Chihebri m’Chingelezi mogwiritsira ntchito mkhalapakati, kupyolera mu Septuagint? Kodi sitinatengere liwu lachihebri lakuti Yehova? Kodi Κύριος, kapena kuti Ambuye, wa Septuagint, sali liwu lobwerekera lachigiriki m’malo ambirimbiri a Yehova wachihebri? Nangano, bwanji osabwezera liwu lake loyambirira; ndipo m’Chipangano Chakale kutembenuza mokhulupirika Yehova, pamalo pake pa Yehova; ndipo vesi lililonse m’Chipangano Chatsopano, lotchula za Chakale, mwa dzina limenelo lachihebri pa lemba losonyezedwalo?”

Perowne anavomereza kuti matchulidwe enieni a Tetragrammaton yachihebri azimiririka, komano anati: “Koma ngati chili chifukwa chakuti dzinalo linalekedwa kugwiritsiridwa ntchito m’Tchalitchi cha Ayuda chifukwa cha kuwopa mwambo, ndipo ngati ndi chifukwa cha kutsanzira kwambiri Matembenuzidwe achigiriki ndi achilatini Matembenuzidwe athu enieniwo [Chingelezi] anataya dzinalo, izi nzifukwa zopanda mphamvu ya kutsutsa kugwiritsiridwa ntchito kwake koyamba.” Perowne anakonda dzina lakuti “Yehova” chifukwa chakuti linali lodziŵika. Kuyambira pamenepo matembenuzidwe angapo amakono nawonso agwiritsira ntchito dzina la Mulungulo. New World Translation of the Holy Scriptures imagwiritsira ntchito dzinalo Yehova nthaŵi zoposa 7,200 m’Malemba Achihebri ndi Achigiriki Achikristu.

M’kutembenuza kwake Masalmo, Perowne anayesetsa kumamatira “mosamalitsa ku mpangidwe wachihebri, ponse paŵiri m’kalembedwe ka chinenerocho ndi m’maumbidwe a mawu.” Potembenuza Salmo 69, mavesi 5 ndi 6, anaona kufunika kwa kusiyanitsa mawu achihebri a “Mulungu” (ʼElo·himʹ), “Ambuye” (ʼAdho·naiʹ), ndi “Yehova”: “O Mulungu [ʼElo·himʹ], Mudziŵa bwino kupusa kwanga, ndipo liwongo langa silinabisike kwa Inu. Musalole oyembekezera pa Inu kuchita manyazi chifukwa cha ine, O Ambuye [ʼAdho·naiʹ], Yehova (Mulungu wa) makamu. Musalole iwo ofuna Inu kuvutika mtima, chifukwa cha ine, O Mulungu wa Israyeli.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena