Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 4/15 tsamba 32
  • “Ndi Zochita za Yehova”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Ndi Zochita za Yehova”
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 4/15 tsamba 32

“Ndi Zochita za Yehova”

Umenewo unali mutu wa nkhani ina mu El Norte, nyuzipepala ya ku Monterrey City, Mexico. Nkhaniyo inali yosimba za Nyumba ya Msonkhano yatsopano ya Mboni za Yehova.

Monterrey ndi mzinda wa anthu 2,300,000 (kuphatikizapo milaga) kumpoto kwa Mexico, ndipo uli ndi ofalitsa Ufumu 19,200. Kwa pafupifupi chaka ndi theka, Mboni zinayesetsa mogwirizana kumanga Nyumba ya Msonkhano yokongola ndi yoyenera yokhala ndi mipando yabwino 3,000 ndi makina oloŵetsa mphepo mkati. Mboni zakumaloko zinasangalala pamene chiŵalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova chinapereka nkhani ya kupatuliridwa kwake. Programu yake inaphatikizapo kusimbidwa kwachidule kwa mbiri ya ntchitoyo mu Monterrey, ndipo awo amene anagwira nawo ntchitoyo anafunsidwa. Ndiyeno anthu 4,500 amene anafika pamsonkhanowo anasangalala ndi nkhani ya kupatulira.

Imeneyi ndi yachitatu pa Nyumba za Misonkhano zimene zamangidwa posachedwapa ku Mexico mu mkupiti umene wafotokozedwa kukhala wa “Nyumba za Ufumu ndi Nyumba za Misonkhano Zambiri, Zazikulu, ndi Zabwino Kwambiri.”

Pokhala ndi ofalitsa oposa 443,000 ku Mexico, ndi ofika pa Chikumbutso 1,492,500 mu 1995, Nyumba za Misonkhano zatsopano, monga ya ku Monterrey, ndithudi zidzakwaniritsa chifuno cha Mulungu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena